Surah 58 · 22 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Surah Al-Mujadilah in Chichewa
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
قَدۡ سَمِعَ ٱللَّهُ قَوۡلَ ٱلَّتِي تُجَٰدِلُكَ فِي زَوۡجِهَا وَتَشۡتَكِيٓ إِلَى ٱللَّهِ وَٱللَّهُ يَسۡمَعُ تَحَاوُرَكُمَآۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٌ
Ndithudi Mulungu wamva mau a mkazi amene ali kutsutsana ndi iwe pa nkhani ya mwamuna wake ndipo iye wapereka madandaulo ake kwa Mulungu. Ndipo Mulungu wamva kukangana kwanu chifukwa Iye amamva ndiponso amaona chili chonse
ٱلَّذِينَ يُظَٰهِرُونَ مِنكُم مِّن نِّسَآئِهِم مَّا هُنَّ أُمَّهَٰتِهِمۡۖ إِنۡ أُمَّهَٰتُهُمۡ إِلَّا ٱلَّٰٓـِٔي وَلَدۡنَهُمۡۚ وَإِنَّهُمۡ لَيَقُولُونَ مُنكَرًا مِّنَ ٱلۡقَوۡلِ وَزُورًاۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَعَفُوٌّ غَفُورٌ
Iwo amene ali pakati panu ndipo amasudzula akazi awo ponena kuti: “Iwe uli ngati msana wa Amai anga.” Iwo sangakhale Amai awo ai. Palibe amene angakhale amayi awo, kupatula okhawo amene anawabara. Ndithudi iwo amalankhula mau oipa ndi bodza. Ndithudi Mulungu amakhululukira nthawi zonse
وَٱلَّذِينَ يُظَٰهِرُونَ مِن نِّسَآئِهِمۡ ثُمَّ يَعُودُونَ لِمَا قَالُواْ فَتَحۡرِيرُ رَقَبَةٍ مِّن قَبۡلِ أَن يَتَمَآسَّاۚ ذَٰلِكُمۡ تُوعَظُونَ بِهِۦۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٌ
Ndipo iwo amene amasudzula akazi ponena kuti amaoneka ngati kumbuyo kwa amayi awo kenaka afuna kuti akhululukidwe pa zomwe adanena ayenera kumasula kapolo asanabwererane. Limeneli ndi lamulo limene mwalamulidwa kuti mulimvere ndipo Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita
فَمَن لَّمۡ يَجِدۡ فَصِيَامُ شَهۡرَيۡنِ مُتَتَابِعَيۡنِ مِن قَبۡلِ أَن يَتَمَآسَّاۖ فَمَن لَّمۡ يَسۡتَطِعۡ فَإِطۡعَامُ سِتِّينَ مِسۡكِينًاۚ ذَٰلِكَ لِتُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦۚ وَتِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِۗ وَلِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابٌ أَلِيمٌ
Ndipo ngati wina sangathe kutero, ayenera kusala chakudya miyezi iwiri mosadukiza asanabwererane. Koma ngati sangathe kutero, ayenera kudyetsa anthu osauka makumi asanu ndi limodzi; ndi cholinga chakuti muonetse chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Amenewa ndiwo malamulo amene adakhazikitsidwa ndi Mulungu. Ndipo kwa anthu osakhulupilira kuli chilango chowawa
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُحَآدُّونَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ كُبِتُواْ كَمَا كُبِتَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ وَقَدۡ أَنزَلۡنَآ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٍۚ وَلِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابٌ مُّهِينٌ
Ndithudi onse amene amatsutsa Mulungu ndi Mtumwi wakeadzatsitsidwakwambirimongamomweadatsitsidwira iwo amene adalipo kale. Ndipo Ife tatumiza zizindikiro zooneka. Ndipo anthu onse osakhulupirira adzalandira chilango chochititsa manyazi
يَوۡمَ يَبۡعَثُهُمُ ٱللَّهُ جَمِيعًا فَيُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوٓاْۚ أَحۡصَىٰهُ ٱللَّهُ وَنَسُوهُۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ شَهِيدٌ
Patsiku limene Mulungu adzawaukitsa onse kwa akufa ndi kuwauza ntchito zawo zonse zimene adachita. Mulungu anasunga zimene iwo adaiwala. Ndipo Mulungu ndi mboni pazinthu zonse
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ مَا يَكُونُ مِن نَّجۡوَىٰ ثَلَٰثَةٍ إِلَّا هُوَ رَابِعُهُمۡ وَلَا خَمۡسَةٍ إِلَّا هُوَ سَادِسُهُمۡ وَلَآ أَدۡنَىٰ مِن ذَٰلِكَ وَلَآ أَكۡثَرَ إِلَّا هُوَ مَعَهُمۡ أَيۡنَ مَا كَانُواْۖ ثُمَّ يُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُواْ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٌ
Kodi iwe siudaone kuti Mulungu amadziwa zonse zimene zili mlengalenga ndi chilichonse chimene chili padziko lapansi? Palibe nkhani za chinsinsi pakati pa anthu atatu zimene Iye sakhala wachinayi, kapena pakati pa anthu asanu pamene Iye sakhala wa chisanu ndi chimodzi, kapena pakati pa anthu ochepa kapena ochuluka, koma Iye amakhala pakati pawo. Kulikonse kumene iwo angakhale pomaliza Iye adzawauza zonse zimene adachita patsiku lachiweruzo. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse
أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ نُهُواْ عَنِ ٱلنَّجۡوَىٰ ثُمَّ يَعُودُونَ لِمَا نُهُواْ عَنۡهُ وَيَتَنَٰجَوۡنَ بِٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡعُدۡوَٰنِ وَمَعۡصِيَتِ ٱلرَّسُولِۖ وَإِذَا جَآءُوكَ حَيَّوۡكَ بِمَا لَمۡ يُحَيِّكَ بِهِ ٱللَّهُ وَيَقُولُونَ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ لَوۡلَا يُعَذِّبُنَا ٱللَّهُ بِمَا نَقُولُۚ حَسۡبُهُمۡ جَهَنَّمُ يَصۡلَوۡنَهَاۖ فَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ
Kodi iwe siudawaone amene adaletsedwa kuchita misonkhano ya mseri komabe amayambanso kuchita misonkhano ya chinsinsi imene adaletsedwa kuti asamachite? Iwo amachita misonkhano pakati pawo ndi cholinga choukira ndi kusamvera Mtumwi wa Mulungu. Koma iwo akamadza kwa iwe, iwo amakulonjera iwe osati monga mmene Mulungu amakulonjerera ayi koma mwachinyengo. Ndipo iwo amati kwa wina ndi mnzake: “Kodi bwanji Mulungu satilanga pa zimene timanena?” Gahena ndi yokwana kwa iwo, ndipo adzapsa m’malawi ake. Ndipo kumeneko ndi konyansa kwambiri
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا تَنَٰجَيۡتُمۡ فَلَا تَتَنَٰجَوۡاْ بِٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡعُدۡوَٰنِ وَمَعۡصِيَتِ ٱلرَّسُولِ وَتَنَٰجَوۡاْ بِٱلۡبِرِّ وَٱلتَّقۡوَىٰۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ ٱلَّذِيٓ إِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ
oh inu anthu okhulupirira! Pamene inu muchita misonkhano yanu yamseri musalankhule zinthu zoipa, zoukira ndi zosamvera Mtumwi koma muzilankhula zinthu zachilungamo ndi zamvano. Ndipo muopeni Mulungu chifukwa ndi kumene nonse mudzabwerera
إِنَّمَا ٱلنَّجۡوَىٰ مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ لِيَحۡزُنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَلَيۡسَ بِضَآرِّهِمۡ شَيۡـًٔا إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ
Misonkhano yamseri imachokera kwa Satana amene amafuna kusokoneza anthu okhulupirira. Koma Iye sangawalakwitse ayi kupatula ndi chilolezo cha Mulungu ndipo mwa Mulungu ndi momwe anthu okhulupirira ayenera kuika chikhulupiriro chawo
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا قِيلَ لَكُمۡ تَفَسَّحُواْ فِي ٱلۡمَجَٰلِسِ فَٱفۡسَحُواْ يَفۡسَحِ ٱللَّهُ لَكُمۡۖ وَإِذَا قِيلَ ٱنشُزُواْ فَٱنشُزُواْ يَرۡفَعِ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنكُمۡ وَٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ دَرَجَٰتٍۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٌ
Oh inu anthu okhulupirira! Ngati muuzidwa kukonza malo m’misonkhano yanu, konzani malo okwanira. Ndipo Mulungu adzakukonzerani inu malo okwanira kwambiri. Ndipo mukauzidwa kuti mudzuke, dzukani. Mulungu adzakweza mu maudindo ena a inu amene mukhulupirira ndi iwo amene apatsidwa nzeru. Ndipo Mulungu amadziwa ntchito zanu zonse
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا نَٰجَيۡتُمُ ٱلرَّسُولَ فَقَدِّمُواْ بَيۡنَ يَدَيۡ نَجۡوَىٰكُمۡ صَدَقَةًۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٌ لَّكُمۡ وَأَطۡهَرُۚ فَإِن لَّمۡ تَجِدُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ
oh inu anthu okhulupirira! Ngati mufuna kukumana ndi Mtumwi mwamseri, perekani chaulere chanu musanayambe kukambirana naye. Zimenezo zidzakhala zabwino kwa inu ndiponso dongosolo. Koma ngati inu mulibe chopereka, Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisonichosatha
ءَأَشۡفَقۡتُمۡ أَن تُقَدِّمُواْ بَيۡنَ يَدَيۡ نَجۡوَىٰكُمۡ صَدَقَٰتٍۚ فَإِذۡ لَمۡ تَفۡعَلُواْ وَتَابَ ٱللَّهُ عَلَيۡكُمۡ فَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥۚ وَٱللَّهُ خَبِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ
Kodiinumulikuchitamanthakupereka chaulere chanu musanakumane naye? Ngati nditero, musachite mantha chifukwa Mulungu wakukhululukirani. Motero pitirizani kupemphera nthawi zonse, perekani msonkho wothandiza osauka, ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake. Ndithudi Mulungu amadziwa ntchito zanu zonse
أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ تَوَلَّوۡاْ قَوۡمًا غَضِبَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مَّا هُم مِّنكُمۡ وَلَا مِنۡهُمۡ وَيَحۡلِفُونَ عَلَى ٱلۡكَذِبِ وَهُمۡ يَعۡلَمُونَ
Kodi iwe suwaona amene amapalana ubwenzi ndi anthu amene adalandira mkwiyo wa Mulungu? Iwo si a m’gulu lako kapena a mgulu lawo, ndipo iwo amalumbira zabodza pamene ali kudziwa
أَعَدَّ ٱللَّهُ لَهُمۡ عَذَابًا شَدِيدًاۖ إِنَّهُمۡ سَآءَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Mulungu wawakonzera chilango chowawa. Ndithudi zoipa ndizo anali kuchita
ٱتَّخَذُوٓاْ أَيۡمَٰنَهُمۡ جُنَّةً فَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ فَلَهُمۡ عَذَابٌ مُّهِينٌ
Iwo apanga malonjezo awo kukhala chishango. Kotero iwo amatchinjiriza anthu ku njira ya Mulungu ndipo iwo adzalandira chilango chochititsa manyazi
لَّن تُغۡنِيَ عَنۡهُمۡ أَمۡوَٰلُهُمۡ وَلَآ أَوۡلَٰدُهُم مِّنَ ٱللَّهِ شَيۡـًٔاۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Chuma kapena ana awo sizidzawathandiza ku mkwiyo wa Mulungu. Iwo adzapita kumoto kumene adzakhaleko mpaka kalekale
يَوۡمَ يَبۡعَثُهُمُ ٱللَّهُ جَمِيعًا فَيَحۡلِفُونَ لَهُۥ كَمَا يَحۡلِفُونَ لَكُمۡ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُمۡ عَلَىٰ شَيۡءٍۚ أَلَآ إِنَّهُمۡ هُمُ ٱلۡكَٰذِبُونَ
Patsiku limene Mulungu adzawadzutsa onse, iwo adzalumbira pamaso pake monga momwe alumbirira kwa inu. Ndipo iwo amaganiza kuti ali ndi mtsamiro. Ndithudi iwo ndi abodza
ٱسۡتَحۡوَذَ عَلَيۡهِمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ فَأَنسَىٰهُمۡ ذِكۡرَ ٱللَّهِۚ أُوْلَٰٓئِكَ حِزۡبُ ٱلشَّيۡطَٰنِۚ أَلَآ إِنَّ حِزۡبَ ٱلشَّيۡطَٰنِ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ
Satana ndiye ali kuwalamulira. Ndipo wawachititsa iwo kuti aiwale kukumbukira Mulungu. Iwo ali m’gulu la Satana. Ndithudi gulu la Satana lidzakhala lolephera
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُحَآدُّونَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥٓ أُوْلَٰٓئِكَ فِي ٱلۡأَذَلِّينَ
Iwo amene amatsutsa Mulungu ndi Mtumwi wake adzakhala pakati pa anthu amene adzanyozedwa zedi
كَتَبَ ٱللَّهُ لَأَغۡلِبَنَّ أَنَا۠ وَرُسُلِيٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ قَوِيٌّ عَزِيزٌ
Mulungu walamulira kuti: Ndithudi! Ine pamodzi ndi Atumwi anga tidzapambana. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu zonse
لَّا تَجِدُ قَوۡمًا يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ يُوَآدُّونَ مَنۡ حَآدَّ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَلَوۡ كَانُوٓاْ ءَابَآءَهُمۡ أَوۡ أَبۡنَآءَهُمۡ أَوۡ إِخۡوَٰنَهُمۡ أَوۡ عَشِيرَتَهُمۡۚ أُوْلَٰٓئِكَ كَتَبَ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلۡإِيمَٰنَ وَأَيَّدَهُم بِرُوحٍ مِّنۡهُۖ وَيُدۡخِلُهُمۡ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ رَضِيَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ وَرَضُواْ عَنۡهُۚ أُوْلَٰٓئِكَ حِزۡبُ ٱللَّهِۚ أَلَآ إِنَّ حِزۡبَ ٱللَّهِ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ
Iwe sudzapeza anthu amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ali kuchita chibwenzi ndi iwo amene amatsutsa Mulungu ndi Mtumwi wake ngakhale kuti atakhala abambo wawo, kapena ana awo kapena abale awo kapena anansi awo. Kwa awa, Iye wakhazikitsa chikhulupiriro m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi ulangizi, wochokera kwa Iye. Ndipo Iye adzawalandira m’minda ya Paradiso, imene pansi pake pamayenda mitsinje kuti akhale komweko mpaka kalekale. Mulungu wasangalala nawo ndipo nawonso asangalala ndi Iye. Iwo ndi anthu a gulu la Mulungu. Ndithudi ndi anthu a Mulungu amene adzapambana
Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.