Surah 61 · 14 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah As-Saff in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

61:1

سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

Chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi, chimalemekeza Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru

61:2

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لِمَ تَقُولُونَ مَا لَا تَفۡعَلُونَ

oh inu okhulupirira! Kodi bwanji mumanena zinthu zimene simuchita

61:3

كَبُرَ مَقۡتًا عِندَ ٱللَّهِ أَن تَقُولُواْ مَا لَا تَفۡعَلُونَ

Ndithudi ndi chinthu chonyansa kwambiri pamaso pa Mulungu kuti muzinena chinthu chimene simuchita

61:4

إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلَّذِينَ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِهِۦ صَفًّا كَأَنَّهُم بُنۡيَٰنٌ مَّرۡصُوصٌ

Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amamenya nkhondo ndi cholinga chokhazikitsa ulamuliro wake molimba, m’magulu, ngati chipupa cha miyala

61:5

وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ لِمَ تُؤۡذُونَنِي وَقَد تَّعۡلَمُونَ أَنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُمۡۖ فَلَمَّا زَاغُوٓاْ أَزَاغَ ٱللَّهُ قُلُوبَهُمۡۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡفَٰسِقِينَ

Ndi pamene Mose adanena ndi anthu ake: “oh inu anthu anga! Kodi bwanji mukundikwiyitsa pamene muli kudziwa kuti ine ndine Mtumwi wa Mulungu kwa inuyo?” Ndipo pamene iwo adalakwa, Mulungu adalola kuti mitima yawo ilakwe. Ndipo Mulungu satsogolera anthu ophwanya malamulo

61:6

وَإِذۡ قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُم مُّصَدِّقًا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيَّ مِنَ ٱلتَّوۡرَىٰةِ وَمُبَشِّرَۢا بِرَسُولٍ يَأۡتِي مِنۢ بَعۡدِي ٱسۡمُهُۥٓ أَحۡمَدُۖ فَلَمَّا جَآءَهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٌ مُّبِينٌ

Ndi pamene Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, adati: “oh inu ana a Israyeli! Ine ndine Mtumwi wa Mulungu amene ndatumidwa kwa inu, kutsimikizira za Buku la Chipangano chakale limene lidadza ine ndisanadze, ndi kuulula nkhani yabwino ya Mtumwi Ahmad amene adzabwera ine nditachoka.” Koma pamene iye adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka, iwo adati: “Awa ndiwo matsenga enieni.”

61:7

وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ وَهُوَ يُدۡعَىٰٓ إِلَى ٱلۡإِسۡلَٰمِۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ

Kodi amalakwa kwambiri ndani kuposa As-Saff 597 iye amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ngakhale pamene ali kuitanidwa kuti alowe Chisilamu? Ndipo Mulungu satsogolera iwo amene amachita zoipa

61:8

يُرِيدُونَ لِيُطۡفِـُٔواْ نُورَ ٱللَّهِ بِأَفۡوَٰهِهِمۡ وَٱللَّهُ مُتِمُّ نُورِهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡكَٰفِرُونَ

Cholinga chawo ndikufuna kuzimitsa nyali ya Mulungu ndi milomo yawo. Koma Mulungu adzateteza nyali yake ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo

61:9

هُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ رَسُولَهُۥ بِٱلۡهُدَىٰ وَدِينِ ٱلۡحَقِّ لِيُظۡهِرَهُۥ عَلَى ٱلدِّينِ كُلِّهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُشۡرِكُونَ

Ndiye amene watumiza Mtumwi wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choonadi kuti chikhale chapamwamba pa zipembedzo zina zonse ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo

61:10

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰ تِجَٰرَةٍ تُنجِيكُم مِّنۡ عَذَابٍ أَلِيمٍ

Oh inu anthu okhulupirira! Kodi ndikulangizeni malonda apafupi amene angakuomboleni ku chilango choopsa

61:11

تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتُجَٰهِدُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ بِأَمۡوَٰلِكُمۡ وَأَنفُسِكُمۡۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٌ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

Kuti mukhulupirire mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, kuti mudzipereke kwathunthu mu njira ya Mulungu pogwiritsa ntchito chuma chanu ndi inu eni ake. Chimenechi ndicho chinthu chabwino kwa inu ngati inu mukadadziwa

61:12

يَغۡفِرۡ لَكُمۡ ذُنُوبَكُمۡ وَيُدۡخِلۡكُمۡ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ وَمَسَٰكِنَ طَيِّبَةً فِي جَنَّٰتِ عَدۡنٍۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ

Iyeadzakukhululukiraniinumachimoanu ndi kukulandirani m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje, ndipo adzakulowetsani m’nyumba zokongola ndi zaulemu za m’Paradiso. Kumeneko, ndithudi, ndiko kupambana kwenikweni

61:13

وَأُخۡرَىٰ تُحِبُّونَهَاۖ نَصۡرٌ مِّنَ ٱللَّهِ وَفَتۡحٌ قَرِيبٌۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo Iye adzakupatsani madalitso ena amene mumakonda. Chithandizo chochokera kwa Mulungu ndi kupambana mwamsanga. Kotero auze nkhani yabwino anthu okhulupirira

61:14

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُونُوٓاْ أَنصَارَ ٱللَّهِ كَمَا قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ لِلۡحَوَارِيِّـۧنَ مَنۡ أَنصَارِيٓ إِلَى ٱللَّهِۖ قَالَ ٱلۡحَوَارِيُّونَ نَحۡنُ أَنصَارُ ٱللَّهِۖ فَـَٔامَنَت طَّآئِفَةٌ مِّنۢ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَكَفَرَت طَّآئِفَةٌۖ فَأَيَّدۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ عَلَىٰ عَدُوِّهِمۡ فَأَصۡبَحُواْ ظَٰهِرِينَ

oh inu okhulupirira! Khalani otumikira Mulungu monga momwe ananenera Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, kwa ophunzira ake: “Kodi ndani andithandiza ine potumikira Mulungu?” Iwo adayankha: “Ife ndife othandiza Mulungu.” Kotero ena mwa ana a Israyeli adakhulupirira pamene ena sadakhulupirire. Motero Ife tidawapatsa mphamvu iwo amene adakhulupirira zopambana adani awo ndipo iwo adapambanadi

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.