Surah 99 · 8 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Az-Zalzalah in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

99:1

إِذَا زُلۡزِلَتِ ٱلۡأَرۡضُ زِلۡزَالَهَا

Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chivomerezi chomaliza

99:2

وَأَخۡرَجَتِ ٱلۡأَرۡضُ أَثۡقَالَهَا

Ndipo pamene nthaka idzatulutsa katundu amene ali m’kati mwake

99:3

وَقَالَ ٱلۡإِنسَٰنُ مَا لَهَا

Ndipo munthu adzafunsa: “Kodi yatani?”

99:4

يَوۡمَئِذٍ تُحَدِّثُ أَخۡبَارَهَا

Pa tsikuli nthaka idzaulula zonse

99:5

بِأَنَّ رَبَّكَ أَوۡحَىٰ لَهَا

Chifukwa Ambuye wako wayiuza kuti itero

99:6

يَوۡمَئِذٍ يَصۡدُرُ ٱلنَّاسُ أَشۡتَاتًا لِّيُرَوۡاْ أَعۡمَٰلَهُمۡ

Pa tsikuli mtundu wa anthu udzadza m’magulu osiyana siyana kudzalangizidwa ntchito zawo

99:7

فَمَن يَعۡمَلۡ مِثۡقَالَ ذَرَّةٍ خَيۡرًا يَرَهُۥ

Motero aliyense amene amachita chabwino cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona

99:8

وَمَن يَعۡمَلۡ مِثۡقَالَ ذَرَّةٍ شَرًّا يَرَهُۥ

Ndipo aliyense amene amachita choipa cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.