Surah 35 · 45 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Fatir in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

35:1

ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ فَاطِرِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ جَاعِلِ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ رُسُلًا أُوْلِيٓ أَجۡنِحَةٍ مَّثۡنَىٰ وَثُلَٰثَ وَرُبَٰعَۚ يَزِيدُ فِي ٱلۡخَلۡقِ مَا يَشَآءُۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ قَدِيرٌ

Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi, amene adalenga angelo, atumwi ouluka, amapiko awiri, atatu ndi anayi. Iye amachulukitsa zolengedwa mwachifuniro chake. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

35:2

مَّا يَفۡتَحِ ٱللَّهُ لِلنَّاسِ مِن رَّحۡمَةٍ فَلَا مُمۡسِكَ لَهَاۖ وَمَا يُمۡسِكۡ فَلَا مُرۡسِلَ لَهُۥ مِنۢ بَعۡدِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

Chimene Mulungu, mwachifundo chake, amapereka kwa anthu palibe amene angawalande, ndipo chilichonse chimene Iye awamana palibe wina amene angawapatse. Iye ndiye Mwini mphamvu ndiponso Mwini nzeru

35:3

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡۚ هَلۡ مِنۡ خَٰلِقٍ غَيۡرُ ٱللَّهِ يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَأَنَّىٰ تُؤۡفَكُونَ

Oh anthu inu! Kumbukirani zokoma zimene Mulungu adakupatsani! Kodipali Namalengawinakupatula Mulungu amene akhoza kukupatsani zokoma kuchokera kumwamba kapena padziko lapansi? Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Nanga ndi chifukwa chiyani mumanyengedwa

35:4

وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدۡ كُذِّبَتۡ رُسُلٌ مِّن قَبۡلِكَۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ

Ndipo ngati akuti iwe ndi wabodza, ndithudi, Atumwi amene adadza iwe usanabadwe nawonso adatchulidwa kuti ndi abodza ndipo ndi kwa Mulungu kokha kumene zinthu zonse zidzabwerera

35:5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقٌّۖ فَلَا تَغُرَّنَّكُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا وَلَا يَغُرَّنَّكُم بِٱللَّهِ ٱلۡغَرُورُ

Anthu inu! Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona, kotero musalole zokoma za m’moyo uno kuti zikunyengeni ndiponso musalole mdyerekezi kuti akunyengeni zokhudza Mulungu

35:6

إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ لَكُمۡ عَدُوٌّ فَٱتَّخِذُوهُ عَدُوًّاۚ إِنَّمَا يَدۡعُواْ حِزۡبَهُۥ لِيَكُونُواْ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلسَّعِيرِ

Ndithudi Satana ndi mdani wanu, kotero dziwani kuti iye ndi mdani wanu. Iye amangoitana gulu lake kuti akhoza kukakhala nalo ku moto woyaka

35:7

ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَهُمۡ عَذَابٌ شَدِيدٌۖ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُم مَّغۡفِرَةٌ وَأَجۡرٌ كَبِيرٌ

Kwa iwo amene sakhulupirira, iwo adzalandira chilango chowawa ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, iwo adzakhululukidwa ndi kulandira mphotho yaikulu

35:8

أَفَمَن زُيِّنَ لَهُۥ سُوٓءُ عَمَلِهِۦ فَرَءَاهُ حَسَنًاۖ فَإِنَّ ٱللَّهَ يُضِلُّ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُۖ فَلَا تَذۡهَبۡ نَفۡسُكَ عَلَيۡهِمۡ حَسَرَٰتٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمُۢ بِمَا يَصۡنَعُونَ

Kodi iye,amene zoipa zake zimaoneka ngati zabwino, moti akamaziona amati ndi zabwino? Ndithudi Mulungu amasocheretsa aliyense amene amamufuna ndiponso amatsogolera aliyense amene wamufuna. Kotero usavutike mu mtima mwako chifukwa cha iwo. Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene amachita

35:9

وَٱللَّهُ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ ٱلرِّيَٰحَ فَتُثِيرُ سَحَابًا فَسُقۡنَٰهُ إِلَىٰ بَلَدٍ مَّيِّتٍ فَأَحۡيَيۡنَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَاۚ كَذَٰلِكَ ٱلنُّشُورُ

Ndipo Mulungu ndiye amene amatumiza mphepo imene imayendetsa mtambo, ndipo timauyendetsa kudziko lakufa ndipo ndi iwo timapereka moyo ku nthaka ikafa. Kumeneko ndiko kuuka kwa akufa

35:10

مَن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡعِزَّةَ فَلِلَّهِ ٱلۡعِزَّةُ جَمِيعًاۚ إِلَيۡهِ يَصۡعَدُ ٱلۡكَلِمُ ٱلطَّيِّبُ وَٱلۡعَمَلُ ٱلصَّٰلِحُ يَرۡفَعُهُۥۚ وَٱلَّذِينَ يَمۡكُرُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِ لَهُمۡ عَذَابٌ شَدِيدٌۖ وَمَكۡرُ أُوْلَٰٓئِكَ هُوَ يَبُورُ

Aliyense amene afuna ulemu ndi mphamvu ndi kwa Mulungu kumene kuli ulemu ndi mphamvu. Kwa Iye ndiko kumene kumapita mawu abwino ndipo ntchito zabwino amazinyamula. Akakhala iwo amene amakonza ntchito zoipa, iwo adzalandira chilango chowawa ndipo chikonzero chawo chidzafafanizidwa

35:11

وَٱللَّهُ خَلَقَكُم مِّن تُرَابٍ ثُمَّ مِن نُّطۡفَةٍ ثُمَّ جَعَلَكُمۡ أَزۡوَٰجًاۚ وَمَا تَحۡمِلُ مِنۡ أُنثَىٰ وَلَا تَضَعُ إِلَّا بِعِلۡمِهِۦۚ وَمَا يُعَمَّرُ مِن مُّعَمَّرٍ وَلَا يُنقَصُ مِنۡ عُمُرِهِۦٓ إِلَّا فِي كِتَٰبٍۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٌ

Ndipo Mulungu adakulengani inu kuchokera ku dothi, kenaka adakulengani kuchokera ku dontho la umuna ndipo adakupangani inu awiriawiri ndipo palibe mkazi amene amaima kapena kubala kupatula ndi chilolezo chake. Ndipo palibe aliyense amene moyo wake umapitirizidwa kapena kuchepetsedwa kupatula zimene zidalembedwa m’Buku Lopatulika. Ndithudi zimenezi ndi za pafupi ndi Mulungu

35:12

وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡبَحۡرَانِ هَٰذَا عَذۡبٌ فُرَاتٌ سَآئِغٌ شَرَابُهُۥ وَهَٰذَا مِلۡحٌ أُجَاجٌۖ وَمِن كُلٍّ تَأۡكُلُونَ لَحۡمًا طَرِيًّا وَتَسۡتَخۡرِجُونَ حِلۡيَةً تَلۡبَسُونَهَاۖ وَتَرَى ٱلۡفُلۡكَ فِيهِ مَوَاخِرَ لِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Ndiponyanjaziwirisizingakhalezofananakwenikweni. Ina ndi ya madzi ozuna amene amatha ludzu chifukwa cha kukoma kwake, okoma kumwa; ndipo ina ndi yamchere, imene imatentha chifukwa cha mchere. Komabe kuchokera mu zonse inu mumadya zakudya zabwino ndipo mumatulutsamo zinthu zosangalatsa zimene mumavala. Ndipo inu mumaona zombo zilikuyenda m’mafunde kuti inu muthe kufunafuna zokoma za Mulungu ndiponso kuti muzithokoza

35:13

يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلٌّ يَجۡرِي لِأَجَلٍ مُّسَمًّىۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ لَهُ ٱلۡمُلۡكُۚ وَٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ مَا يَمۡلِكُونَ مِن قِطۡمِيرٍ

Iye amasanduliza usiku kuti ukhale usana ndipo amasanduliza usana kuti ukhale usiku ndipo Iye adalamula dzuwa ndi mwezi kumvera malamulo ake. Iye adalamula chilichonse kuti chiziyenda m’njira yake mpaka pa tsiku lokhazikitsidwa. Iye ndi Mulungu,Ambuye wanu; wake ndi Ufumu ndipo iwo amene mumapembedza poonjezera pa Mulungu salamulira chinthu ngakhale chaching’ono

35:14

إِن تَدۡعُوهُمۡ لَا يَسۡمَعُواْ دُعَآءَكُمۡ وَلَوۡ سَمِعُواْ مَا ٱسۡتَجَابُواْ لَكُمۡۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَكۡفُرُونَ بِشِرۡكِكُمۡۚ وَلَا يُنَبِّئُكَ مِثۡلُ خَبِيرٍ

Ngati inu muwapempha iwo sadzamva kupempha kwanu ndipo ngati iwo akadamva iwo sangathe kuyankha mapemphero anu. Ndipo pa tsiku lachiweruzo iwo adzakukanani inu. Ndipo palibe wina amene angakuuzeni inu kuposa Iye amene amadziwa chilichonse

35:15

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ أَنتُمُ ٱلۡفُقَرَآءُ إِلَى ٱللَّهِۖ وَٱللَّهُ هُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ

Anthu inu! Ndinu amene mumafuna Mulungu ndipo Mulungu ndiye amene ali woima payekha ndi woyamikiridwa

35:16

إِن يَشَأۡ يُذۡهِبۡكُمۡ وَيَأۡتِ بِخَلۡقٍ جَدِيدٍ

Ngati Iye atafuna akhoza kukuchotsani ndi kubweretsa m’badwo wina watsopano

35:17

وَمَا ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ بِعَزِيزٍ

Ndipo kutero si kovuta kwa Mulungu

35:18

وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۚ وَإِن تَدۡعُ مُثۡقَلَةٌ إِلَىٰ حِمۡلِهَا لَا يُحۡمَلۡ مِنۡهُ شَيۡءٌ وَلَوۡ كَانَ ذَا قُرۡبَىٰٓۗ إِنَّمَا تُنذِرُ ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُم بِٱلۡغَيۡبِ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَۚ وَمَن تَزَكَّىٰ فَإِنَّمَا يَتَزَكَّىٰ لِنَفۡسِهِۦۚ وَإِلَى ٱللَّهِ ٱلۡمَصِيرُ

Ndipo mzimu wolemedwa sungathe kunyamula katundu wa mzimu wina wolemedwa ndipo ngati mzimu wina wolemedwa utalilira mzimu wina wolemedwa kuti uunyamulire katundu wake, winawo siungathe kunyamula katunduyo ngakhale kuti mizimuyo itakhala pa chibale. Achenjeze okhawo amene amaopa Ambuye wawo mwamseri ndipo amakwaniritsa mapemphero, ndipo aliyense amene adziyeretsa, amatero populumutsa mzimu wake. Ndi kwa Mulungu kokha kumene onse adzabwerera

35:19

وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُ

Ndipo anthu akhungu ndi openya safanana

35:20

وَلَا ٱلظُّلُمَٰتُ وَلَا ٱلنُّورُ

Ngakhalenso usiku ndi usana sizifanana

35:21

وَلَا ٱلظِّلُّ وَلَا ٱلۡحَرُورُ

Ngakhalenso mthunzi wozizira kwambiri ndi kutentha kwa dzuwa sizingafanane

35:22

وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡأَحۡيَآءُ وَلَا ٱلۡأَمۡوَٰتُۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُسۡمِعُ مَن يَشَآءُۖ وَمَآ أَنتَ بِمُسۡمِعٍ مَّن فِي ٱلۡقُبُورِ

Ndipo zamoyo ndi zakufa sizifanana. Ndithudi Mulungu akhoza kumupanga aliyense amene wamufuna kuti amve koma iwe siungathe kuwauza iwo amene ali m’manda kuti amve

35:23

إِنۡ أَنتَ إِلَّا نَذِيرٌ

Iwe ndiwe wochenjeza kwambiri

35:24

إِنَّآ أَرۡسَلۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ بَشِيرًا وَنَذِيرًاۚ وَإِن مِّنۡ أُمَّةٍ إِلَّا خَلَا فِيهَا نَذِيرٌ

Ndithudi Ife takutumiza iwe ndi choonadi ngati wotenga nkhani zabwino ndi mchenjezi ndipo palibe mtundu wa anthu umene sadakhale ndi mchenjezi pakati pawo kalelo

35:25

وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدۡ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ وَبِٱلزُّبُرِ وَبِٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُنِيرِ

Ndipo ngati iwo akuti iwe ndiwe wabodza, nawonso amene adalipo kale, adawatcha Atumwi awo kuti ndi abodza. Atumwi awo adadza kwa iwo ndi chiphunzitso chomveka ndi mawu opatulika ndi Buku la muuni

35:26

ثُمَّ أَخَذۡتُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۖ فَكَيۡفَ كَانَ نَكِيرِ

Kotero ndidawalanga anthu onse amene sadakhulupirire. Kodi chilango changa chidali chotani

35:27

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦ ثَمَرَٰتٍ مُّخۡتَلِفًا أَلۡوَٰنُهَاۚ وَمِنَ ٱلۡجِبَالِ جُدَدُۢ بِيضٌ وَحُمۡرٌ مُّخۡتَلِفٌ أَلۡوَٰنُهَا وَغَرَابِيبُ سُودٌ

Kodi inu simuona mmene Mulungu amagwetsera mvula kuchokera ku mitambo? Ndi mvulayo Ife timameretsa mbewu za maonekedwe osiyanasiyana. Ndipo m’mapiri muli njira zoyera ndi zofiira, zooneka m’maonekedwe osiyanasiyana ndi zina zakuda

35:28

وَمِنَ ٱلنَّاسِ وَٱلدَّوَآبِّ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ مُخۡتَلِفٌ أَلۡوَٰنُهُۥ كَذَٰلِكَۗ إِنَّمَا يَخۡشَى ٱللَّهَ مِنۡ عِبَادِهِ ٱلۡعُلَمَٰٓؤُاْۗ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ غَفُورٌ

Pali kusiyana m’maonekedwe pakati pa anthu, zolengedwa ndi zinyama. Iwo amene amaopa Mulungu pakati pa akapolo ake ndiwo amene ali ndi nzeru chifukwa Mulungu ndi wamphamvu zambiri ndi wokhululukira nthawi zonse

35:29

إِنَّ ٱلَّذِينَ يَتۡلُونَ كِتَٰبَ ٱللَّهِ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَنفَقُواْ مِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ سِرًّا وَعَلَانِيَةً يَرۡجُونَ تِجَٰرَةً لَّن تَبُورَ

Iwo amene amawerenga Buku la Mulungu, amene amapitiriza kupemphera nthawi zonse ndipo amapereka chaulere pa katundu amene tawapatsa mwamseri kapena poyera, ayenera kukhulupirira m’malonda amene sadzatha ayi

35:30

لِيُوَفِّيَهُمۡ أُجُورَهُمۡ وَيَزِيدَهُم مِّن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ غَفُورٌ شَكُورٌ

Kuti Iye akhoza kuwalipira mphotho zawo zonse ndi kuwapatsa zambiri kudzera m’chisomo chake. Ndithudi Iye ndi wokhululukira amene amachulukitsa malipiro

35:31

وَٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ مِنَ ٱلۡكِتَٰبِ هُوَ ٱلۡحَقُّ مُصَدِّقًا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيۡهِۗ إِنَّ ٱللَّهَ بِعِبَادِهِۦ لَخَبِيرُۢ بَصِيرٌ

Ndipo chimene tavumbulutsa kwa iwe kuchokera m’Buku ndi choonadi chimene chitsimikiza zimene zidalipo kale. Ndithudi Mulungu amadziwa ndipo amaona zochita za akapolo ake

35:32

ثُمَّ أَوۡرَثۡنَا ٱلۡكِتَٰبَ ٱلَّذِينَ ٱصۡطَفَيۡنَا مِنۡ عِبَادِنَاۖ فَمِنۡهُمۡ ظَالِمٌ لِّنَفۡسِهِۦ وَمِنۡهُم مُّقۡتَصِدٌ وَمِنۡهُمۡ سَابِقُۢ بِٱلۡخَيۡرَٰتِ بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَضۡلُ ٱلۡكَبِيرُ

Ndipo tidapereka Buku kuti lisungidwe ndi anthu amene adali pakati pa akapolo athu. Ndipo pakati pawo pali munthu amene amataya mzimu wake ndipo pakati pawo pali iye amene amaima pakati ndi pakati ndiponso pakati pawo pali iye amene amakhala patsogolo pochita ntchito zabwino ndi chilolezo cha Mulungu. Umenewu ndiwo ubwino wopambana

35:33

جَنَّٰتُ عَدۡنٍ يَدۡخُلُونَهَا يُحَلَّوۡنَ فِيهَا مِنۡ أَسَاوِرَ مِن ذَهَبٍ وَلُؤۡلُؤًاۖ وَلِبَاسُهُمۡ فِيهَا حَرِيرٌ

Iwo adzalowa m’minda yokhalitsa ndipo azidzavala zibangiri zagolide ndi nkhombe ndipo zovala zawo zidzakhala za silika

35:34

وَقَالُواْ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِيٓ أَذۡهَبَ عَنَّا ٱلۡحَزَنَۖ إِنَّ رَبَّنَا لَغَفُورٌ شَكُورٌ

Ndipoiwoadzati,“Kuyamikidwakonsendikwa Mulungu amene wachotsa chisoni pakati pathu. Ndithudi Ambuye wathu ndi wokhululukira ndiponso amene amachulukitsa malipiro.”

35:35

ٱلَّذِيٓ أَحَلَّنَا دَارَ ٱلۡمُقَامَةِ مِن فَضۡلِهِۦ لَا يَمَسُّنَا فِيهَا نَصَبٌ وَلَا يَمَسُّنَا فِيهَا لُغُوبٌ

“Amene watikhazika m’nyumba yokhalamo mpaka kalekale mwachisomo chake. Palibe mavuto amene adzatipeza kuno ndiponso sitidzakhala otopa.”

35:36

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَهُمۡ نَارُ جَهَنَّمَ لَا يُقۡضَىٰ عَلَيۡهِمۡ فَيَمُوتُواْ وَلَا يُخَفَّفُ عَنۡهُم مِّنۡ عَذَابِهَاۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي كُلَّ كَفُورٍ

Akakhala iwo amene sakhulupirira, iwo adzakhala kumoto wa ku Gahena. Iwo siudzawamaliza kuti afe ayi, ndipo chilango chawo sichidzachepetsedwa. Kotero ndi mmene timalipirira aliyense wosayamika

35:37

وَهُمۡ يَصۡطَرِخُونَ فِيهَا رَبَّنَآ أَخۡرِجۡنَا نَعۡمَلۡ صَٰلِحًا غَيۡرَ ٱلَّذِي كُنَّا نَعۡمَلُۚ أَوَلَمۡ نُعَمِّرۡكُم مَّا يَتَذَكَّرُ فِيهِ مَن تَذَكَّرَ وَجَآءَكُمُ ٱلنَّذِيرُۖ فَذُوقُواْ فَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِن نَّصِيرٍ

Ndipo iwo adzalira pofuna chipulumutso nati, “Ambuye wathu! Tichotseni kuno. Ife tikachita zinthu zabwino kusiyana ndi zimene tinali kuchita”. “Kodi Ife sitidakusungeni ndi moyo nthawi yaitali kuti iye amene amalabadira akadazindikira za zimenezi? Ndipo kwa inu kudadza mchenjezi kotero lawani chilango chifukwa munthu wochimwa alibe woti angamuthandize”

35:38

إِنَّ ٱللَّهَ عَٰلِمُ غَيۡبِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ

Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zobisika zakumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndithudi Iye amaona zimene zili m’mitima mwa anthu

35:39

هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَكُمۡ خَلَٰٓئِفَ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ فَمَن كَفَرَ فَعَلَيۡهِ كُفۡرُهُۥۖ وَلَا يَزِيدُ ٱلۡكَٰفِرِينَ كُفۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ إِلَّا مَقۡتًاۖ وَلَا يَزِيدُ ٱلۡكَٰفِرِينَ كُفۡرُهُمۡ إِلَّا خَسَارًا

Ndiye amene adakusankhani kukhala oweruza pa dziko. Kotero aliyense amene sakhulupirira, kusakhulupirira kwake kudzamupweteka yekha. Ndipo kusakhulupirira kwawo sikuonjezera china chilichonse kwa Ambuye wawo kupatula chidani chokha. Ndipo kusakhulupirira kwawo sikuonjezera china chilichonse kwa iwo kupatula kutayika

35:40

قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ شُرَكَآءَكُمُ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَرُونِي مَاذَا خَلَقُواْ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ لَهُمۡ شِرۡكٌ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ أَمۡ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ كِتَٰبًا فَهُمۡ عَلَىٰ بَيِّنَتٍ مِّنۡهُۚ بَلۡ إِن يَعِدُ ٱلظَّٰلِمُونَ بَعۡضُهُم بَعۡضًا إِلَّا غُرُورًا

Nena, “Kodi mudayamba mwaganiza za mafano anu amene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu? Tandilangizani gawo limodzi la dziko limene mafanowo adalenga? Kodi kapena iwo ali ndi gawo kumwamba? Kodi kapena Ife tidawapatsa Buku Lopatulika limene iwo amatsatira chiphunzitso chake? Iyayi! Anthu ochimwa sakwaniritsa malonjezo pakati pawo koma kunyengana basi.”

35:41

إِنَّ ٱللَّهَ يُمۡسِكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ أَن تَزُولَاۚ وَلَئِن زَالَتَآ إِنۡ أَمۡسَكَهُمَا مِنۡ أَحَدٍ مِّنۢ بَعۡدِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ حَلِيمًا غَفُورًا

Ndithudi ndi Mulungu amene amayang’anira kumwamba ndi dziko lapansi kuti zingaonongeke ndipo izo zitaonongeka palibe wina amene akhoza kuzikonzanso kupatula Iye yekha. Ndithudi Iye ndi wopirira ndi wokhululukira

35:42

وَأَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ لَئِن جَآءَهُمۡ نَذِيرٌ لَّيَكُونُنَّ أَهۡدَىٰ مِنۡ إِحۡدَى ٱلۡأُمَمِۖ فَلَمَّا جَآءَهُمۡ نَذِيرٌ مَّا زَادَهُمۡ إِلَّا نُفُورًا

Ndipo iwo adalumbira motchula Mulungu ndi molimbika kuti ngati kungadze kwa iwo Mtumwi iwo adzalandira ulangizi wake kuposa mtundu wina uliwonse. Koma pamene Mtumwi adadza kwa iwo, kubwera kwake kudaonjezera kuipa kwawo

35:43

ٱسۡتِكۡبَارًا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَكۡرَ ٱلسَّيِّيِٕۚ وَلَا يَحِيقُ ٱلۡمَكۡرُ ٱلسَّيِّئُ إِلَّا بِأَهۡلِهِۦۚ فَهَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا سُنَّتَ ٱلۡأَوَّلِينَۚ فَلَن تَجِدَ لِسُنَّتِ ٱللَّهِ تَبۡدِيلًاۖ وَلَن تَجِدَ لِسُنَّتِ ٱللَّهِ تَحۡوِيلًا

Chifukwa cha mwano ndi chiwembu chimene anali kukonza ndi chifukwa chakukonza chiwembucho, choipa chidagwa pa onse amene adakonza chiwembucho. Kodi iwo ayembekeza kusamalidwa mosiyana ndi anthu akale? Ndipo inu simudzapeza chosintha m’machitidwe a Mulungu

35:44

أَوَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ وَكَانُوٓاْ أَشَدَّ مِنۡهُمۡ قُوَّةًۚ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيُعۡجِزَهُۥ مِن شَيۡءٍ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَلَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَلِيمًا قَدِيرًا

Kodi iwo sadayende padziko lapansi ndi kuona zimene zidawachitikira anthu amene adalipo kale pamene mitundu ya anthuwo idali yamphamvu kuposa iwo? Kulibe chinthu kumwamba kapena padziko lapansi chimene chingakhumudwitse Mulungu chifukwa Iye amadziwa chilichonse ndipo ndi mwini mphamvu zonse

35:45

وَلَوۡ يُؤَاخِذُ ٱللَّهُ ٱلنَّاسَ بِمَا كَسَبُواْ مَا تَرَكَ عَلَىٰ ظَهۡرِهَا مِن دَآبَّةٍ وَلَٰكِن يُؤَخِّرُهُمۡ إِلَىٰٓ أَجَلٍ مُّسَمًّىۖ فَإِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِعِبَادِهِۦ بَصِيرَۢا

Ndipo Mulungu akamalanga anthu chifukwa cha zoipa zimene amachita, sipakadakhala cholengedwa chimene chikadakhala ndi moyo padziko lapansi. Koma Iye amazisunga mpaka pa nthawi ya malire awo. Ndipo pamene nthawi yawo ikwana, ndithudi, Mulungu amaona akapolo ake onse

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.