Surah 14 · 52 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Ibrahim in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

14:1

الٓرۚ كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ إِلَيۡكَ لِتُخۡرِجَ ٱلنَّاسَ مِنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِ بِإِذۡنِ رَبِّهِمۡ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَمِيدِ

Alif Lam Ra. Tavumbulutsa Buku lino kwa iwe kuti uwatulutse anthu kuchoka kumdima ndi kupita kowala, kunjira ya Mwini Mphamvu, ndi Mwini kuyamikidwa mwachifuniro cha Ambuye wawo

14:2

ٱللَّهِ ٱلَّذِي لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَوَيۡلٌ لِّلۡكَٰفِرِينَ مِنۡ عَذَابٍ شَدِيدٍ

Mulungu ndiye Mwini wa zonse zimene zili kumwamba ndi dziko lapansi. Tsoka kwa anthu osakhulupirira chifukwa cha chilango chowawa

14:3

ٱلَّذِينَ يَسۡتَحِبُّونَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا عَلَى ٱلۡأٓخِرَةِ وَيَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَيَبۡغُونَهَا عِوَجًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ فِي ضَلَٰلِۭ بَعِيدٍ

Iwo ameneamakondamoyounokuposamoyoumeneulinkudza ndipo amaletsa kutsatira njira ya Mulungu ndipo amafuna za chinyengo mu izo, iwo ndi wosochera kwambiri

14:4

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن رَّسُولٍ إِلَّا بِلِسَانِ قَوۡمِهِۦ لِيُبَيِّنَ لَهُمۡۖ فَيُضِلُّ ٱللَّهُ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

NdipoIfesitinatumizeMtumwikupatulam’chilankhulo cha anthu ake ndi cholinga chakuti akhoza kuwafotokozera momveka. Ndipo Mulungu amasocheretsa aliyense amene Iye wamufuna ndi kutsogolera amene wamufuna. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndiponso Mwini luntha

14:5

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ أَنۡ أَخۡرِجۡ قَوۡمَكَ مِنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِ وَذَكِّرۡهُم بِأَيَّىٰمِ ٱللَّهِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّكُلِّ صَبَّارٍ شَكُورٍ

Ndithudi Ife tidamutuma Mose ndi zizindikiro zathu ndi kunena kuti, “Atulutse anthu ako kuchoka ku mdima ndi kupita nawo kowala ndipo uwakumbutse za masiku a Mulungu.” Ndithudi mu izi muli zizindikiro kwa aliyense wopirira ndi wothokoza

14:6

وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ إِذۡ أَنجَىٰكُم مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ يَسُومُونَكُمۡ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ وَيُذَبِّحُونَ أَبۡنَآءَكُمۡ وَيَسۡتَحۡيُونَ نِسَآءَكُمۡۚ وَفِي ذَٰلِكُم بَلَآءٌ مِّن رَّبِّكُمۡ عَظِيمٌ

Ndipo pamene Mose adawauza anthu ake kuti, “Kumbukirani ubwino wa Mulungu kwa inu pamene Iye adakupulumutsani inu kwa anthu a Farawo, amene adakupatsani inu mavuto aakulu ndipo anali kupha ana anu aamuna ndi kusiya ana anu aakazi amoyo, ndithudi, zimenezi zidali mayesero aakulu kuchokera kwa Ambuye wanu.”

14:7

وَإِذۡ تَأَذَّنَ رَبُّكُمۡ لَئِن شَكَرۡتُمۡ لَأَزِيدَنَّكُمۡۖ وَلَئِن كَفَرۡتُمۡ إِنَّ عَذَابِي لَشَدِيدٌ

Ndipo pamenepo Ambuye wanu adalengeza kuti, “Ngati inu muthokoza, Ine ndidzakupatsani zinthu zambiri koma ngati simuthokoza, ndithudi, chilango changa ndi chokhwima kwambiri.”

14:8

وَقَالَ مُوسَىٰٓ إِن تَكۡفُرُوٓاْ أَنتُمۡ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعًا فَإِنَّ ٱللَّهَ لَغَنِيٌّ حَمِيدٌ

Ndipo Mose adati “Ngati inu simukhulupirira, inu ndi wonse amene ali padziko lapansi, ndithudi, Mulungu ndi wolemera ndipo ndi Mwini kuyamikidwa.”

14:9

أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ نَبَؤُاْ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكُمۡ قَوۡمِ نُوحٍ وَعَادٍ وَثَمُودَ وَٱلَّذِينَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ لَا يَعۡلَمُهُمۡ إِلَّا ٱللَّهُۚ جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَرَدُّوٓاْ أَيۡدِيَهُمۡ فِيٓ أَفۡوَٰهِهِمۡ وَقَالُوٓاْ إِنَّا كَفَرۡنَا بِمَآ أُرۡسِلۡتُم بِهِۦ وَإِنَّا لَفِي شَكٍّ مِّمَّا تَدۡعُونَنَآ إِلَيۡهِ مُرِيبٍ

Kodi inu simunamve nkhani za anthu a Nowa, Aad, ndi Thamoud omwe adalipo inu musanadze? Ndiponso za iwo amene adadza pambuyo pawo? Palibe adziwa za iwo kupatula Mulungu yekha. Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka koma iwo adatseka pakamwa pawo ndi manja awo ndipo adati, “Ndithudi ife sitikhulupirira mu zimene mwatumidwa, ndithudi ife tili ndi chikaiko pazimene mukutiitanira.”

14:10

قَالَتۡ رُسُلُهُمۡ أَفِي ٱللَّهِ شَكٌّ فَاطِرِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ يَدۡعُوكُمۡ لِيَغۡفِرَ لَكُم مِّن ذُنُوبِكُمۡ وَيُؤَخِّرَكُمۡ إِلَىٰٓ أَجَلٍ مُّسَمًّىۚ قَالُوٓاْ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُنَا تُرِيدُونَ أَن تَصُدُّونَا عَمَّا كَانَ يَعۡبُدُ ءَابَآؤُنَا فَأۡتُونَا بِسُلۡطَٰنٍ مُّبِينٍ

Atumwi awo adati, “Chiyani! Kodi pangakhale chikayiko pa Mulungu, Namalenga wa kumwamba ndi dziko lapansi? Iye akukuitanani kuti akukhululukireni machimo anu ndi kukusungani mpaka pa nthawi yomwe idaikidwa.” Iwo adati, “Inu simuli ena, koma anthu ngati ife. Inu mufuna kutiletsa zimene makolo athu anali kupembedza. Tipatseni umboni weniweni wooneka.”

14:11

قَالَتۡ لَهُمۡ رُسُلُهُمۡ إِن نَّحۡنُ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُكُمۡ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يَمُنُّ عَلَىٰ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۖ وَمَا كَانَ لَنَآ أَن نَّأۡتِيَكُم بِسُلۡطَٰنٍ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ

Atumwi awo adati kwa iwo, “Ife tili anthu ngati inu nomwe koma Mulungu amakhazikitsa chisomo chake pa ena mwa akapolo ake amene Iye wawasankha. Ife sitingathe kukupatsani chizindikiro pokhapokha ngati Mulungu afuna. Mwa Mulungu yekha onse okhulupirira aike chikhulupiriro chawo.”

14:12

وَمَا لَنَآ أَلَّا نَتَوَكَّلَ عَلَى ٱللَّهِ وَقَدۡ هَدَىٰنَا سُبُلَنَاۚ وَلَنَصۡبِرَنَّ عَلَىٰ مَآ ءَاذَيۡتُمُونَاۚ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُتَوَكِّلُونَ

“Kodi ife tingalekerenji kuika chikhulupiriro chathu mwa Mulungu pamene Iye watitsogolera kunjira zathu? Ndithudi ife tidzapirira ku mazunzo amene mungatipatse ife ndipo mwa Mulungu, onse amene amakhulupirira aike chikhulupiriro chawo.”

14:13

وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِرُسُلِهِمۡ لَنُخۡرِجَنَّكُم مِّنۡ أَرۡضِنَآ أَوۡ لَتَعُودُنَّ فِي مِلَّتِنَاۖ فَأَوۡحَىٰٓ إِلَيۡهِمۡ رَبُّهُمۡ لَنُهۡلِكَنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo anthu osakhulupirira adati kwa Atumwi awo, “Ndithudi ife tidzakuthamangitsani m’dziko lathu kapena mubwerere kuchipembedzo chathu.” Koma Ambuye wawo adawalangiza iwo nati, “Ndithudi tidzaononga anthu ochita zoipa.”

14:14

وَلَنُسۡكِنَنَّكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡۚ ذَٰلِكَ لِمَنۡ خَافَ مَقَامِي وَخَافَ وَعِيدِ

“Ndipo, ndithudi, tidzakukhazikitsani m’dziko pambuyo pa iwo. Chimenechi ndi cha iye amene aopa kudzaima pamaso panga ndipo amaopa chenjezo langa.”

14:15

وَٱسۡتَفۡتَحُواْ وَخَابَ كُلُّ جَبَّارٍ عَنِيدٍ

Ndipo iwo adafunafuna kupambana ndi chithandizo ndipo aliyense wamwano, wamtudzu ndi wolamula mwankhanza, adatayika ndi kuonongeka

14:16

مِّن وَرَآئِهِۦ جَهَنَّمُ وَيُسۡقَىٰ مِن مَّآءٍ صَدِيدٍ

Kutsogolo kwake kuli Gahena ndipo adzamwetsedwa madzi owira ndi othukusira

14:17

يَتَجَرَّعُهُۥ وَلَا يَكَادُ يُسِيغُهُۥ وَيَأۡتِيهِ ٱلۡمَوۡتُ مِن كُلِّ مَكَانٍ وَمَا هُوَ بِمَيِّتٍۖ وَمِن وَرَآئِهِۦ عَذَابٌ غَلِيظٌ

Iye, mwa unyizi, adzangopsontha koma sadzamwa ngakhale ndi pang’ono pomwe, ndipo imfa idzadza kuchokera kumbali zonse koma iye sadzafa ayi ndipo chilango chowawa chidzakhala kutsogolo kwake

14:18

مَّثَلُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِرَبِّهِمۡۖ أَعۡمَٰلُهُمۡ كَرَمَادٍ ٱشۡتَدَّتۡ بِهِ ٱلرِّيحُ فِي يَوۡمٍ عَاصِفٍۖ لَّا يَقۡدِرُونَ مِمَّا كَسَبُواْ عَلَىٰ شَيۡءٍۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلضَّلَٰلُ ٱلۡبَعِيدُ

Fanizo la iwo amene sakhulupirira mwa Ambuye wawo ndi lakuti ntchito zawo zili ngati phulusa limene liulutsidwa ndi mphepo pa tsiku la mphepo ya mkuntho. Iwo sadzapeza china chilichonse kuchokera ku zinthu zimene ankachita. Ndipo kumeneku ndiko kusochera kwenikweni

14:19

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۚ إِن يَشَأۡ يُذۡهِبۡكُمۡ وَيَأۡتِ بِخَلۡقٍ جَدِيدٍ

Kodi iwe siuona kuti Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi? Atafuna Iye akhoza kukuchotsani ndi kubweretsa zolengedwa zatsopano

14:20

وَمَا ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ بِعَزِيزٍ

Kwa Mulungu zoterezo si zovuta ayi

14:21

وَبَرَزُواْ لِلَّهِ جَمِيعًا فَقَالَ ٱلضُّعَفَٰٓؤُاْ لِلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُوٓاْ إِنَّا كُنَّا لَكُمۡ تَبَعًا فَهَلۡ أَنتُم مُّغۡنُونَ عَنَّا مِنۡ عَذَابِ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٍۚ قَالُواْ لَوۡ هَدَىٰنَا ٱللَّهُ لَهَدَيۡنَٰكُمۡۖ سَوَآءٌ عَلَيۡنَآ أَجَزِعۡنَآ أَمۡ صَبَرۡنَا مَا لَنَا مِن مَّحِيصٍ

Ndipo onse adzaonekera pa maso pa Mulungu. Ndipo anthu ochepa mphamvu adzanena kwa iwo amene anali a mwano kuti, “Ndithudi ife tinali kutsatira inu. Kodi inu mungatiteteze ife ku chilango cha Mulungu?” Iwo adzati, “Mulungu akadatitsogolera ife tikadakutsogolerani inu. Ndi chimodzimodzi kwa ife kaya tikalipa kapena tipirira, tilibe kothawira.”

14:22

وَقَالَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لَمَّا قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ إِنَّ ٱللَّهَ وَعَدَكُمۡ وَعۡدَ ٱلۡحَقِّ وَوَعَدتُّكُمۡ فَأَخۡلَفۡتُكُمۡۖ وَمَا كَانَ لِيَ عَلَيۡكُم مِّن سُلۡطَٰنٍ إِلَّآ أَن دَعَوۡتُكُمۡ فَٱسۡتَجَبۡتُمۡ لِيۖ فَلَا تَلُومُونِي وَلُومُوٓاْ أَنفُسَكُمۖ مَّآ أَنَا۠ بِمُصۡرِخِكُمۡ وَمَآ أَنتُم بِمُصۡرِخِيَّ إِنِّي كَفَرۡتُ بِمَآ أَشۡرَكۡتُمُونِ مِن قَبۡلُۗ إِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٌ

Ndipo Satana adzanena, pamene chiweruzo chaperekedwa, kuti: “Ndithudi Mulungu adakulonjezani lonjezo loona. Inenso ndidakulonjezani koma ndidakusocheretsani. Ine ndidalibe udindo pa inu, kupatula kuti ndidangokuitanani ndipo inu mudandiyankha. Tsopano musandidzudzule ine ayi koma dzidzudzuleni nokha. Ine sindingathe kukuthandizani ndipo inu simungandithandize ine. Ndithudi ine ndakana kundisakaniza kwanu ndi Mulungu kumene munali kuchita.” Zoonadi ochita zoipa adzalangidwa zedi

14:23

وَأُدۡخِلَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا بِإِذۡنِ رَبِّهِمۡۖ تَحِيَّتُهُمۡ فِيهَا سَلَٰمٌ

Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzalowetsedwa ku minda yothiriridwa ndi madzi yam’mitsinje ndipo adzakhala komweko mpaka kalekale ndi chilolezo cha Ambuye wawo. Kulonjerana kwawo kudzakhala “Mtendere”

14:24

أَلَمۡ تَرَ كَيۡفَ ضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلًا كَلِمَةً طَيِّبَةً كَشَجَرَةٍ طَيِّبَةٍ أَصۡلُهَا ثَابِتٌ وَفَرۡعُهَا فِي ٱلسَّمَآءِ

Kodi simuona mmene Mulungu amaperekera chitsanzo? Liwu labwino lili ngati mtengo wabwino umene mizu yake ndi yokhazikika ndi nthambi zake zifika mlengalenga

14:25

تُؤۡتِيٓ أُكُلَهَا كُلَّ حِينِۭ بِإِذۡنِ رَبِّهَاۗ وَيَضۡرِبُ ٱللَّهُ ٱلۡأَمۡثَالَ لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ

Umene umabereka zipatso nyengo iliyonse ndi chilolezo cha Ambuye wake ndipo Mulungu amapereka mafanizo kwa anthu ndi cholinga chakuti azikumbukira

14:26

وَمَثَلُ كَلِمَةٍ خَبِيثَةٍ كَشَجَرَةٍ خَبِيثَةٍ ٱجۡتُثَّتۡ مِن فَوۡقِ ٱلۡأَرۡضِ مَا لَهَا مِن قَرَارٍ

Ndipo chitsanzo cha liwu loipa lili ngati mtengo woipa, umene uzulidwa kuchoka ku nthaka ndipo ulibe mizu ina iliyonse

14:27

يُثَبِّتُ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱلۡقَوۡلِ ٱلثَّابِتِ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِۖ وَيُضِلُّ ٱللَّهُ ٱلظَّٰلِمِينَۚ وَيَفۡعَلُ ٱللَّهُ مَا يَشَآءُ

Mulungu adzalimbikitsa anthu okhulupirira ndi liwu lokhazikika m’moyo uno ndi m’moyo umene uli nkudza. Ndipo Mulungu adzasocheretsa ochita zoipa ndipo Mulungu amachita zimene Iye afuna

14:28

أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ بَدَّلُواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ كُفۡرًا وَأَحَلُّواْ قَوۡمَهُمۡ دَارَ ٱلۡبَوَارِ

Kodi siunaone iwo amene amasinthanitsa chisomo cha Mulungu ndi kusakhulupirira ndi kuwakankhizira anthu awo kuti akhale m’nyumba ya mazunzo

14:29

جَهَنَّمَ يَصۡلَوۡنَهَاۖ وَبِئۡسَ ٱلۡقَرَارُ

Ndipo Gahena, m’mene iwo akalowe, ndi malo oipa kukhalako

14:30

وَجَعَلُواْ لِلَّهِ أَندَادًا لِّيُضِلُّواْ عَن سَبِيلِهِۦۗ قُلۡ تَمَتَّعُواْ فَإِنَّ مَصِيرَكُمۡ إِلَى ٱلنَّارِ

Iwo akhazikitsa milungu yabodza kuti ikhale yofanana ndi Mulungu ndi cholinga chosokoneza anthu ku njira yake. Nena, “Basangalalani! Koma, ndithudi, kokafikira kwanu ndi ku Moto.”

14:31

قُل لِّعِبَادِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ يُقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُنفِقُواْ مِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ سِرًّا وَعَلَانِيَةً مِّن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَ يَوۡمٌ لَّا بَيۡعٌ فِيهِ وَلَا خِلَٰلٌ

Auze akapolo anga, amene ali okhulupirira kuti apitirize mapemphero ndi kupereka zothandiza osauka kuchokera ku zimene tawapatsa mseri ndi pooneka, lisanafike tsiku limene sikudzakhala kukambirana kapena kuchita ubwenzi

14:32

ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَأَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَأَخۡرَجَ بِهِۦ مِنَ ٱلثَّمَرَٰتِ رِزۡقًا لَّكُمۡۖ وَسَخَّرَ لَكُمُ ٱلۡفُلۡكَ لِتَجۡرِيَ فِي ٱلۡبَحۡرِ بِأَمۡرِهِۦۖ وَسَخَّرَ لَكُمُ ٱلۡأَنۡهَٰرَ

Ndi Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo amagwetsa madzi kuchokera kumwamba amene amameretsa zipatso kuti zikhale chakudya chanu. Iye adapanga zombo kuti muzizigwiritsa ntchito; kuti zikhoza kuyenda pa nyanja ndi chilolezo chake ndipo adapanga mitsinje kuti izikutumikirani

14:33

وَسَخَّرَ لَكُمُ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ دَآئِبَيۡنِۖ وَسَخَّرَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ

Ndipo adalenga dzuwa ndi mwezi, zimene zimayenda mokhazikika m’misewu yawo kuti muzigwiritsa ntchito. Ndipo adalenga usiku ndi usana kuti muziugwiritsa ntchito

14:34

وَءَاتَىٰكُم مِّن كُلِّ مَا سَأَلۡتُمُوهُۚ وَإِن تَعُدُّواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ لَا تُحۡصُوهَآۗ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَظَلُومٌ كَفَّارٌ

Ndipo Iye adakupatsani zonse zimene mudamupempha ndipo ngati inu muwerenga zokoma za Mulungu inu simungathe kuziwerenga zonse. Zoonadi munthu ndi wosayamika ndi wosakhulupirira

14:35

وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِيمُ رَبِّ ٱجۡعَلۡ هَٰذَا ٱلۡبَلَدَ ءَامِنًا وَٱجۡنُبۡنِي وَبَنِيَّ أَن نَّعۡبُدَ ٱلۡأَصۡنَامَ

Ndipo pamenepo Abrahamu adati, “oh Ambuye wanga! Upangeni uwu kukhala Mzinda wamtendere ndipo nditetezeni ine ndi ana anga kuti tisapembedze mafano.”

14:36

رَبِّ إِنَّهُنَّ أَضۡلَلۡنَ كَثِيرًا مِّنَ ٱلنَّاسِۖ فَمَن تَبِعَنِي فَإِنَّهُۥ مِنِّيۖ وَمَنۡ عَصَانِي فَإِنَّكَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ

“oh Ambuye wanga! Ndithudi mafano asocheretsa anthu ambiri. Koma iye amene anditsatira ine ndithudi adzakhala wa ine. Koma aliyense amene sandimvera ine, komabe Inu ndinu okhululukira ndi wachisoni chosatha.”

14:37

رَّبَّنَآ إِنِّيٓ أَسۡكَنتُ مِن ذُرِّيَّتِي بِوَادٍ غَيۡرِ ذِي زَرۡعٍ عِندَ بَيۡتِكَ ٱلۡمُحَرَّمِ رَبَّنَا لِيُقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ فَٱجۡعَلۡ أَفۡـِٔدَةً مِّنَ ٱلنَّاسِ تَهۡوِيٓ إِلَيۡهِمۡ وَٱرۡزُقۡهُم مِّنَ ٱلثَّمَرَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَشۡكُرُونَ

“Oh Ambuye wathu! Ine ndakhazika ena mwa ana anga m’dambo lopanda zomera limene lili pafupi ndi Nyumba yanu yoyera, Oh Ambuye wathu, kuti iwo azipemphera. Motero dzazani mitima ya anthu ndi chikondi kuti awaonetsere iwo ndipo apatseni iwo zipatso kuti akhale othokoza.”

14:38

رَبَّنَآ إِنَّكَ تَعۡلَمُ مَا نُخۡفِي وَمَا نُعۡلِنُۗ وَمَا يَخۡفَىٰ عَلَى ٱللَّهِ مِن شَيۡءٍ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فِي ٱلسَّمَآءِ

“Oh Ambuye wathu! Ndithudi inu mumadziwa zonse zimene timazibisa ndi zonse zimene timaulula. Palibe china pa dziko lapansi kapena kumwamba chimene chimabisika kwa Mulungu.”

14:39

ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي وَهَبَ لِي عَلَى ٱلۡكِبَرِ إِسۡمَٰعِيلَ وَإِسۡحَٰقَۚ إِنَّ رَبِّي لَسَمِيعُ ٱلدُّعَآءِ

“Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu amene wandipatsa ine Ishimayeli ndi Isake ku ukalamba wanga. Ndithudi! Ambuye wanga ndiye amene amamva mapemphero onse.”

14:40

رَبِّ ٱجۡعَلۡنِي مُقِيمَ ٱلصَّلَوٰةِ وَمِن ذُرِّيَّتِيۚ رَبَّنَا وَتَقَبَّلۡ دُعَآءِ

“oh Ambuye wanga! Ndipangeni ine kukhala mmodzi wopemphera ndiponso kuchokera ku ana anga. Ambuye wathu! Landirani pempho langa.”

14:41

رَبَّنَا ٱغۡفِرۡ لِي وَلِوَٰلِدَيَّ وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ يَوۡمَ يَقُومُ ٱلۡحِسَابُ

“Ambuye wathu! Khululukireni ine ndi makolo anga ndi onse okhulupirira pa tsiku limene zonse zidzakhazikitsidwa.”

14:42

وَلَا تَحۡسَبَنَّ ٱللَّهَ غَٰفِلًا عَمَّا يَعۡمَلُ ٱلظَّٰلِمُونَۚ إِنَّمَا يُؤَخِّرُهُمۡ لِيَوۡمٍ تَشۡخَصُ فِيهِ ٱلۡأَبۡصَٰرُ

Usaganize kuti Mulungu sadziwa ntchito za anthu ochita zoipa koma Iye akungowasiya mpaka patsiku limene maso awo adzaona motuzuka

14:43

مُهۡطِعِينَ مُقۡنِعِي رُءُوسِهِمۡ لَا يَرۡتَدُّ إِلَيۡهِمۡ طَرۡفُهُمۡۖ وَأَفۡـِٔدَتُهُمۡ هَوَآءٌ

Iwo adzathamanga kupita kutsogolo, makosi osololoka, mitu yokwezedwa ndi maso awo otuzuka ndipo mitima yawo idzakhala yopanda chilichonse

14:44

وَأَنذِرِ ٱلنَّاسَ يَوۡمَ يَأۡتِيهِمُ ٱلۡعَذَابُ فَيَقُولُ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ رَبَّنَآ أَخِّرۡنَآ إِلَىٰٓ أَجَلٍ قَرِيبٍ نُّجِبۡ دَعۡوَتَكَ وَنَتَّبِعِ ٱلرُّسُلَۗ أَوَلَمۡ تَكُونُوٓاْ أَقۡسَمۡتُم مِّن قَبۡلُ مَا لَكُم مِّن زَوَالٍ

Achenjeze anthu za tsiku limene chilango chidzadza pa iwo ndipo anthu ochita zoipa adzati, “Ambuye wathu tipatseni mpumulo wa kanthawi kochepa ndipo ife tidzamvera kuitana kwanu ndi kutsatira Atumwi anu.” Koma adzati kwa iwo, “Kodi inu nthawi zina simudalumbira kuti simudzafa?”

14:45

وَسَكَنتُمۡ فِي مَسَٰكِنِ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَتَبَيَّنَ لَكُمۡ كَيۡفَ فَعَلۡنَا بِهِمۡ وَضَرَبۡنَا لَكُمُ ٱلۡأَمۡثَالَ

Inu mumakhala m’nyumba za anthu amene adachimwira miyoyo yawo pamene mumadziwa zonse zimene tidawachitira iwo. Ndipo Ife tidakuikirani chitsanzo

14:46

وَقَدۡ مَكَرُواْ مَكۡرَهُمۡ وَعِندَ ٱللَّهِ مَكۡرُهُمۡ وَإِن كَانَ مَكۡرُهُمۡ لِتَزُولَ مِنۡهُ ٱلۡجِبَالُ

Ndithudi iwo akonza chiwembu chawo ndipo chiwembu chawo chili ndi Mulungu ngakhale kuti chiwembu chawo chinali choti, chingathe kuchotsa mapiri

14:47

فَلَا تَحۡسَبَنَّ ٱللَّهَ مُخۡلِفَ وَعۡدِهِۦ رُسُلَهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ ذُو ٱنتِقَامٍ

Musaganize kuti Mulungu adzalephera kukwaniritsa lonjezo lake limene adapereka kwa Atumwi ake. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu ndipo amatha kulanga

14:48

يَوۡمَ تُبَدَّلُ ٱلۡأَرۡضُ غَيۡرَ ٱلۡأَرۡضِ وَٱلسَّمَٰوَٰتُۖ وَبَرَزُواْ لِلَّهِ ٱلۡوَٰحِدِ ٱلۡقَهَّارِ

Pa tsiku limene dziko lapansi lidzasinthidwa kukhala dziko lapansi la mtundu wina, ndi kumwamba kukhala kwa tsopano, mtundu onse udzaonekera pamaso pa Mulungu, Mmodzi yekha yemwe ndi Mwini mphamvu zonse

14:49

وَتَرَى ٱلۡمُجۡرِمِينَ يَوۡمَئِذٍ مُّقَرَّنِينَ فِي ٱلۡأَصۡفَادِ

Pa tsiku limeneli iwe udzaona anthu osakhulupirira atamangidwa m’magoli

14:50

سَرَابِيلُهُم مِّن قَطِرَانٍ وَتَغۡشَىٰ وُجُوهَهُمُ ٱلنَّارُ

Zovala zawo zidzakhala zakuda ngati phula ndi nkhope zawo zidzakutidwa ndi malawi a moto

14:51

لِيَجۡزِيَ ٱللَّهُ كُلَّ نَفۡسٍ مَّا كَسَبَتۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَرِيعُ ٱلۡحِسَابِ

Kuti Mulungu alipire munthu aliyense pa zimene adachita. Ndithudi Mulungu ndi wachangu powerengera

14:52

هَٰذَا بَلَٰغٌ لِّلنَّاسِ وَلِيُنذَرُواْ بِهِۦ وَلِيَعۡلَمُوٓاْ أَنَّمَا هُوَ إِلَٰهٌ وَٰحِدٌ وَلِيَذَّكَّرَ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Uwu ndi uthenga kwa anthu onse kuti achenjezedwe nawo ndi kudziwa kuti Mulungu ndi mmodzi yekha ndi kuti anthu anzeru akumbukire

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.