Surah 15 · 99 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Hijr in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

15:1

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ وَقُرۡءَانٍ مُّبِينٍ

Alif Lam Ra. Awa ndi mavesi a Buku, ndipo ndi Korani yofotokoza bwino

15:2

رُّبَمَا يَوَدُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡ كَانُواْ مُسۡلِمِينَ

Mwina iwo amene sakhulupirira adzafuna kuti akadakhala Asilamu

15:3

ذَرۡهُمۡ يَأۡكُلُواْ وَيَتَمَتَّعُواْ وَيُلۡهِهِمُ ٱلۡأَمَلُۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ

Alekeni kuti adye, ndi kuti asangalale ndipo alekeni kuti atangwanike ndi chikhulupiriro chabodza. Iwo adzadziwa posachedwapa

15:4

وَمَآ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةٍ إِلَّا وَلَهَا كِتَابٌ مَّعۡلُومٌ

Ndipo Ife sitinaonongepo mzinda wina uliwonse, kupatula pamene nthawi yake itakwana

15:5

مَّا تَسۡبِقُ مِنۡ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ

Anthu sangathe kufulumizitsa chionongeko chawo kapena kuchichedwetsa ayi

15:6

وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِي نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ إِنَّكَ لَمَجۡنُونٌ

Iwo amati, “Iwe, amene Korani yavumbulutsidwa kwa iwe! Ndithudi ndiwe munthu wa misala.”

15:7

لَّوۡمَا تَأۡتِينَا بِٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

“Bwanji siutibweretsera angelo ngati iweyo uli mmodzi mwa onena zoona?”

15:8

مَا نُنَزِّلُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَمَا كَانُوٓاْ إِذًا مُّنظَرِينَ

Ife sitimatsitsa pansi angelo, kupatula ndi choonadi ndipo zitatero iwo sadzapatsidwa nthawi

15:9

إِنَّا نَحۡنُ نَزَّلۡنَا ٱلذِّكۡرَ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ

Ndithudi ndife amene tidatsitsa Korani ndipo, ndithudi, Ife ndife amene tidzaiteteza

15:10

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي شِيَعِ ٱلۡأَوَّلِينَ

Ndithudi Ife tidatumizapo, iwe usanadze, Atumwi ena pakati pa mibadwo yakale

15:11

وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ

Ndipo sikunadze kwa iwo Mtumwi, amene iwo sanamuchite chipongwe

15:12

كَذَٰلِكَ نَسۡلُكُهُۥ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Kotero timalowetsa chisokonezo m’mitima ya anthu ochita zoipa

15:13

لَا يُؤۡمِنُونَ بِهِۦ وَقَدۡ خَلَتۡ سُنَّةُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Iwo sangakhulupirire mu uthenga wa Korani ndipo ndi chizolowezi cha anthu amene adalipo kale

15:14

وَلَوۡ فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابًا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ فَظَلُّواْ فِيهِ يَعۡرُجُونَ

Ndipo ngati Ife tikadatsekula khomo lakumwamba, iwo ndi kumakwera kumwamba mosalekeza

15:15

لَقَالُوٓاْ إِنَّمَا سُكِّرَتۡ أَبۡصَٰرُنَا بَلۡ نَحۡنُ قَوۡمٌ مَّسۡحُورُونَ

Iwo akadakanabe kuti, “Maso athu athobwa. Ndithudi ife talodzedwa.”

15:16

وَلَقَدۡ جَعَلۡنَا فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجًا وَزَيَّنَّٰهَا لِلنَّٰظِرِينَ

Ndithudi Ife taika nyenyezi zikuluzikulu kumwamba ndipo tazikongoletsa kuti zizikondweretsa anthu oyang’ana

15:17

وَحَفِظۡنَٰهَا مِن كُلِّ شَيۡطَٰنٍ رَّجِيمٍ

Ndipo tawateteza malo a kumwamba kwa Satana wotembereredwa

15:18

إِلَّا مَنِ ٱسۡتَرَقَ ٱلسَّمۡعَ فَأَتۡبَعَهُۥ شِهَابٌ مُّبِينٌ

Kupatula iye amene amamvetsera mwakuba, iye amatsatiridwa ndi malawi a moto

15:19

وَٱلۡأَرۡضَ مَدَدۡنَٰهَا وَأَلۡقَيۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ شَيۡءٍ مَّوۡزُونٍ

Ife tidatambasula dziko lapansi ndi kuikamo mapiri ndipo tameletsa mu ilo zinthu zosiyanasiyana chilichonse chili ndi muyeso wake

15:20

وَجَعَلۡنَا لَكُمۡ فِيهَا مَعَٰيِشَ وَمَن لَّسۡتُمۡ لَهُۥ بِرَٰزِقِينَ

Ndipo takupatsani mu ilo njira zopezela chakudya chanu ndi cha izo zimene inu simungathe kuzidyetsa

15:21

وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا عِندَنَا خَزَآئِنُهُۥ وَمَا نُنَزِّلُهُۥٓ إِلَّا بِقَدَرٍ مَّعۡلُومٍ

Palibe chilichonse, chimene nkhokwe yake siili ndi Ife ndipo sititumiza kupatula m’muyeso wodziwika

15:22

وَأَرۡسَلۡنَا ٱلرِّيَٰحَ لَوَٰقِحَ فَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَأَسۡقَيۡنَٰكُمُوهُ وَمَآ أَنتُمۡ لَهُۥ بِخَٰزِنِينَ

Ndipo Ife timatumiza mphepo yobereketsa ndipo timatsitsa madzi kuchokera kumwamba ndipo timakupatsani kuti mumwe; ndipo inu si ndinu osunga nkhokwe zake

15:23

وَإِنَّا لَنَحۡنُ نُحۡيِۦ وَنُمِيتُ وَنَحۡنُ ٱلۡوَٰرِثُونَ

Ndipo, ndithudi, Ife ndife amene timapereka moyo ndi imfa ndipo zinthu zonse ndi zathu

15:24

وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَقۡدِمِينَ مِنكُمۡ وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَـٔۡخِرِينَ

Ndipo, ndithudi, Ife timadziwa onse amene adalipo kale inu musanadze ndipo timadziwa mibadwo yanu yatsopano ndi iwo amene adzadza m’tsogolo

15:25

وَإِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَحۡشُرُهُمۡۚ إِنَّهُۥ حَكِيمٌ عَلِيمٌ

Ndipo, ndithudi, Ambuye wako adzasonkhanitsa onse pamodzi. Zoonadi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa chilichonse

15:26

وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن صَلۡصَٰلٍ مِّنۡ حَمَإٍ مَّسۡنُونٍ

Ndipo, ndithudi, Ife tidamulenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu, losinthidwa m’matope akuda osalala

15:27

وَٱلۡجَآنَّ خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ مِن نَّارِ ٱلسَّمُومِ

Tidapanga mtundu wa majini poyamba kuchokera ku mphepo ya moto

15:28

وَإِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنِّي خَٰلِقُۢ بَشَرًا مِّن صَلۡصَٰلٍ مِّنۡ حَمَإٍ مَّسۡنُونٍ

Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa angelo, “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.”

15:29

فَإِذَا سَوَّيۡتُهُۥ وَنَفَخۡتُ فِيهِ مِن رُّوحِي فَقَعُواْ لَهُۥ سَٰجِدِينَ

“Motero ndikatha kumukonza ndi kuuzira mpweya umene ndidalenga chifukwa cha iye ndipo nonse gwadani kumulambira iye.”

15:30

فَسَجَدَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ كُلُّهُمۡ أَجۡمَعُونَ

Motero Angelo onse adagwada ndi kumulambira

15:31

إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰٓ أَن يَكُونَ مَعَ ٱلسَّٰجِدِينَ

Kupatula Satanaadakanakukhalammodzimwaolambira

15:32

قَالَ يَٰٓإِبۡلِيسُ مَا لَكَ أَلَّا تَكُونَ مَعَ ٱلسَّٰجِدِينَ

Mulungu adati, “oh iwe Satana! Kodi ndi chifukwa chiyani siuli pamodzi ndi olambira?”

15:33

قَالَ لَمۡ أَكُن لِّأَسۡجُدَ لِبَشَرٍ خَلَقۡتَهُۥ مِن صَلۡصَٰلٍ مِّنۡ حَمَإٍ مَّسۡنُونٍ

Satana adati, “Ine sindingagwadire munthu amene Inu mwamulenga kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.”

15:34

قَالَ فَٱخۡرُجۡ مِنۡهَا فَإِنَّكَ رَجِيمٌ

Mulungu adati: “Motero choka kuno chifukwa ndithudi iwe ndiwe wotembereredwa.”

15:35

وَإِنَّ عَلَيۡكَ ٱللَّعۡنَةَ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلدِّينِ

Ndipo, ndithudi, temberero lidzakhala pa iwe mpaka pa tsiku lachiweruzo.”

15:36

قَالَ رَبِّ فَأَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ

Satana adati, “oh Ambuye wanga! Bandisungani mpaka patsiku louka kwa akufa.”

15:37

قَالَ فَإِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ

Mulungu adati, “Ndithudi iwe uli m’gulu la anthu amene apatsidwa nthawi.”

15:38

إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡوَقۡتِ ٱلۡمَعۡلُومِ

“Mpaka pa nthawi ya tsiku lotsimikizika.”

15:39

قَالَ رَبِّ بِمَآ أَغۡوَيۡتَنِي لَأُزَيِّنَنَّ لَهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَأُغۡوِيَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ

Satana adati, “Oh Ambuye wanga! Popeza Inuyo mwandisocheretsa ine, ndithudi, ndidzawasalalitsira njira yautchimo anthu onse padziko lapansi, ndithudi onse ndidzawasocheretsa

15:40

إِلَّا عِبَادَكَ مِنۡهُمُ ٱلۡمُخۡلَصِينَ

Kupatula akapolo anu osankhidwa amene ali pakati pawo.”

15:41

قَالَ هَٰذَا صِرَٰطٌ عَلَيَّ مُسۡتَقِيمٌ

Mulungu adati, “Imeneyi ndiyo njira imene idzalondola mwachindunji kwa Ine.”

15:42

إِنَّ عِبَادِي لَيۡسَ لَكَ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٌ إِلَّا مَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلۡغَاوِينَ

“Ndithudi iwe siudzakhala ndi mphamvu pa akapolo anga, kupatula anthu ochita zoipa amene amakutsatira iweyo.”

15:43

وَإِنَّ جَهَنَّمَ لَمَوۡعِدُهُمۡ أَجۡمَعِينَ

“Ndipo, ndithudi, Gahena ndi malo olonjezedwa kwa iwo onse.”

15:44

لَهَا سَبۡعَةُ أَبۡوَٰبٍ لِّكُلِّ بَابٍ مِّنۡهُمۡ جُزۡءٌ مَّقۡسُومٌ

“Iyo ili ndi makomo asanu ndi awiri, ndipo chipata chilichonse chidzakhala ndi anthu ake olowapo.”

15:45

إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ

“Ndithudi! Onse oopa Mulungu adzakhala m’kati mwa minda ndi m’kati mwa a kasupe.”

15:46

ٱدۡخُلُوهَا بِسَلَٰمٍ ءَامِنِينَ

“Lowanimo mwamtendere mopanda mavuto.”

15:47

وَنَزَعۡنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنۡ غِلٍّ إِخۡوَٰنًا عَلَىٰ سُرُرٍ مُّتَقَٰبِلِينَ

“Ndipo Ife tidzachotsa m’mitima yawo mkwiyo uliwonse kuti akhoza kukhala pachibale ndi kupumula m’mipando yawofowofo moyang’anizana.”

15:48

لَا يَمَسُّهُمۡ فِيهَا نَصَبٌ وَمَا هُم مِّنۡهَا بِمُخۡرَجِينَ

“Ndipo iwo sadzatopa kumeneko ndipo sadzafunsidwa kuti achoke ku Paradiso.”

15:49

نَبِّئۡ عِبَادِيٓ أَنِّيٓ أَنَا ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ

Auze akapolo anga kuti ndithudi Ine ndimakhululukira ndipo ndine wachisoni

15:50

وَأَنَّ عَذَابِي هُوَ ٱلۡعَذَابُ ٱلۡأَلِيمُ

Ndiponso kuti chilango changa, ndithudi, ndi chilango chowawa koposa

15:51

وَنَبِّئۡهُمۡ عَن ضَيۡفِ إِبۡرَٰهِيمَ

Auze za alendo a Abrahamu

15:52

إِذۡ دَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَقَالُواْ سَلَٰمًا قَالَ إِنَّا مِنكُمۡ وَجِلُونَ

Pamene iwo adadza kwa iye ndi kumuuza kuti, “Mtendere ukhale kwa iwe.’ Koma iye adawayankha kuti, “Ndili ndi mantha ndi inu.”

15:53

قَالُواْ لَا تَوۡجَلۡ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ عَلِيمٍ

Iwo adati, “Usaope! Ife tadza kwa iwe ndi nkhani yabwino ya mwana wamwamuna amene adzakhala wodziwa zambiri.”

15:54

قَالَ أَبَشَّرۡتُمُونِي عَلَىٰٓ أَن مَّسَّنِيَ ٱلۡكِبَرُ فَبِمَ تُبَشِّرُونَ

Iye adati, “Kodi inu muli kudzandiuza nkhani yabwino pamene ine nditakalamba kale? “Kodi nkhani yanu ndi yotani?”

15:55

قَالُواْ بَشَّرۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ فَلَا تَكُن مِّنَ ٱلۡقَٰنِطِينَ

Iwo adati, “Ife tili kukuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi. Kotero usakhale wotaya mtima.”

15:56

قَالَ وَمَن يَقۡنَطُ مِن رَّحۡمَةِ رَبِّهِۦٓ إِلَّا ٱلضَّآلُّونَ

Iye adati, “Ndani amene angataye mtima ndi chifundo cha Mulungu, kupatula osochera?”

15:57

قَالَ فَمَا خَطۡبُكُمۡ أَيُّهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ

Iye adatinso, “Kodi cholinga chanu ndi chiyani, inu otumidwa?”

15:58

قَالُوٓاْ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمٍ مُّجۡرِمِينَ

Iwo adati, “Ife tatumidwa kwa anthu oipa.”

15:59

إِلَّآ ءَالَ لُوطٍ إِنَّا لَمُنَجُّوهُمۡ أَجۡمَعِينَ

“onse kupatula anthu otsatira Loti okha. Ife, ndithudi, tidzawapulumutsa iwo okha.”

15:60

إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ قَدَّرۡنَآ إِنَّهَا لَمِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ

“Kupatula mkazi wake amene ife talamulidwa kuti akhalire m’mbuyo pamodzi ndi iwo amene anali kukhalira m’mbuyo.”

15:61

فَلَمَّا جَآءَ ءَالَ لُوطٍ ٱلۡمُرۡسَلُونَ

Ndipo pamene a Kazembe athu adadza ku nyumba ya Loti

15:62

قَالَ إِنَّكُمۡ قَوۡمٌ مُّنكَرُونَ

Loti adati, “Ndithudi inu ndinu anthu omwe sindikudziwani.”

15:63

قَالُواْ بَلۡ جِئۡنَٰكَ بِمَا كَانُواْ فِيهِ يَمۡتَرُونَ

Iwo adati, “Iyayi. Ife takubweretsera iweyo zinthu zimene iwo anali kukayika.”

15:64

وَأَتَيۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ

“Ndipo Ife tadza ndi choonadi kwa iwe ndipo, ndithudi, ife ndife onena zoona.”

15:65

فَأَسۡرِ بِأَهۡلِكَ بِقِطۡعٍ مِّنَ ٱلَّيۡلِ وَٱتَّبِعۡ أَدۡبَٰرَهُمۡ وَلَا يَلۡتَفِتۡ مِنكُمۡ أَحَدٌ وَٱمۡضُواْ حَيۡثُ تُؤۡمَرُونَ

“Motero choka ndi abale ako pakati pa usiku, iwe uziyenda pambuyo pawo ndipo usalole wina aliyense kuti atembenuke. Kapita kumene walamulidwa kupita.”

15:66

وَقَضَيۡنَآ إِلَيۡهِ ذَٰلِكَ ٱلۡأَمۡرَ أَنَّ دَابِرَ هَٰٓؤُلَآءِ مَقۡطُوعٌ مُّصۡبِحِينَ

Ndipo tidamuuza lamulo ili kuti mizu ya iwo idzazulidwa m’mawa

15:67

وَجَآءَ أَهۡلُ ٱلۡمَدِينَةِ يَسۡتَبۡشِرُونَ

Ndipo anthu a mu Mzinda adadza ali osangala

15:68

قَالَ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ ضَيۡفِي فَلَا تَفۡضَحُونِ

Iye adati, “Ndithudi! Awa ndi alendo anga motero musandichititse manyazi ayi.”

15:69

وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَلَا تُخۡزُونِ

“opani Mulungu ndipo musandipangitse manyazi.”

15:70

قَالُوٓاْ أَوَلَمۡ نَنۡهَكَ عَنِ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Iwo adati, “Kodi ife sitidakuletse kuti uzichereza alendo?”

15:71

قَالَ هَٰٓؤُلَآءِ بَنَاتِيٓ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ

Iye adati, “Awa ndi ana anga a aakazi; akwatireni ngati inu mufunadi kutero.”

15:72

لَعَمۡرُكَ إِنَّهُمۡ لَفِي سَكۡرَتِهِمۡ يَعۡمَهُونَ

Ndithudi pali moyo wako! Iwo chifukwa chakuledzera anali kuyenda mwakhungu

15:73

فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُشۡرِقِينَ

Ndipo chilango chidawapeza pamene dzuwa linkatuluka

15:74

فَجَعَلۡنَا عَٰلِيَهَا سَافِلَهَا وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِمۡ حِجَارَةً مِّن سِجِّيلٍ

Ndipo Ife tidaononga (mizinda yawo) zapansi kukhala pamwamba ndipo tidawagwetsera mvula ya miyala ya moto

15:75

إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّلۡمُتَوَسِّمِينَ

Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu omvetsa

15:76

وَإِنَّهَا لَبِسَبِيلٍ مُّقِيمٍ

Ndipo, ndithudi, iyo ili m’mphepete mwa msewu umene umapitidwa

15:77

إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةً لِّلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndithudi! Muizimulizizindikirokwaanthuokhulupirira

15:78

وَإِن كَانَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأَيۡكَةِ لَظَٰلِمِينَ

Ngakhale anthu okhala m’nkhalango nawonso anali ochimwa

15:79

فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ وَإِنَّهُمَا لَبِإِمَامٍ مُّبِينٍ

Motero Ife tidawalanga. Ndipo iwo ali pamalo poonekera

15:80

وَلَقَدۡ كَذَّبَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡحِجۡرِ ٱلۡمُرۡسَلِينَ

Ndipo, ndithudi, anthu a ku Hijr adakana Atumwi

15:81

وَءَاتَيۡنَٰهُمۡ ءَايَٰتِنَا فَكَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ

Ndipo Ife tidawapatsa zizindikiro zathu koma iwo adazikana

15:82

وَكَانُواْ يَنۡحِتُونَ مِنَ ٱلۡجِبَالِ بُيُوتًا ءَامِنِينَ

Ndipo iwo anali kukumba mapiri kukhala nyumba zawo ndipo anali kukhala mosaopa

15:83

فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُصۡبِحِينَ

Phokoso la chilango lidafika kwa iwo m’mawa

15:84

فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Ndipo sizidawathandize zonse zimene anali kuchita

15:85

وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَإِنَّ ٱلسَّاعَةَ لَأٓتِيَةٌۖ فَٱصۡفَحِ ٱلصَّفۡحَ ٱلۡجَمِيلَ

Ndipo Ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo kupatula ndi choonadi. Ndithudi popanda chikayiko tsiku lachiweruzo lidzadza; kotero akhululukireni, kukhululuka kwabwino

15:86

إِنَّ رَبَّكَ هُوَ ٱلۡخَلَّٰقُ ٱلۡعَلِيمُ

Ndithudi Ambuye wako ndi Namalenga ndi wodziwa zinthu zonse

15:87

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَٰكَ سَبۡعًا مِّنَ ٱلۡمَثَانِي وَٱلۡقُرۡءَانَ ٱلۡعَظِيمَ

Ndipo, ndithudi, Ife tidakupatsa mavesi asanu ndi awiri amene amanenedwa kawirikawiri ndi Korani yolemekezeka

15:88

لَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجًا مِّنۡهُمۡ وَلَا تَحۡزَنۡ عَلَيۡهِمۡ وَٱخۡفِضۡ جَنَاحَكَ لِلۡمُؤۡمِنِينَ

Usamayang’ane mwanjiru zinthu zokoma zimene tawapatsa ena a iwo kapena kumamva chisoni pa izo. Ndipo onetsani chifundo kwa anthu okhulupirira

15:89

وَقُلۡ إِنِّيٓ أَنَا ٱلنَّذِيرُ ٱلۡمُبِينُ

Ndipo Nena, “Ine ndine Mchenjezi”

15:90

كَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَى ٱلۡمُقۡتَسِمِينَ

Monga tidatumiza kwa amene amagawanitsa

15:91

ٱلَّذِينَ جَعَلُواْ ٱلۡقُرۡءَانَ عِضِينَ

Amene apanga Buku la Korani kukhala magawo awiri

15:92

فَوَرَبِّكَ لَنَسۡـَٔلَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ

Kotero, pali Ambuye wako, tidzawafunsa

15:93

عَمَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Pa zonse zimene anali kuchita

15:94

فَٱصۡدَعۡ بِمَا تُؤۡمَرُ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡمُشۡرِكِينَ

Motero lalikira poyera zonse zimene walamulidwa, ndipo choka pakati pa osakhulupirira

15:95

إِنَّا كَفَيۡنَٰكَ ٱلۡمُسۡتَهۡزِءِينَ

Ndithudi Ife tidzakuteteza kwa onyoza

15:96

ٱلَّذِينَ يَجۡعَلُونَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ

Iwo amene amatumikira mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni iwowo adzadziwa

15:97

وَلَقَدۡ نَعۡلَمُ أَنَّكَ يَضِيقُ صَدۡرُكَ بِمَا يَقُولُونَ

Ndithudi Ife tilikudziwakutizimakupweteka mumtima mwako zinthu zimene amanena

15:98

فَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ وَكُن مِّنَ ٱلسَّٰجِدِينَ

Motero lemekeza Ambuye wako ndipo khala mmodzi wa iwo amene amagwada pomulemekeza Iye

15:99

وَٱعۡبُدۡ رَبَّكَ حَتَّىٰ يَأۡتِيَكَ ٱلۡيَقِينُ

Ndipo pembedza Ambuye wako mpaka pamene ola lotsimikizidwa likupeza

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.