Surah 33 · 73 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Ahzab in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

33:1

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ ٱتَّقِ ٱللَّهَ وَلَا تُطِعِ ٱلۡكَٰفِرِينَ وَٱلۡمُنَٰفِقِينَۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمًا

Oh iwe Mtumwi! Opa Mulungu ndipo usamvere zonena za anthu osakhulupirira ndi a chinyengo. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha

33:2

وَٱتَّبِعۡ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرًا

Koma tsatira zonse zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako ndithudi Mulungu amadziwa zimene umachita

33:3

وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلًا

Ndipo ukhale ndi chikhulupiriro mwa Mulungu chifukwa Iye ndi wokwana kukhala wokusamalira iwe

33:4

مَّا جَعَلَ ٱللَّهُ لِرَجُلٍ مِّن قَلۡبَيۡنِ فِي جَوۡفِهِۦۚ وَمَا جَعَلَ أَزۡوَٰجَكُمُ ٱلَّٰٓـِٔي تُظَٰهِرُونَ مِنۡهُنَّ أُمَّهَٰتِكُمۡۚ وَمَا جَعَلَ أَدۡعِيَآءَكُمۡ أَبۡنَآءَكُمۡۚ ذَٰلِكُمۡ قَوۡلُكُم بِأَفۡوَٰهِكُمۡۖ وَٱللَّهُ يَقُولُ ٱلۡحَقَّ وَهُوَ يَهۡدِي ٱلسَّبِيلَ

Mulungusadalengemitimaiwirim’chifuwachamunthu, ndipo Iye sadalenge akazi anu amene mumawasudzula chifukwa chakuti amalingana ndi amayi anu, ndipo sadawalenge ana omwe mkazi wanu adabereka ndi mwamuna wina kukhala ana anu enieni. Zimenezo ndizo zongokamba zanu chabe koma Mulungu ali kukuuzani inu choonadi ndipo Iye amalangiza njira yoyenera

33:5

ٱدۡعُوهُمۡ لِأٓبَآئِهِمۡ هُوَ أَقۡسَطُ عِندَ ٱللَّهِۚ فَإِن لَّمۡ تَعۡلَمُوٓاْ ءَابَآءَهُمۡ فَإِخۡوَٰنُكُمۡ فِي ٱلدِّينِ وَمَوَٰلِيكُمۡۚ وَلَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ فِيمَآ أَخۡطَأۡتُم بِهِۦ وَلَٰكِن مَّا تَعَمَّدَتۡ قُلُوبُكُمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا

Aitaneni ndi mayina atate awo ana onse omwe mkazi wanu adaberaka ndi mwamuna wina chifukwa chimenecho ndicho chilungamo pamaso pa Mulungu. Koma ngati inu simudziwa mayina atate awo, pamenepo iwo ndi abale anu m’chipembedzo kapena abwenzi. Koma palibe cholakwa kwa inu ngati mulakwitsa. Chimene chifunika kwenikweni ndi cholinga chimene chili mu mtima mwanu. Ndithudi Mulungu amakhululukira nthawi zonse ndipo ndi mwini chisoni chosatha

33:6

ٱلنَّبِيُّ أَوۡلَىٰ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ مِنۡ أَنفُسِهِمۡۖ وَأَزۡوَٰجُهُۥٓ أُمَّهَٰتُهُمۡۗ وَأُوْلُواْ ٱلۡأَرۡحَامِ بَعۡضُهُمۡ أَوۡلَىٰ بِبَعۡضٍ فِي كِتَٰبِ ٱللَّهِ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُهَٰجِرِينَ إِلَّآ أَن تَفۡعَلُوٓاْ إِلَىٰٓ أَوۡلِيَآئِكُم مَّعۡرُوفًاۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَسۡطُورًا

Mtumwi ali ndi udindo waukulu pa anthu okhulupirira kuposa umene iwo ali nawo pakati pa wina ndi mnzake ndipo akazi a Mtumwi ali ngati amayi awo. Ndipo ubale wa magazi amodzi pakati pawo umawabweretsa pafupi wina ndi mnzake. M’Buku la Mulungu, ubale umene umadza kwa iwo amene akhulupirira uposa amene amathawa ku nyumba kwawo. Ngakhale zili choncho inu muyenera kuonetsa zabwino kwa abwenzi anu. Zimenezi ndizo zimene zidalembedwa m’Buku la Mulungu

33:7

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ مِيثَٰقَهُمۡ وَمِنكَ وَمِن نُّوحٍ وَإِبۡرَٰهِيمَ وَمُوسَىٰ وَعِيسَى ٱبۡنِ مَرۡيَمَۖ وَأَخَذۡنَا مِنۡهُم مِّيثَٰقًا غَلِيظًا

Kumbukira pamene tidalandira lonjezo lochokera kwa Atumwi ndi kwa iwe. Ndiponso kuchokera kwa Nowa, Abrahamu, Mose, ndi Yesu mwana wamwamuna wa Maria. Tidalandira lonjezo lokhazikika kuchokera kwa iwo

33:8

لِّيَسۡـَٔلَ ٱلصَّٰدِقِينَ عَن صِدۡقِهِمۡۚ وَأَعَدَّ لِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابًا أَلِيمًا

Kuti Mulungu akhoza kufunsa anthu olungama za chilungamo chawo ndipo Iye wawakonzera anthu osakhulupirira chilango chowawa kwambiri

33:9

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ إِذۡ جَآءَتۡكُمۡ جُنُودٌ فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِيحًا وَجُنُودًا لَّمۡ تَرَوۡهَاۚ وَكَانَ ٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرًا

oh inu anthu okhulupirira! Kumbukirani chisomo cha Mulungu pa inu pamene kudadza gulu la adani. Koma Ife tidatumiza, kuti iwagonjetse, mphepo ya mkuntho ndi Asirikali amene inu simudawaone. Koma Mulungu amaona zonse zimene mumachita

33:10

إِذۡ جَآءُوكُم مِّن فَوۡقِكُمۡ وَمِنۡ أَسۡفَلَ مِنكُمۡ وَإِذۡ زَاغَتِ ٱلۡأَبۡصَٰرُ وَبَلَغَتِ ٱلۡقُلُوبُ ٱلۡحَنَاجِرَ وَتَظُنُّونَ بِٱللَّهِ ٱلظُّنُونَا۠

Pamene iwo adadza kwa inu kuchokera kumwamba ndi kuchokera padziko lapansi ndiponso pamene maso adatembenuka, mitima yanu idafumuka mpaka pakhosi ndipo inu mudayamba kuganiza maganizo oipa okhudza Mulungu

33:11

هُنَالِكَ ٱبۡتُلِيَ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ وَزُلۡزِلُواْ زِلۡزَالًا شَدِيدًا

Pamenepo anthu onse okhulupirira adayesedwa ndipo adavutitsidwa

33:12

وَإِذۡ يَقُولُ ٱلۡمُنَٰفِقُونَ وَٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ مَّا وَعَدَنَا ٱللَّهُ وَرَسُولُهُۥٓ إِلَّا غُرُورًا

Ndipo taona! Anthu onse a chinyengo ndi iwo amene mu mitima mwawo muli matenda adati, “Mulungu pamodzi ndi Mtumwi wake sadatilonjeze china chilichonse koma chinyengo.”

33:13

وَإِذۡ قَالَت طَّآئِفَةٌ مِّنۡهُمۡ يَٰٓأَهۡلَ يَثۡرِبَ لَا مُقَامَ لَكُمۡ فَٱرۡجِعُواْۚ وَيَسۡتَـٔۡذِنُ فَرِيقٌ مِّنۡهُمُ ٱلنَّبِيَّ يَقُولُونَ إِنَّ بُيُوتَنَا عَوۡرَةٌ وَمَا هِيَ بِعَوۡرَةٍۖ إِن يُرِيدُونَ إِلَّا فِرَارًا

Taona! Gulu lina limene lidali pakati pawo lidati, “Inu anthu a ku Yasrib simungawagonjetse awa ayi kotero bwererani m’mbuyo!” Ndipo kagulu kena kamapempha chilolezo kwa Mtumwi ndipo kadati, “Ndithudi nyumba zathu zilibe woziteteza.” Koma sizinali choncho ayi koma kuti iwo amangofuna kupeza njira yothawira

33:14

وَلَوۡ دُخِلَتۡ عَلَيۡهِم مِّنۡ أَقۡطَارِهَا ثُمَّ سُئِلُواْ ٱلۡفِتۡنَةَ لَأٓتَوۡهَا وَمَا تَلَبَّثُواْ بِهَآ إِلَّا يَسِيرًا

Ndipo mdani akadalowa kudzera pachipata cha mbali ina ya mzindawu, ndipo iwo akadafunsidwa kuti aleke chisilamu. Ndithudi, iwo akadachita chomwecho. Ndipo sakadakayika kutero, ngakhale mpang’ono pomwe

33:15

وَلَقَدۡ كَانُواْ عَٰهَدُواْ ٱللَّهَ مِن قَبۡلُ لَا يُوَلُّونَ ٱلۡأَدۡبَٰرَۚ وَكَانَ عَهۡدُ ٱللَّهِ مَسۡـُٔولًا

Komatu iwo adalonjeza kale kwa Mulungu kuti sadzabwerera m’mbuyo ndipo lonjezo la Mulungu liyenera kukwaniritsidwa

33:16

قُل لَّن يَنفَعَكُمُ ٱلۡفِرَارُ إِن فَرَرۡتُم مِّنَ ٱلۡمَوۡتِ أَوِ ٱلۡقَتۡلِ وَإِذًا لَّا تُمَتَّعُونَ إِلَّا قَلِيلًا

Nena, “Kuthawa sikudzakuthandizani inu ngati inu muli kuthawa imfa, kapena kuphedwa. Ndipo ngakhale kuti inu mungathawe, mudzangosangalala m’moyo wa pa dziko lino lapansi pa kanthawi kochepa chabe.”

33:17

قُلۡ مَن ذَا ٱلَّذِي يَعۡصِمُكُم مِّنَ ٱللَّهِ إِنۡ أَرَادَ بِكُمۡ سُوٓءًا أَوۡ أَرَادَ بِكُمۡ رَحۡمَةًۚ وَلَا يَجِدُونَ لَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا

Nena, “Kodi ndani amene angakutetezeni inu kwa Mulungu ngati iye atafuna kuti akulangeni inu? Kodi ndani amene akhoza kumuletsa Mulungu ngati atafuna kuti akuonetseni chifundo chake?” Ndipo iwo sadzapeza wina kupatula Mulungu kukhala mtetezi kapena mthandizi wawo

33:18

قَدۡ يَعۡلَمُ ٱللَّهُ ٱلۡمُعَوِّقِينَ مِنكُمۡ وَٱلۡقَآئِلِينَ لِإِخۡوَٰنِهِمۡ هَلُمَّ إِلَيۡنَاۖ وَلَا يَأۡتُونَ ٱلۡبَأۡسَ إِلَّا قَلِيلًا

Ndithudi Mulungu amawadziwa onse amene amaletsa anzawo ndi iwo amene amauza abale awo kuti, “Bwerani kwa ife.” Pamene iwo sadza ku nkhondo kupatula ochepa

33:19

أَشِحَّةً عَلَيۡكُمۡۖ فَإِذَا جَآءَ ٱلۡخَوۡفُ رَأَيۡتَهُمۡ يَنظُرُونَ إِلَيۡكَ تَدُورُ أَعۡيُنُهُمۡ كَٱلَّذِي يُغۡشَىٰ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡمَوۡتِۖ فَإِذَا ذَهَبَ ٱلۡخَوۡفُ سَلَقُوكُم بِأَلۡسِنَةٍ حِدَادٍ أَشِحَّةً عَلَى ٱلۡخَيۡرِۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَمۡ يُؤۡمِنُواْ فَأَحۡبَطَ ٱللَّهُ أَعۡمَٰلَهُمۡۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرًا

Ndi njiru imene ali nayo pa iwe, pamene choopsa chidza, iwe udzawaona ali kukuyang’ana, maso awo ali kutembenuzika, monga munthu amene ali pafupi kufa. Komangatichoopsachidutsaiwoamakunyozandimalirime awo akuthwa chifukwa cha njiru pa zinthu zabwino zimene uli nazo. Awa sadakhulupirire ndipo Mulungu wasandutsa zochita zawo kukhala zopanda pake ndipo zimenezi si zovuta kwa Mulungu

33:20

يَحۡسَبُونَ ٱلۡأَحۡزَابَ لَمۡ يَذۡهَبُواْۖ وَإِن يَأۡتِ ٱلۡأَحۡزَابُ يَوَدُّواْ لَوۡ أَنَّهُم بَادُونَ فِي ٱلۡأَعۡرَابِ يَسۡـَٔلُونَ عَنۡ أَنۢبَآئِكُمۡۖ وَلَوۡ كَانُواْ فِيكُم مَّا قَٰتَلُوٓاْ إِلَّا قَلِيلًا

Iwo akuganiza kuti owathandiza awo alipo ndipo ngati iwo akadabweranso iwo akadafuna akadakhala ali m’chipululu pamodzi ndi anthu okhala m’chipululu ndi kufunsa nkhani zokhudza iwe kuchokera kutali. Ndipo iwo akadakhala pakati panu, akadamenya nkhondo pang’ono

33:21

لَّقَدۡ كَانَ لَكُمۡ فِي رَسُولِ ٱللَّهِ أُسۡوَةٌ حَسَنَةٌ لِّمَن كَانَ يَرۡجُواْ ٱللَّهَ وَٱلۡيَوۡمَ ٱلۡأٓخِرَ وَذَكَرَ ٱللَّهَ كَثِيرًا

Ndithudi muli chitsanzo chabwino mwa Mtumwi wa Mulungu kwa iye amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ndipo amakumbukira Mulungu kwambiri

33:22

وَلَمَّا رَءَا ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٱلۡأَحۡزَابَ قَالُواْ هَٰذَا مَا وَعَدَنَا ٱللَّهُ وَرَسُولُهُۥ وَصَدَقَ ٱللَّهُ وَرَسُولُهُۥۚ وَمَا زَادَهُمۡ إِلَّآ إِيمَٰنًا وَتَسۡلِيمًا

Pamene anthu okhulupirira adaona anzawo owathandiza, iwo adati, “Ichi ndi chimene Mulungu ndi Mtumwi wake adatilonjeza. Ndithudi Mulungu ndi Mtumwi wake adatiuza zoona.” Ndipo izi zidaonjezera chikhulupiriro chawo ndi kudzipereka kwawo kwathunthu

33:23

مِّنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ رِجَالٌ صَدَقُواْ مَا عَٰهَدُواْ ٱللَّهَ عَلَيۡهِۖ فَمِنۡهُم مَّن قَضَىٰ نَحۡبَهُۥ وَمِنۡهُم مَّن يَنتَظِرُۖ وَمَا بَدَّلُواْ تَبۡدِيلًا

Pakati pa okhulupirira pali anthu amene amakwaniritsa lonjezo limene adachita ndi Mulungu. Ena mwa iwo adafa ndipo ena akadadikira. Koma iwo sadasinthe maganizo ngakhale pang’ono

33:24

لِّيَجۡزِيَ ٱللَّهُ ٱلصَّٰدِقِينَ بِصِدۡقِهِمۡ وَيُعَذِّبَ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ إِن شَآءَ أَوۡ يَتُوبَ عَلَيۡهِمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا

Kuti Mulungu akhoza kupereka malipiro kwa anthu olungama chifukwa cha chilungamo chawo ndi kulanga anthu a chinyengo ngati chimenecho ndicho chifuniro chake kapena kuwakhululukira chifukwa Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha

33:25

وَرَدَّ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِغَيۡظِهِمۡ لَمۡ يَنَالُواْ خَيۡرًاۚ وَكَفَى ٱللَّهُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٱلۡقِتَالَۚ وَكَانَ ٱللَّهُ قَوِيًّا عَزِيزًا

Ndipo Mulungu adawabweza anthu osakhulupirira atakwiya. Iwo sadapeze chabwino china chilichonse ndipo Mulungu adawathandiza anthu okhulupirira pomenya nkhondo. Ndipo Mulungu ndi wamphamvu zambiri

33:26

وَأَنزَلَ ٱلَّذِينَ ظَٰهَرُوهُم مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ مِن صَيَاصِيهِمۡ وَقَذَفَ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلرُّعۡبَ فَرِيقًا تَقۡتُلُونَ وَتَأۡسِرُونَ فَرِيقًا

Ndipo anthu a m’Buku amene adawathandiza iwo, Mulungu adawachotsa kumalo awo okhazikika ndipo adakhazika mantha m’mitima mwawo, kotero inu mudapha ena ndi ena mudawagwira ukapolo

33:27

وَأَوۡرَثَكُمۡ أَرۡضَهُمۡ وَدِيَٰرَهُمۡ وَأَمۡوَٰلَهُمۡ وَأَرۡضًا لَّمۡ تَطَـُٔوهَاۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ قَدِيرًا

Ndipo Iye adakupatsani dziko lawo, nyumba zawo, ndi katundu wawo ndi dziko limene inu simuyendamo. Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

33:28

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ قُل لِّأَزۡوَٰجِكَ إِن كُنتُنَّ تُرِدۡنَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا وَزِينَتَهَا فَتَعَالَيۡنَ أُمَتِّعۡكُنَّ وَأُسَرِّحۡكُنَّ سَرَاحًا جَمِيلًا

Oh iwe Mtumwi! Auze akazi ako kuti, “Ngati inu mukonda moyo wa dziko lino ndiponso zosangalatsa zake, bwerani, ine ndidzakupatsani zosangalatsa zake ndipo ndidzakulolani kuti muchoke bwinobwino.”

33:29

وَإِن كُنتُنَّ تُرِدۡنَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَٱلدَّارَ ٱلۡأٓخِرَةَ فَإِنَّ ٱللَّهَ أَعَدَّ لِلۡمُحۡسِنَٰتِ مِنكُنَّ أَجۡرًا عَظِيمًا

Ndipo ngati inu mufuna Mulungu ndi Mtumwi wake ndi moyo umene uli nkudza, ndithudi, Mulungu wawakonzera mphotho yaikulu anthu ochita zabwino amene ali pakati panu

33:30

يَٰنِسَآءَ ٱلنَّبِيِّ مَن يَأۡتِ مِنكُنَّ بِفَٰحِشَةٍ مُّبَيِّنَةٍ يُضَٰعَفۡ لَهَا ٱلۡعَذَابُ ضِعۡفَيۡنِۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرًا

oh inu akazi a Mtumwi! Aliyense wa inu amene achita choipa poyera, chilango chake chidzaonjezedwa kawiri ndipo kutero ndi kwapafupi kwa Mulungu

33:31

وَمَن يَقۡنُتۡ مِنكُنَّ لِلَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتَعۡمَلۡ صَٰلِحًا نُّؤۡتِهَآ أَجۡرَهَا مَرَّتَيۡنِ وَأَعۡتَدۡنَا لَهَا رِزۡقًا كَرِيمًا

Ndipo aliyense wa inu amene ndi omvera Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amachita ntchito zabwino, Ife tidzamupatsa malipiro ake kawiri ndipo tamukonzera iye chakudya cholemekezeka

33:32

يَٰنِسَآءَ ٱلنَّبِيِّ لَسۡتُنَّ كَأَحَدٍ مِّنَ ٱلنِّسَآءِ إِنِ ٱتَّقَيۡتُنَّۚ فَلَا تَخۡضَعۡنَ بِٱلۡقَوۡلِ فَيَطۡمَعَ ٱلَّذِي فِي قَلۡبِهِۦ مَرَضٌ وَقُلۡنَ قَوۡلًا مَّعۡرُوفًا

Oh inu akazi a Mtumwi! Inu simuli akazi wamba. Ngati inu mumaopa Mulungu, muziwayankhula mawu okoma chifukwa mwina anthu amene mu mtima mwawo muli matenda akhoza kuyamba kukusirirani. Koma yankhulani mawu abwino

33:33

وَقَرۡنَ فِي بُيُوتِكُنَّ وَلَا تَبَرَّجۡنَ تَبَرُّجَ ٱلۡجَٰهِلِيَّةِ ٱلۡأُولَىٰۖ وَأَقِمۡنَ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتِينَ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَطِعۡنَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥٓۚ إِنَّمَا يُرِيدُ ٱللَّهُ لِيُذۡهِبَ عَنكُمُ ٱلرِّجۡسَ أَهۡلَ ٱلۡبَيۡتِ وَيُطَهِّرَكُمۡ تَطۡهِيرًا

Ndipo khalani mwakachetechete m’nyumba zanu ndipo musachite zinthu zoipa zoti muonekere poyera monga mmene amachitira anthu nthawi yaumbuli. Ndipo pitirizani kupemphera, perekani msonkho wothandiza anthu osauka ndipo muzimvera Mulungu ndi Mtumwi wake yemwe. Ndipo Mulungu angofuna kuchotsa uve umene uli mwa inu anthu a pabanja lake, ndikukuyeretsani inu

33:34

وَٱذۡكُرۡنَ مَا يُتۡلَىٰ فِي بُيُوتِكُنَّ مِنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ وَٱلۡحِكۡمَةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ لَطِيفًا خَبِيرًا

Ndipo kumbukirani chimene chaphunzitsidwa kwa inu m’nyumba mwanu cha zizindikiro za Mulungu ndi luntha lake. Chifukwa Mulungu ndiye mwini chifundo ndipo amadziwa chilichonse

33:35

إِنَّ ٱلۡمُسۡلِمِينَ وَٱلۡمُسۡلِمَٰتِ وَٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ وَٱلۡقَٰنِتِينَ وَٱلۡقَٰنِتَٰتِ وَٱلصَّٰدِقِينَ وَٱلصَّٰدِقَٰتِ وَٱلصَّٰبِرِينَ وَٱلصَّٰبِرَٰتِ وَٱلۡخَٰشِعِينَ وَٱلۡخَٰشِعَٰتِ وَٱلۡمُتَصَدِّقِينَ وَٱلۡمُتَصَدِّقَٰتِ وَٱلصَّٰٓئِمِينَ وَٱلصَّٰٓئِمَٰتِ وَٱلۡحَٰفِظِينَ فُرُوجَهُمۡ وَٱلۡحَٰفِظَٰتِ وَٱلذَّٰكِرِينَ ٱللَّهَ كَثِيرًا وَٱلذَّٰكِرَٰتِ أَعَدَّ ٱللَّهُ لَهُم مَّغۡفِرَةً وَأَجۡرًا عَظِيمًا

Ndithudi a Chisilamu amene amakhulupirira ndi amuna ndi akazi okhulupirira, amuna ndi akazi a chilungamo, amuna ndi akazi opirira, amuna ndi akazi ofatsa, amuna ndi akazi othandiza osauka, amuna ndi akazi osala, ndi amuna ndi akazi osachita chiwerewere ndi amuna ndi akazi amene amakumbukira Mulungu kwambiri; kwa anthu onse otere, Mulungu wawakonzera chikhululukiro ndi mphotho yaikulu

33:36

وَمَا كَانَ لِمُؤۡمِنٍ وَلَا مُؤۡمِنَةٍ إِذَا قَضَى ٱللَّهُ وَرَسُولُهُۥٓ أَمۡرًا أَن يَكُونَ لَهُمُ ٱلۡخِيَرَةُ مِنۡ أَمۡرِهِمۡۗ وَمَن يَعۡصِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ فَقَدۡ ضَلَّ ضَلَٰلًا مُّبِينًا

Si koyenera kwa munthu wokhulupirira wamwamuna kapena wamkazi kuti pamene nkhani yalamulidwa ndi Mulungu ndi Mtumwi wake, kuti anene china chilichonse pa chiweruzo cha nkhaniyo. Ngati wina samvera Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, iye ali wosochera moonekeratu

33:37

وَإِذۡ تَقُولُ لِلَّذِيٓ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِ وَأَنۡعَمۡتَ عَلَيۡهِ أَمۡسِكۡ عَلَيۡكَ زَوۡجَكَ وَٱتَّقِ ٱللَّهَ وَتُخۡفِي فِي نَفۡسِكَ مَا ٱللَّهُ مُبۡدِيهِ وَتَخۡشَى ٱلنَّاسَ وَٱللَّهُ أَحَقُّ أَن تَخۡشَىٰهُۖ فَلَمَّا قَضَىٰ زَيۡدٌ مِّنۡهَا وَطَرًا زَوَّجۡنَٰكَهَا لِكَيۡ لَا يَكُونَ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ حَرَجٌ فِيٓ أَزۡوَٰجِ أَدۡعِيَآئِهِمۡ إِذَا قَضَوۡاْ مِنۡهُنَّ وَطَرًاۚ وَكَانَ أَمۡرُ ٱللَّهِ مَفۡعُولًا

Ndi pamene iwe udamuuza wina amene adalandira chisomo cha Mulungu ndi chifundo chake kuti, “Musunge mkazi wako ndipo uope Mulungu.” Ndipo iwe udabisa mu mtima mwako zimene Mulungu akadaulula ndipo iwe udaopaanthupamenekunalikoyenerakutiuziopaMulungu. Ndipo pamene Zaid adamusudzula iye, tidamukwatitsa iye kwa iwe ndi cholinga chakuti kutsogolo kusadzakhale vuto kwa anthu okhulupirira pa nkhani ya ukwati wokhudzana ndi ana owapeza pamene iwo asudzulana. Ulamuliro wa Mulungu uyenera kukwaniritsidwa

33:38

مَّا كَانَ عَلَى ٱلنَّبِيِّ مِنۡ حَرَجٍ فِيمَا فَرَضَ ٱللَّهُ لَهُۥۖ سُنَّةَ ٱللَّهِ فِي ٱلَّذِينَ خَلَوۡاْ مِن قَبۡلُۚ وَكَانَ أَمۡرُ ٱللَّهِ قَدَرًا مَّقۡدُورًا

Palibe vuto kwa Mtumwi pa zimene Mulungu wamupatsa ngati udindo wake. Chidali chizolowezi cha Mulungu kwa anthu amene adalipo kale. Ndipo ulamuliro wa Mulungu ndi wokhazikika

33:39

ٱلَّذِينَ يُبَلِّغُونَ رِسَٰلَٰتِ ٱللَّهِ وَيَخۡشَوۡنَهُۥ وَلَا يَخۡشَوۡنَ أَحَدًا إِلَّا ٱللَّهَۗ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ حَسِيبًا

Iwo amene amalalikira uthenga wa Mulungu ndipo amene amamuopa Iye, iwo saopa wina aliyense koma Mulungu ndipo Mulungu ndi wokwanira kubwezera

33:40

مَّا كَانَ مُحَمَّدٌ أَبَآ أَحَدٍ مِّن رِّجَالِكُمۡ وَلَٰكِن رَّسُولَ ٱللَّهِ وَخَاتَمَ ٱلنَّبِيِّـۧنَۗ وَكَانَ ٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمًا

Muhammad si atate wa wina aliyense wa inu koma iye ndi Mthenga wa Mulungu ndi womaliza wa Atumwi a Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse

33:41

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱذۡكُرُواْ ٱللَّهَ ذِكۡرًا كَثِيرًا

oh inu anthu okhulupirira! Kumbukirani Mulungu ndipo muzimukumbukira pafupipafupi

33:42

وَسَبِّحُوهُ بُكۡرَةً وَأَصِيلًا

Ndipo muyamikeni m’mawa ndi madzulo aliwonse

33:43

هُوَ ٱلَّذِي يُصَلِّي عَلَيۡكُمۡ وَمَلَٰٓئِكَتُهُۥ لِيُخۡرِجَكُم مِّنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِۚ وَكَانَ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ رَحِيمًا

Ndiye amene amapereka madalitso ake pa inu ndipo angelo ake amachita chimodzimodzi kuti Iye akhoza kukuchotsani inu ku mdima kupita kowala. Ndipo Iye ndi wachifundo kwa okhulupirira

33:44

تَحِيَّتُهُمۡ يَوۡمَ يَلۡقَوۡنَهُۥ سَلَٰمٌۚ وَأَعَدَّ لَهُمۡ أَجۡرًا كَرِيمًا

Kulonjerana kwawo pa tsiku limene adzakumana naye kudzakhala adzati,“Mtendere”. Ndipo Iye wawakonzera mphotho yolemekezeka

33:45

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ إِنَّآ أَرۡسَلۡنَٰكَ شَٰهِدًا وَمُبَشِّرًا وَنَذِيرًا

Oh iwe Mtumwi! Ndithudi takutumiza iwe ngati mboni ndi wobweretsa nkhani yabwino ndi wochenjeza

33:46

وَدَاعِيًا إِلَى ٱللَّهِ بِإِذۡنِهِۦ وَسِرَاجًا مُّنِيرًا

Ngati munthu woitana anthu kuti adze kwa Mulungu ndi chilolezo chake ndiponso ngati Muuni

33:47

وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ بِأَنَّ لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ فَضۡلًا كَبِيرًا

Kotero auze nkhani yabwino anthu okhulupirira kuti adzalandira mphatso yaikulu kuchokera kwa Mulungu

33:48

وَلَا تُطِعِ ٱلۡكَٰفِرِينَ وَٱلۡمُنَٰفِقِينَ وَدَعۡ أَذَىٰهُمۡ وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلًا

Ndipo usamvere zilakolako za anthu osakhulupirira ndi za anthu a chinyengo. Usalabadire zonena zawo koma ika chikhulupiriro chako mwa Mulungu. Mulungu ndi wokwana kukhala Mtetezi

33:49

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا نَكَحۡتُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ ثُمَّ طَلَّقۡتُمُوهُنَّ مِن قَبۡلِ أَن تَمَسُّوهُنَّ فَمَا لَكُمۡ عَلَيۡهِنَّ مِنۡ عِدَّةٍ تَعۡتَدُّونَهَاۖ فَمَتِّعُوهُنَّ وَسَرِّحُوهُنَّ سَرَاحًا جَمِيلًا

Oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukwatira akazi okhulupirira ndipo muwasudzula musanalowane nawo, palibe nthawi yoyembekezera pakhomo panu. Kotero asanachoke apatseni mphatso yawo ndipo alekeni kuti achoke mwaubwino

33:50

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ إِنَّآ أَحۡلَلۡنَا لَكَ أَزۡوَٰجَكَ ٱلَّٰتِيٓ ءَاتَيۡتَ أُجُورَهُنَّ وَمَا مَلَكَتۡ يَمِينُكَ مِمَّآ أَفَآءَ ٱللَّهُ عَلَيۡكَ وَبَنَاتِ عَمِّكَ وَبَنَاتِ عَمَّٰتِكَ وَبَنَاتِ خَالِكَ وَبَنَاتِ خَٰلَٰتِكَ ٱلَّٰتِي هَاجَرۡنَ مَعَكَ وَٱمۡرَأَةً مُّؤۡمِنَةً إِن وَهَبَتۡ نَفۡسَهَا لِلنَّبِيِّ إِنۡ أَرَادَ ٱلنَّبِيُّ أَن يَسۡتَنكِحَهَا خَالِصَةً لَّكَ مِن دُونِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۗ قَدۡ عَلِمۡنَا مَا فَرَضۡنَا عَلَيۡهِمۡ فِيٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ وَمَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ لِكَيۡلَا يَكُونَ عَلَيۡكَ حَرَجٌۗ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا

Oh iwe Mtumwi! Takulola kukhala ndi akazi onse amene iwe wapereka chiongo chawo ndi iwo amene ndi akapolo ako kuchokera kugulu limene lidagwidwa pankhondo ndipo Mulungu wakupatsa iwe; ana a akazi a atsibweni ndi azakhali ako, a kuchimuna kapena kuchikazi amene adachoka pamodzi ndi iwe. Ndiponso mkazi wina aliyense wokhulupirira amene adzipereka yekha kwa Mtumwi ngati Mtumwi afuna kumukwatira iye. Chilolezo ichi ndi cha iwe wekha osati cha anthu onse okhulupirira. Ife tikudziwa chimene tawasankhira iwo zokhudza akazi awo ndi akapolo amene iwo amasunga, ndi cholinga chakuti pasadzakhale vuto kwa iwe. Ndipo Mulungu amakhululukira nthawi zonse ndipo ndiye Mwini chisoni chosatha

33:51

تُرۡجِي مَن تَشَآءُ مِنۡهُنَّ وَتُـٔۡوِيٓ إِلَيۡكَ مَن تَشَآءُۖ وَمَنِ ٱبۡتَغَيۡتَ مِمَّنۡ عَزَلۡتَ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكَۚ ذَٰلِكَ أَدۡنَىٰٓ أَن تَقَرَّ أَعۡيُنُهُنَّ وَلَا يَحۡزَنَّ وَيَرۡضَيۡنَ بِمَآ ءَاتَيۡتَهُنَّ كُلُّهُنَّۚ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا فِي قُلُوبِكُمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَلِيمًا

Iwe ukhoza kumusiya aliyense wa iwo amene wafuna ndipo ukhoza kutenga aliyense wa iwo amene wafuna ndi aliyense wa iwo amene udawasiya pa kanthawi kochepa. Palibe cholakwa kwa iwe pochita izi kuti maso awo azizire ndiponso onse asadandaule ndi zimene uwapatsa. Ndipo Mulungu amadziwa zinthu zonse zomwe zili m’mitima mwanu. Mulungu amadziwa zonse ndiponso ndi wopirira

33:52

لَّا يَحِلُّ لَكَ ٱلنِّسَآءُ مِنۢ بَعۡدُ وَلَآ أَن تَبَدَّلَ بِهِنَّ مِنۡ أَزۡوَٰجٍ وَلَوۡ أَعۡجَبَكَ حُسۡنُهُنَّ إِلَّا مَا مَلَكَتۡ يَمِينُكَۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ رَّقِيبًا

Iwe siuloledwa kukwatiranso akazi ena pambuyo pa awa kapena kuwasintha kuti upeze akazi ena ngakhale kuti kukongola kwawo kuli kukusangalatsa kupatula akapolo amene uli nawo. Ndipo Mulungu amayang’anitsitsa pa zinthu zonse

33:53

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَدۡخُلُواْ بُيُوتَ ٱلنَّبِيِّ إِلَّآ أَن يُؤۡذَنَ لَكُمۡ إِلَىٰ طَعَامٍ غَيۡرَ نَٰظِرِينَ إِنَىٰهُ وَلَٰكِنۡ إِذَا دُعِيتُمۡ فَٱدۡخُلُواْ فَإِذَا طَعِمۡتُمۡ فَٱنتَشِرُواْ وَلَا مُسۡتَـٔۡنِسِينَ لِحَدِيثٍۚ إِنَّ ذَٰلِكُمۡ كَانَ يُؤۡذِي ٱلنَّبِيَّ فَيَسۡتَحۡيِۦ مِنكُمۡۖ وَٱللَّهُ لَا يَسۡتَحۡيِۦ مِنَ ٱلۡحَقِّۚ وَإِذَا سَأَلۡتُمُوهُنَّ مَتَٰعًا فَسۡـَٔلُوهُنَّ مِن وَرَآءِ حِجَابٍۚ ذَٰلِكُمۡ أَطۡهَرُ لِقُلُوبِكُمۡ وَقُلُوبِهِنَّۚ وَمَا كَانَ لَكُمۡ أَن تُؤۡذُواْ رَسُولَ ٱللَّهِ وَلَآ أَن تَنكِحُوٓاْ أَزۡوَٰجَهُۥ مِنۢ بَعۡدِهِۦٓ أَبَدًاۚ إِنَّ ذَٰلِكُمۡ كَانَ عِندَ ٱللَّهِ عَظِيمًا

Oh inu anthu okhulupirira! Musamalowe m’nyumba za Mtumwi pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kuti mukadye chakudya osati kukadikira chakudya mpaka pamene chiphikidwa. Koma pamene mwaitanidwa lowani ndipo pamene mumaliza kudya chokani. Musayembekeze kumvetsera nkhani. Ndithudi zimenezi zimamupatsa Mtumwi mavuto koma iye amachita nanu manyazi pamene Mulungu sachita manyazi kuulula choonadi. Ndipo ngati inu mufunsa katundu wina aliyense, funsani kuchokera ku malo osaonekera. Ichi ndi chabwino kwa inu ndiponso kwa iwo ndipo si koyenera kuti inu mumupatse mavuto Mtumwi wa Mulungu kapena kuti inu mukwatire akazi ake iye atawasiya. Ndithudi chimenechi ndi chinthu choipa pamaso pa Mulungu

33:54

إِن تُبۡدُواْ شَيۡـًٔا أَوۡ تُخۡفُوهُ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمًا

Ngati inu muchita chinthu poyera kapena mobisa, ndithudi, dziwani kuti Mulungu amadziwa zinthu zonse

33:55

لَّا جُنَاحَ عَلَيۡهِنَّ فِيٓ ءَابَآئِهِنَّ وَلَآ أَبۡنَآئِهِنَّ وَلَآ إِخۡوَٰنِهِنَّ وَلَآ أَبۡنَآءِ إِخۡوَٰنِهِنَّ وَلَآ أَبۡنَآءِ أَخَوَٰتِهِنَّ وَلَا نِسَآئِهِنَّ وَلَا مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُنَّۗ وَٱتَّقِينَ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ شَهِيدًا

Palibe cholakwa kwa iwo pa nkhani zokhudza atate awo kapena ana awo kapena abale awo kapena ana a abale awo kapena akazi awo kapena atumiki awo. Ndipo opani Mulungu. Ndithudi, Mulungu ndi mboni pa chinthu china chilichonse

33:56

إِنَّ ٱللَّهَ وَمَلَٰٓئِكَتَهُۥ يُصَلُّونَ عَلَى ٱلنَّبِيِّۚ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ صَلُّواْ عَلَيۡهِ وَسَلِّمُواْ تَسۡلِيمًا

Ndithudi Mulungu ndi angelo amamudalitsa Mtumwi wake. oh inu anthu okhulupirira! Pemphani madalitso kuti adze pa iye ndipo mulonjereni ndi malonje abwino

33:57

إِنَّ ٱلَّذِينَ يُؤۡذُونَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ لَعَنَهُمُ ٱللَّهُ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِ وَأَعَدَّ لَهُمۡ عَذَابًا مُّهِينًا

Ndithudi iwo amene amanena zinthu zoipa zokhudza Mulungu ndi Mtumwi wake, Mulungu anawatemberera iwo m’moyo uno ndiponso adzawatemberera m’moyo umene uli nkudza ndipo wawakonzera chilango chochititsa manyazi

33:58

وَٱلَّذِينَ يُؤۡذُونَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ بِغَيۡرِ مَا ٱكۡتَسَبُواْ فَقَدِ ٱحۡتَمَلُواْ بُهۡتَٰنًا وَإِثۡمًا مُّبِينًا

Ndipo iwo amene amayankhula zinthu zoipa zokhudza anthu a amuna okhulupirira ndi anthu a akazi okhulupirira, pamene iwo sadalakwe, iwowo ali pamlandu wonamizira ndi wochita tchimo looneka

33:59

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ قُل لِّأَزۡوَٰجِكَ وَبَنَاتِكَ وَنِسَآءِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ يُدۡنِينَ عَلَيۡهِنَّ مِن جَلَٰبِيبِهِنَّۚ ذَٰلِكَ أَدۡنَىٰٓ أَن يُعۡرَفۡنَ فَلَا يُؤۡذَيۡنَۗ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا

Oh iwe Mtumwi! Auze akazi ako ndi ana ako, akazi ndi akazi a anthu okhulupirira kuti azivala moyenera zovala zawo zapamwamba zoonjezera pa zovala zomwe avala mkati. Zimenezi zidzakhala zabwino kuti akhoza kudziwika nazo ndipo kotero iwo sadzavutitsidwa ayi. Ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha

33:60

لَّئِن لَّمۡ يَنتَهِ ٱلۡمُنَٰفِقُونَ وَٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ وَٱلۡمُرۡجِفُونَ فِي ٱلۡمَدِينَةِ لَنُغۡرِيَنَّكَ بِهِمۡ ثُمَّ لَا يُجَاوِرُونَكَ فِيهَآ إِلَّا قَلِيلًا

Ngati anthu achinyengo pamodzi ndi iwo amene m’mitima mwawo muli matenda ndiponso anthu amene amayambitsa chisokonezo mu mzinda, saleka mchitidwe oterewu,** ndithudi, Ife tidzalimbana nawo ndipo iwo sadzakhala pafupi ndi inu kupatula nthawi yochepa

33:61

مَّلۡعُونِينَۖ أَيۡنَمَا ثُقِفُوٓاْ أُخِذُواْ وَقُتِّلُواْ تَقۡتِيلًا

Iwo ndi otembereredwa. Paliponse pamene adzapezeka iwo adzagwidwa ndi kuphedwa mwankhanza

33:62

سُنَّةَ ٱللَّهِ فِي ٱلَّذِينَ خَلَوۡاْ مِن قَبۡلُۖ وَلَن تَجِدَ لِسُنَّةِ ٱللَّهِ تَبۡدِيلًا

Amenewa ndiwo adali machitidwe a Mulungu kwa anthu akale ndipo inu simudzapeza chosintha m’machitidwe a Mulungu

33:63

يَسۡـَٔلُكَ ٱلنَّاسُ عَنِ ٱلسَّاعَةِۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ ٱللَّهِۚ وَمَا يُدۡرِيكَ لَعَلَّ ٱلسَّاعَةَ تَكُونُ قَرِيبًا

Anthuamakufunsanizaola. Nenakuti,“Mulunguyekha ndiye amene amadziwa za ilo. Kodi chidzakudziwitsani ndi chiyani za olali? Mwinatu lili pafupi!”

33:64

إِنَّ ٱللَّهَ لَعَنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ وَأَعَدَّ لَهُمۡ سَعِيرًا

Ndithudi Mulungu watemberera anthu osakhulupirira ndipo wawakonzera moto woyaka

33:65

خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًاۖ لَّا يَجِدُونَ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا

Adzakhalamo mpaka kalekale ndipo iwo sadzapeza mtetezi kapena wowathandiza

33:66

يَوۡمَ تُقَلَّبُ وُجُوهُهُمۡ فِي ٱلنَّارِ يَقُولُونَ يَٰلَيۡتَنَآ أَطَعۡنَا ٱللَّهَ وَأَطَعۡنَا ٱلرَّسُولَا۠

Pa tsiku limene nkhope zawo zidzalangizidwe moto, iwo adzati, “Kukadakhala bwino kuti tikadamvera Mulungu ndi kumvera Mtumwi”

33:67

وَقَالُواْ رَبَّنَآ إِنَّآ أَطَعۡنَا سَادَتَنَا وَكُبَرَآءَنَا فَأَضَلُّونَا ٱلسَّبِيلَا۠

Ndipo iwo adzati, “Oh Ambuye wathu! Ndithudi ife tidamvera atsogoleri athu ndi akuluakulu athu kotero iwo adatisocheretsa.”

33:68

رَبَّنَآ ءَاتِهِمۡ ضِعۡفَيۡنِ مِنَ ٱلۡعَذَابِ وَٱلۡعَنۡهُمۡ لَعۡنًا كَبِيرًا

“oh Ambuye wathu! Apatseni iwo chilango chowirikiza ndipo atemberereni iwo ndi matemberero ochuluka.”

33:69

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَكُونُواْ كَٱلَّذِينَ ءَاذَوۡاْ مُوسَىٰ فَبَرَّأَهُ ٱللَّهُ مِمَّا قَالُواْۚ وَكَانَ عِندَ ٱللَّهِ وَجِيهًا

oh inu anthu okhulupirira! Musakhale ngati anthu amene adayankhula zinthu zoipa zokhudza Mose. Koma Mulungu adatsutsa zonse zimene anali kunena za Mose. Ndipo iye anali wolemekezeka kwa Mulungu

33:70

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَقُولُواْ قَوۡلًا سَدِيدًا

oh inu anthu okhulupirira! Opani Mulungu ndipo muzinena mawu abwino

33:71

يُصۡلِحۡ لَكُمۡ أَعۡمَٰلَكُمۡ وَيَغۡفِرۡ لَكُمۡ ذُنُوبَكُمۡۗ وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ فَقَدۡ فَازَ فَوۡزًا عَظِيمًا

Iye adzasunga ntchito zanu pamalo abwino ndi kukukhululukirani machimo anu. Ndipo aliyense amene amamvera Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, iyeyo wapeza chinthu chopambana

33:72

إِنَّا عَرَضۡنَا ٱلۡأَمَانَةَ عَلَى ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَٱلۡجِبَالِ فَأَبَيۡنَ أَن يَحۡمِلۡنَهَا وَأَشۡفَقۡنَ مِنۡهَا وَحَمَلَهَا ٱلۡإِنسَٰنُۖ إِنَّهُۥ كَانَ ظَلُومًا جَهُولًا

Ndithudi Ife tidapereka udindo ndi chikhulupiriro kumwamba, pa dziko ndi pa mapiri koma zonse zidakana kulandira ndipo adauopa. Koma munthu adauvomera. Ndithudi iye ndi wosalungama ndiponso mbuli

33:73

لِّيُعَذِّبَ ٱللَّهُ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ وَٱلۡمُنَٰفِقَٰتِ وَٱلۡمُشۡرِكِينَ وَٱلۡمُشۡرِكَٰتِ وَيَتُوبَ ٱللَّهُ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۗ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمَۢا

Motero Mulungu adzalanga amuna ndi akazi a chinyengo. Ndiponso amuna ndi akazi opembedza mafano. Ndipo Mulungu adzakhululukira anthu onse okhululupirira, amuna ndi akazi. Mulungu ndi wokhululukira ndiponso mwini chisoni chosatha

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.