بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
90:1لَآ أُقۡسِمُ بِهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ
Ine ndili kulumbira pali Mzinda uwu
90:2وَأَنتَ حِلُّۢ بِهَٰذَا ٱلۡبَلَدِ
Ndipo iwe uli ndi ufulu mu Mzinda uwu
90:3وَوَالِدٍ وَمَا وَلَدَ
Ndi pali wobereka ndi chimene adabereka
90:4لَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ فِي كَبَدٍ
Ndithudi Ife tidamulenga munthu m’mavuto
90:5أَيَحۡسَبُ أَن لَّن يَقۡدِرَ عَلَيۡهِ أَحَدٌ
Kodi amaganiza kuti palibe wina aliyense amene ali ndi mphamvu pa iye
90:6يَقُولُ أَهۡلَكۡتُ مَالًا لُّبَدًا
Iye amanena monyada kuti: “Ine Al-Shams 653 ndaononga chuma chambiri.”
90:7أَيَحۡسَبُ أَن لَّمۡ يَرَهُۥٓ أَحَدٌ
Kodi iye amaganiza kuti palibe wina amene ali kumuona
90:8أَلَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ عَيۡنَيۡنِ
Kodi Ife sitidamupatse maso awiri
90:9وَلِسَانًا وَشَفَتَيۡنِ
Ndi lirime ndi milomo iwiri
90:10وَهَدَيۡنَٰهُ ٱلنَّجۡدَيۡنِ
Ndi kumulangiza iye njira ziwiri
90:11فَلَا ٱقۡتَحَمَ ٱلۡعَقَبَةَ
Koma sayerekeza kutsata njira yozyolika
90:12وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡعَقَبَةُ
Kodi chidzakuuza ndi chiani za njira yozyolika
90:13فَكُّ رَقَبَةٍ
Ndi kumasula kapolo
90:14أَوۡ إِطۡعَٰمٌ فِي يَوۡمٍ ذِي مَسۡغَبَةٍ
Kapena kupereka chakudya nthawi ya njala
90:15يَتِيمًا ذَا مَقۡرَبَةٍ
Kwa wamasiye amene ndi wachinansi
90:16أَوۡ مِسۡكِينًا ذَا مَتۡرَبَةٍ
Kapena munthu wosauka, wofuna chithandizo
90:17ثُمَّ كَانَ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلصَّبۡرِ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلۡمَرۡحَمَةِ
Ndipo iye anakhala mmodzi wa anthu amene akhulupirira, ndipo analangizana wina ndi mzake kupilira, kumva chisoni ndi kuonetsa chifundo
90:18أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ
Iwo ndiwo amene adzakhala kudzanja lamanja
90:19وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا هُمۡ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ
Koma iwo amene anakana chivumbulutso chathu, adzaima ku dzanja lamanzere
90:20عَلَيۡهِمۡ نَارٌ مُّؤۡصَدَةُۢ
Ndipo moto wa ku Gahena udzawakuta iwo
Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.