Surah 89 · 30 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Fajr in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

89:1

وَٱلۡفَجۡرِ

Pali m’mbandakucha

89:2

وَلَيَالٍ عَشۡرٍ

Ndi pali usiku khumi

89:3

وَٱلشَّفۡعِ وَٱلۡوَتۡرِ

Pali chofanana ndi chosiyana

89:4

وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَسۡرِ

Pali usiku pamene uli nkutha

89:5

هَلۡ فِي ذَٰلِكَ قَسَمٌ لِّذِي حِجۡرٍ

Ndithudi m’menemu muli umboni wokwanira kwa anthu a nzeru

89:6

أَلَمۡ تَرَ كَيۡفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِعَادٍ

Kodi iwe siudaone mmene Ambuye wako adakhaulitsira anthu a Aad

89:7

إِرَمَ ذَاتِ ٱلۡعِمَادِ

Amene anali atali atali ngati nsanamila zitali zitali

89:8

ٱلَّتِي لَمۡ يُخۡلَقۡ مِثۡلُهَا فِي ٱلۡبِلَٰدِ

wolingana nawo amene sanalengedwepo padziko

89:9

وَثَمُودَ ٱلَّذِينَ جَابُواْ ٱلصَّخۡرَ بِٱلۡوَادِ

Ndi anthu a Thamoud, amene ankakumba nyumba zawo m’miyala ya m’dambo

89:10

وَفِرۡعَوۡنَ ذِي ٱلۡأَوۡتَادِ

Ndi Farao, amene anali ndi zichiri

89:11

ٱلَّذِينَ طَغَوۡاْ فِي ٱلۡبِلَٰدِ

Amene anali kuphwanya malamulo paliponse m’dziko

89:12

فَأَكۡثَرُواْ فِيهَا ٱلۡفَسَادَ

Ndipo adachulukitsa chisokonezo

89:13

فَصَبَّ عَلَيۡهِمۡ رَبُّكَ سَوۡطَ عَذَابٍ

Motero Ambuye wako adabweretsa chilango chosiyana siyana chowawa pa iwo

89:14

إِنَّ رَبَّكَ لَبِٱلۡمِرۡصَادِ

Ndithudi Ambuye wako amaona

89:15

فَأَمَّا ٱلۡإِنسَٰنُ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ رَبُّهُۥ فَأَكۡرَمَهُۥ وَنَعَّمَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَكۡرَمَنِ

Ndipo nthawi zonse munthu, pamene Ambuye wake amuyesa pomukweza ndi kumuonetsera chifundo chake, iye amati: “Ambuye wanga wandilemekeza ine.”

89:16

وَأَمَّآ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ فَقَدَرَ عَلَيۡهِ رِزۡقَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَهَٰنَنِ

Koma akamuyesa pomumana zinthu, iye amati: “Ambuye wanga ali kundizunza ine.”

89:17

كـَلَّاۖ بَل لَّا تُكۡرِمُونَ ٱلۡيَتِيمَ

Iyayi! Koma inu simuonetsa chifundo kwa ana a masiye

89:18

وَلَا تَحَٰٓضُّونَ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ

Ndi kuuzana kuti mudzidyetsa anthu osauka

89:19

وَتَأۡكُلُونَ ٱلتُّرَاثَ أَكۡلًا لَّمًّا

Inu mumalanda chuma cha anthu opanda mphamvu chifukwa cha umbombo

89:20

وَتُحِبُّونَ ٱلۡمَالَ حُبًّا جَمًّا

Ndipo mumakonda chuma ndi mitima yanu yonse

89:21

كـَلَّآۖ إِذَا دُكَّتِ ٱلۡأَرۡضُ دَكًّا دَكًّا

Iyayi! Koma pamene dziko lidzasinjidwa kukhala ufa

89:22

وَجَآءَ رَبُّكَ وَٱلۡمَلَكُ صَفًّا صَفًّا

Ndipo Ambuye wanu adzadza pamodzi ndi angelo ali pa mizere

89:23

وَجِاْيٓءَ يَوۡمَئِذِۭ بِجَهَنَّمَۚ يَوۡمَئِذٍ يَتَذَكَّرُ ٱلۡإِنسَٰنُ وَأَنَّىٰ لَهُ ٱلذِّكۡرَىٰ

Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi patsikuli. Ndipo patsikuli munthu adzakumbukira. Koma, kodi chikumbumtima chake chidzamuthandiza motani

89:24

يَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي قَدَّمۡتُ لِحَيَاتِي

Iye adzanena kuti: “Kalanga ine! Ndikanakhala ndinali kuchita zabwino pamene ndinali ndi moyo.”

89:25

فَيَوۡمَئِذٍ لَّا يُعَذِّبُ عَذَابَهُۥٓ أَحَدٌ

Motero patsikuli, palibe wina amene adzalanga monga momwe Iye adzalangire

89:26

وَلَا يُوثِقُ وَثَاقَهُۥٓ أَحَدٌ

Ndipo palibe wina amene adzamanga monga ngati momwe Iye adzamangire

89:27

يَٰٓأَيَّتُهَا ٱلنَّفۡسُ ٱلۡمُطۡمَئِنَّةُ

oh! Iwe wokhutitsidwa

89:28

ٱرۡجِعِيٓ إِلَىٰ رَبِّكِ رَاضِيَةً مَّرۡضِيَّةً

Bwerera kwa Ambuye wako mosangalala ndi Iye, ndi Iye mosangalala ndi iwe

89:29

فَٱدۡخُلِي فِي عِبَٰدِي

Lowa m’gulu la akapolo anga wolemekezeka

89:30

وَٱدۡخُلِي جَنَّتِي

Ndipo lowa mu Paradiso yanga

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.