Surah 45 · 37 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Jathiyah in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

45:1

حمٓ

Ha Mim

45:2

تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ

Chivumbulutso cha Buku ndi chochokera kwa Mulungu, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru

45:3

إِنَّ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ لَأٓيَٰتٍ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndithudi kumwamba ndi dziko lapansi kuli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

45:4

وَفِي خَلۡقِكُمۡ وَمَا يَبُثُّ مِن دَآبَّةٍ ءَايَٰتٌ لِّقَوۡمٍ يُوقِنُونَ

M’chilengedwe chanu nyama zimapezeka paliponse pa dziko lapansi ndipo ndi zizindikiro kwa iwo amene ali okhulupirira kwenikweni

45:5

وَٱخۡتِلَٰفِ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مِن رِّزۡقٍ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَا وَتَصۡرِيفِ ٱلرِّيَٰحِ ءَايَٰتٌ لِّقَوۡمٍ يَعۡقِلُونَ

Ndi m’kasinthidwe ka usiku ndi usana ndi m’chakudya chimene amatumiza kuchokera ku mitambo ndipo amapereka moyo ku nthaka imene idali yakufa ndipo m’kasinthidwe ka mphepo, muli zizindikiro kwa anthu ozindikira

45:6

تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱللَّهِ نَتۡلُوهَا عَلَيۡكَ بِٱلۡحَقِّۖ فَبِأَيِّ حَدِيثِۭ بَعۡدَ ٱللَّهِ وَءَايَٰتِهِۦ يُؤۡمِنُونَ

Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Mulungu chimene tili kulakatula kwa iwe mwachoonadi. Nanga ndi uthenga uti wa Mulungu ndi chivumbulutso chake chiti chomwe iwo akhoza kukhulupirira

45:7

وَيۡلٌ لِّكُلِّ أَفَّاكٍ أَثِيمٍ

Tsoka kwa wochimwa aliyense wabodza

45:8

يَسۡمَعُ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ثُمَّ يُصِرُّ مُسۡتَكۡبِرًا كَأَن لَّمۡ يَسۡمَعۡهَاۖ فَبَشِّرۡهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ

Amene amamva mawu a Mulungu amene ali kunenedwa kwa iye ndipo amapitirizabe kunyada ngati iye sanamve. Motero muuze iye za chilango chowawa

45:9

وَإِذَا عَلِمَ مِنۡ ءَايَٰتِنَا شَيۡـًٔا ٱتَّخَذَهَا هُزُوًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٌ مُّهِينٌ

Ndipo pamene iye akamva mawu a Mulungu, amawasandutsa kukhala masewera. Ndipo kwa otere kudzakhala chilango chochititsa manyazi

45:10

مِّن وَرَآئِهِمۡ جَهَنَّمُۖ وَلَا يُغۡنِي عَنۡهُم مَّا كَسَبُواْ شَيۡـًٔا وَلَا مَا ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡلِيَآءَۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٌ

Kutsogolo kwawo kuli Gahena, ndipo sadzapeza phindu lina lililonse pa ntchito zawo kapenakwaiwoameneadawasandutsakukhalawowasamala poonjezera pa Mulungu. Ndipo iwo adzalandira chilango chowawa

45:11

هَٰذَا هُدًىۖ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ لَهُمۡ عَذَابٌ مِّن رِّجۡزٍ أَلِيمٌ

Ichi ndi chilangizo choona. Ndipo iwo amene amakana zizindikiro za Ambuye wawo, adzalandira chilango chapadera chowawa

45:12

ٱللَّهُ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَكُمُ ٱلۡبَحۡرَ لِتَجۡرِيَ ٱلۡفُلۡكُ فِيهِ بِأَمۡرِهِۦ وَلِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Ndi Mulungu amene adachepetsa mphamvu ya nyanja kuti masitima aziyenda mwaulamuliro wake ndipo kuti inu mukhoza kufuna chisomo chake kuti muzimuthokoza

45:13

وَسَخَّرَ لَكُم مَّا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعًا مِّنۡهُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يَتَفَكَّرُونَ

Ndipo Iye adachepetsa mphamvu ya chinthu chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene amaganiza mofatsa

45:14

قُل لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ يَغۡفِرُواْ لِلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ أَيَّامَ ٱللَّهِ لِيَجۡزِيَ قَوۡمَۢا بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Auze iwo amene amakhulupirira kuti akhululukire iwo amene sakhulupirira m’masiku a Mulungu kuti Iye akhoza kulipira anthu chimene amachita

45:15

مَنۡ عَمِلَ صَٰلِحًا فَلِنَفۡسِهِۦۖ وَمَنۡ أَسَآءَ فَعَلَيۡهَاۖ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُمۡ تُرۡجَعُونَ

Aliyense amene amachita zabwino amachitira mzimu wake ndipo aliyense amene amachita zoipa adzilakwira yekha. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu

45:16

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحُكۡمَ وَٱلنُّبُوَّةَ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَفَضَّلۡنَٰهُمۡ عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndithudi Ife tidawapatsa ana a Israyeli Buku ndi luntha lozindikira mawu a Mulungu ndi Utumwi ndipo tidawapatsa zinthu zokoma ndipo tidawakonda iwo kuposa mitundu ina yonse

45:17

وَءَاتَيۡنَٰهُم بَيِّنَٰتٍ مِّنَ ٱلۡأَمۡرِۖ فَمَا ٱخۡتَلَفُوٓاْ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَهُمُ ٱلۡعِلۡمُ بَغۡيَۢا بَيۡنَهُمۡۚ إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ

Ndipo Ife tidawapatsa zizindikiro zooneka za chipembedzo. Ndipo iwo adayamba mipatuko pamene nzeru zidaperekedwa kwa iwo chifukwa cha njiru pakati pawo. Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku lachiweruzo pa nkhani zimene anali kutsutsana

45:18

ثُمَّ جَعَلۡنَٰكَ عَلَىٰ شَرِيعَةٍ مِّنَ ٱلۡأَمۡرِ فَٱتَّبِعۡهَا وَلَا تَتَّبِعۡ أَهۡوَآءَ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo iwe takuika pa njira yoyenera. Motero tsatira yoyenerayo ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene sadziwa chilichonse

45:19

إِنَّهُمۡ لَن يُغۡنُواْ عَنكَ مِنَ ٱللَّهِ شَيۡـًٔاۚ وَإِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ بَعۡضُهُمۡ أَوۡلِيَآءُ بَعۡضٍۖ وَٱللَّهُ وَلِيُّ ٱلۡمُتَّقِينَ

Ndithudi iwo sangakuthandize chilichonse ku mkwiyo wa Mulungu. Ndi anthu oipa okha okha omwe amakhala ngati atetezi a wina ndi mnzake koma Mulungu ndi Mtetezi wa iwo amene amalewa zoipa

45:20

هَٰذَا بَصَٰٓئِرُ لِلنَّاسِ وَهُدًى وَرَحۡمَةٌ لِّقَوۡمٍ يُوقِنُونَ

Uwu ndi umboni womveka kwa anthu ndi langizo ndi chisomo kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro chokhazikika

45:21

أَمۡ حَسِبَ ٱلَّذِينَ ٱجۡتَرَحُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ أَن نَّجۡعَلَهُمۡ كَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَوَآءً مَّحۡيَاهُمۡ وَمَمَاتُهُمۡۚ سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ

Kodi anthu amene amachita zoipa amaganiza kuti Ife tidzawasamala monga mmene tidzasamalire anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino zofanana ndi moyo wawo ndiponso imfa yawo? Iwo amaweruza molakwa

45:22

وَخَلَقَ ٱللَّهُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّ وَلِتُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا كَسَبَتۡ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ

Ndipo Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi kuti mzimu uliwonse ukhoza kupeza dipo lake molingana ndi zimene udachita ndipo palibe amene adzaponderezedwa

45:23

أَفَرَءَيۡتَ مَنِ ٱتَّخَذَ إِلَٰهَهُۥ هَوَىٰهُ وَأَضَلَّهُ ٱللَّهُ عَلَىٰ عِلۡمٍ وَخَتَمَ عَلَىٰ سَمۡعِهِۦ وَقَلۡبِهِۦ وَجَعَلَ عَلَىٰ بَصَرِهِۦ غِشَٰوَةً فَمَن يَهۡدِيهِ مِنۢ بَعۡدِ ٱللَّهِۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ

Kodi wamuona iye amene amasandutsa zilakolako zake kukhala mulungu wake? Mulungu wamusocheretsa iye ndipo wakhazikitsa chophimba m’makutu mwake ndi mu mtima mwake. Ndipo waika chophimba m’maso mwake? Kodi ndani amene akhoza kumutsogolera iye kupatula Mulungu? Kodi tsopano simudzakumbukira

45:24

وَقَالُواْ مَا هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا ٱلدُّنۡيَا نَمُوتُ وَنَحۡيَا وَمَا يُهۡلِكُنَآ إِلَّا ٱلدَّهۡرُۚ وَمَا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِنۡ هُمۡ إِلَّا يَظُنُّونَ

Ndipo iwo amati, “Kulibe china chilichonse kupatula moyo wathu wa pa dziko lapansi. Ife timakhala ndi moyo ndipo timafa ndipo palibe chimene chimationonga ife koma nthawi yokha ndiyo.” Ndipo iwo sadziwa chilichonse cha izo koma amangonena zongoganiza

45:25

وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٍ مَّا كَانَ حُجَّتَهُمۡ إِلَّآ أَن قَالُواْ ٱئۡتُواْ بِـَٔابَآئِنَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Ndipo pamene chivumbulutso chathu chomveka chimanenedwa kwa iwo, mtsutso wawo siukhala wina koma kuti, “Bweretsa makolo athu akale ngati zimene ukunena ndi zoonadi.”

45:26

قُلِ ٱللَّهُ يُحۡيِيكُمۡ ثُمَّ يُمِيتُكُمۡ ثُمَّ يَجۡمَعُكُمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا رَيۡبَ فِيهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Nena: “Mulungu amakupatsani inu moyo, amakuphani ndipo Iye adzakusonkhanitsani pa tsiku la kuuka kwa akufa limene lilibe chikayiko. Koma ambiri sadziwa zimenezi.”

45:27

وَلِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يَوۡمَئِذٍ يَخۡسَرُ ٱلۡمُبۡطِلُونَ

Mulungu! Wake ndi ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo patsiku limene ola lidzadza, onse amene amanenazinthuzabodzaadzatayachilichonse

45:28

وَتَرَىٰ كُلَّ أُمَّةٍ جَاثِيَةًۚ كُلُّ أُمَّةٍ تُدۡعَىٰٓ إِلَىٰ كِتَٰبِهَا ٱلۡيَوۡمَ تُجۡزَوۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Ndipoiwe udzaona mtundu uliwonse utagwada pansi ndipo mtundu uliwonse udzaitanidwa monga mmene zidalembedwera. Lero mudzalipidwa molingana ndi zimene mudachita

45:29

هَٰذَا كِتَٰبُنَا يَنطِقُ عَلَيۡكُم بِٱلۡحَقِّۚ إِنَّا كُنَّا نَسۡتَنسِخُ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Buku lathuli lili kunena za inu mwachilungamo. Ndithudi timalemba zonse zimene mumachita

45:30

فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَيُدۡخِلُهُمۡ رَبُّهُمۡ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡمُبِينُ

Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ambuye wawo adzawalowetsa m’chisomo chake. Kumeneku ndiko kupambana kwenikweni

45:31

وَأَمَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَفَلَمۡ تَكُنۡ ءَايَٰتِي تُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فَٱسۡتَكۡبَرۡتُمۡ وَكُنتُمۡ قَوۡمًا مُّجۡرِمِينَ

Koma iwo amene sadakhulupirire adzauzidwa kuti, “Kodi chivumbulutso changa sichidalakatulidwe kwa inu? Koma inu munali onyada ndipo munali anthu ochita zoipa.”

45:32

وَإِذَا قِيلَ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقٌّ وَٱلسَّاعَةُ لَا رَيۡبَ فِيهَا قُلۡتُم مَّا نَدۡرِي مَا ٱلسَّاعَةُ إِن نَّظُنُّ إِلَّا ظَنًّا وَمَا نَحۡنُ بِمُسۡتَيۡقِنِينَ

Ndipo pamene zidanenedwa kuti, “Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo palibe zokayikitsa za kudza kwa Ola”, inu mudati, “Ife sitidziwa kuti Ola ndi chiyani ndipo ife sitiliganiza kupatula kuti ndi maganizo opanda pake ndipo ife sitilikhulupirira ayi.”

45:33

وَبَدَا لَهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا عَمِلُواْ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ

Ndipozoipazonsezimeneadachitazidaonekerapoyera kwa iwo ndipo zonse zimene anali kunyoza zidzawapeza

45:34

وَقِيلَ ٱلۡيَوۡمَ نَنسَىٰكُمۡ كَمَا نَسِيتُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَا وَمَأۡوَىٰكُمُ ٱلنَّارُ وَمَا لَكُم مِّن نَّٰصِرِينَ

Ndipo kudzanenedwa kuti, “Lero takuiwalani inu monga momwe inu mudaiwalira za tsiku lanuli. Ndipo malo anu okhala ndi ku Moto ndipo kumeneko sikudzakhala wina wokuthandizani.”

45:35

ذَٰلِكُم بِأَنَّكُمُ ٱتَّخَذۡتُمۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ هُزُوًا وَغَرَّتۡكُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَاۚ فَٱلۡيَوۡمَ لَا يُخۡرَجُونَ مِنۡهَا وَلَا هُمۡ يُسۡتَعۡتَبُونَ

“Ichi ndi chifukwa chakuti mudatenga chivumbulutso cha Mulungu ngati chinthu choseweretsa ndipo moyo wa padziko lino lapansi udakunyengani inu.” Motero patsiku limeneli, iwo sadzachotsedwa ndipo sadzaloledwa kukonza zolakwa zawo

45:36

فَلِلَّهِ ٱلۡحَمۡدُ رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَرَبِّ ٱلۡأَرۡضِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Motero kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa Kumwamba ndi Ambuye wa padziko lapansi ndi Ambuye wa zolengedwa zonse

45:37

وَلَهُ ٱلۡكِبۡرِيَآءُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

Ndipo wake ndi Ufumu wakumwamba ndi padziko lapansi ndipo Iye ndi Wopambana ndi Wanzeru zonse

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.