Surah 44 · 59 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Surah Ad-Dukhan in Chichewa
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
إِنَّآ أَنزَلۡنَٰهُ فِي لَيۡلَةٍ مُّبَٰرَكَةٍۚ إِنَّا كُنَّا مُنذِرِينَ
Ife tidalivumbulutsa ilo mu usiku wodalitsika. Ndithudi Ife tili kupitirizabe kuchenjeza
أَمۡرًا مِّنۡ عِندِنَآۚ إِنَّا كُنَّا مُرۡسِلِينَ
Lamulo lochokera kwa Ife, ndithudi Ife timatumiza
رَحۡمَةً مِّن رَّبِّكَۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Chifundo chochokera kwa Ambuye wako, ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa
رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ
Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, ngati inu nonse mutakhala ndi chikhulupiriro chenicheni
لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۖ رَبُّكُمۡ وَرَبُّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Ndipo ndiye amene amapereka moyo ndi imfa. Ambuye wako ndi Ambuye wa makolo ako amene adanka kale
فَٱرۡتَقِبۡ يَوۡمَ تَأۡتِي ٱلسَّمَآءُ بِدُخَانٍ مُّبِينٍ
Motero dikirani tsiku limene kumwamba kudzatsitsa utsi wooneka
يَغۡشَى ٱلنَّاسَۖ هَٰذَا عَذَابٌ أَلِيمٌ
Umene udzazungulira anthu ndipo chimenechi ndi chilango chowawa
رَّبَّنَا ٱكۡشِفۡ عَنَّا ٱلۡعَذَابَ إِنَّا مُؤۡمِنُونَ
Iwo adzati, “Ambuye wathu! Tichotsereni chilango ichi chifukwa tsopano takhulupirira.”
أَنَّىٰ لَهُمُ ٱلذِّكۡرَىٰ وَقَدۡ جَآءَهُمۡ رَسُولٌ مُّبِينٌ
Kodi iwo angachenjezedwe bwanji pamene kunadza kale Mtumwi amene anali kuwauza choonadi
ثُمَّ تَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ وَقَالُواْ مُعَلَّمٌ مَّجۡنُونٌ
Iwo adamutembenukira ndi kumati, “Munthu wophunzitsidwa ndi anthu ena, munthu wamisala.”
إِنَّا كَاشِفُواْ ٱلۡعَذَابِ قَلِيلًاۚ إِنَّكُمۡ عَآئِدُونَ
Ndithudi Ife tidzachotsa chilango pa kanthawi kochepa koma ndithudi inu mudzabwerera
يَوۡمَ نَبۡطِشُ ٱلۡبَطۡشَةَ ٱلۡكُبۡرَىٰٓ إِنَّا مُنتَقِمُونَ
Patsiku limene Ife tidzakugwirani mwamphamvu. Ndithudi tidzawabwezera chilango choyenera
وَلَقَدۡ فَتَنَّا قَبۡلَهُمۡ قَوۡمَ فِرۡعَوۡنَ وَجَآءَهُمۡ رَسُولٌ كَرِيمٌ
Ndipo, ndithudi, tidawayesa anthu a Farawo, iwo asanabadwe, ndipo kudadza kwa iwo Mtumwi wolemekezeka
أَنۡ أَدُّوٓاْ إِلَيَّ عِبَادَ ٱللَّهِۖ إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٌ
Naati “Bweretsani kwa ine akapolo a Mulungu.” “Ndithudi ine ndine Mtumwi wokhulupirika kwa inu.”
وَأَن لَّا تَعۡلُواْ عَلَى ٱللَّهِۖ إِنِّيٓ ءَاتِيكُم بِسُلۡطَٰنٍ مُّبِينٍ
“Ndipo musachitire mwano Mulungu. Ndithudi ine ndadza kwa inu ndi ulamuliro wooneka.”
وَإِنِّي عُذۡتُ بِرَبِّي وَرَبِّكُمۡ أَن تَرۡجُمُونِ
“Ndipo ndithudi ine ndapempha chitetezo cha Ambuye wanga ndi Ambuye wanu kuti musandiononge.”
وَإِن لَّمۡ تُؤۡمِنُواْ لِي فَٱعۡتَزِلُونِ
“Koma ngati inu simundikhulupirira ine, ndiye mundisiye ndekha.”
فَدَعَا رَبَّهُۥٓ أَنَّ هَٰٓؤُلَآءِ قَوۡمٌ مُّجۡرِمُونَ
Ndipo iye anati kwa Ambuye wake, “Anthu awa ndi ochimwa.”
فَأَسۡرِ بِعِبَادِي لَيۡلًا إِنَّكُم مُّتَّبَعُونَ
Choka iwe ndi akapolo anga nthawi yausiku. Ndithudi iwe udzalondoledwa
وَٱتۡرُكِ ٱلۡبَحۡرَ رَهۡوًاۖ إِنَّهُمۡ جُندٌ مُّغۡرَقُونَ
“Ileke nyanja kukhala monga mmene ili. Ndithudi iwo ndi anthu amene adzamizidwa.”
كَمۡ تَرَكُواْ مِن جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ
Kodi ndi minda ingati ndiponso a kasupe angati amene iwo adasiya
كَذَٰلِكَۖ وَأَوۡرَثۡنَٰهَا قَوۡمًا ءَاخَرِينَ
Kotero zinali choncho. Ndipo Ife tidawasankha anthu ena kuti atenge zinthu zawo
فَمَا بَكَتۡ عَلَيۡهِمُ ٱلسَّمَآءُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَا كَانُواْ مُنظَرِينَ
Kumwamba kapena dziko lapansi silidakhetse msozi chifukwa cha iwo ndipo iwo sadapatsidwe mpumulo
وَلَقَدۡ نَجَّيۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ مِنَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡمُهِينِ
Ndithudi tidapulumutsa ana a Israyeli ku chilango chochititsa manyazi
مِن فِرۡعَوۡنَۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَالِيًا مِّنَ ٱلۡمُسۡرِفِينَ
Chimene chidaperekedwa ndi Farawo. Ndithudi iye adali wamwano ndi mmodzi wa anthu oswa malamulo
وَلَقَدِ ٱخۡتَرۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ عِلۡمٍ عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndithudi tidawasankha iwo kuti akhale ndi nzeru kuposa mitundu ina
وَءَاتَيۡنَٰهُم مِّنَ ٱلۡأٓيَٰتِ مَا فِيهِ بَلَٰٓؤٌاْ مُّبِينٌ
Ndipo tidawapatsa chivumbulutso chimene chidali ndi mayesero ooneka
إِنۡ هِيَ إِلَّا مَوۡتَتُنَا ٱلۡأُولَىٰ وَمَا نَحۡنُ بِمُنشَرِينَ
“Palibe china chilichonse kupatula imfa yathu yoyamba ndipo ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.”
فَأۡتُواْ بِـَٔابَآئِنَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
“Kotero bweretsa makolo athu ngati zimene ukunena ndi zoona!”
أَهُمۡ خَيۡرٌ أَمۡ قَوۡمُ تُبَّعٍ وَٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ أَهۡلَكۡنَٰهُمۡۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ مُجۡرِمِينَ
Kodi awa ndi opambana kuposa anthu a Tubba ndi iwo amene adalipo kale? Ife tidawaononga onse ndipo iwo adali olakwa
وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا لَٰعِبِينَ
Ndipo ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo mwamasewera
مَا خَلَقۡنَٰهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Ife sitidazilenge zonsezi kupatula mwachoonadi ndipo ambiri a iwo sadziwa
إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ مِيقَٰتُهُمۡ أَجۡمَعِينَ
Ndithudi tsiku lachimaliziro ndi tsiku lomaliza kwa iwo onse
يَوۡمَ لَا يُغۡنِي مَوۡلًى عَن مَّوۡلًى شَيۡـًٔا وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ
Ndi tsiku limene bwenzi sadzakumbukira bwenzi ake ndipo sadzalandira chithandizo
إِلَّا مَن رَّحِمَ ٱللَّهُۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Kupatula yekhawo amene waonetsedwa chisomo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha
خُذُوهُ فَٱعۡتِلُوهُ إِلَىٰ سَوَآءِ ٱلۡجَحِيمِ
“Mugwire iye ndipo mududuzireni m’kati mwa Gahena.”
ثُمَّ صُبُّواْ فَوۡقَ رَأۡسِهِۦ مِنۡ عَذَابِ ٱلۡحَمِيمِ
Ndipo thirani pamutu pake chilango cha madzi owira
ذُقۡ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡكَرِيمُ
“Lawani ichi! Ndithudi inu munali amphamvu ndi aulemu.”
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي مَقَامٍ أَمِينٍ
“Ndithudi! Iwo amene amalewa zoipa adzakhala kumalo otetezedwa.”
يَلۡبَسُونَ مِن سُندُسٍ وَإِسۡتَبۡرَقٍ مُّتَقَٰبِلِينَ
Iwo atavala Silika wokhuthala ndi wokongola, atakhala moyang’anizana
كَذَٰلِكَ وَزَوَّجۡنَٰهُم بِحُورٍ عِينٍ
Kotero zidzakhala choncho ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa akazi a maso aakuluakulu okongola
يَدۡعُونَ فِيهَا بِكُلِّ فَٰكِهَةٍ ءَامِنِينَ
Iwo adzaitanitsa chipatso cha mtundu uliwonse mwamtendere ndi mokhazikika
لَا يَذُوقُونَ فِيهَا ٱلۡمَوۡتَ إِلَّا ٱلۡمَوۡتَةَ ٱلۡأُولَىٰۖ وَوَقَىٰهُمۡ عَذَابَ ٱلۡجَحِيمِ
Ndipo iwo sadzalawa imfa kupatula imfa yoyamba ndipo Iye adzawapulumutsa ku chilango chowawa cha Gahena
فَضۡلًا مِّن رَّبِّكَۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Chisomo chochokera kwa Ambuye wako! Chimenechi chidzakhala chinthu chopambana kwambiri
فَإِنَّمَا يَسَّرۡنَٰهُ بِلِسَانِكَ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ
Ndithudi Ife taipanga Koraniyi kukhala yapafupi m’chiyankhulo chako ndi cholinga chakuti mwina angathe kukumbukira
Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.