Surah 22 · 78 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Hajj in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

22:1

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمۡۚ إِنَّ زَلۡزَلَةَ ٱلسَّاعَةِ شَيۡءٌ عَظِيمٌ

oh anthu inu! opani Ambuye wanu ndipo kwaniritsani udindo wanu kwa Iye. Ndithudi chivomezi cha nthawiyo chidzakhala choopsa kwambiri

22:2

يَوۡمَ تَرَوۡنَهَا تَذۡهَلُ كُلُّ مُرۡضِعَةٍ عَمَّآ أَرۡضَعَتۡ وَتَضَعُ كُلُّ ذَاتِ حَمۡلٍ حَمۡلَهَا وَتَرَى ٱلنَّاسَ سُكَٰرَىٰ وَمَا هُم بِسُكَٰرَىٰ وَلَٰكِنَّ عَذَابَ ٱللَّهِ شَدِيدٌ

Tsiku limene mudzachiona, mkazi aliyense woyamwitsa adzaiwala mwana wake ndipo mkazi aliyense wapakati adzabala nthawi yake isanafike ndipo udzawaona anthu ngati oledzera pamene sali oledzera; koma chilango cha Mulungu chidzakhala chowawa

22:3

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يُجَٰدِلُ فِي ٱللَّهِ بِغَيۡرِ عِلۡمٍ وَيَتَّبِعُ كُلَّ شَيۡطَٰنٍ مَّرِيدٍ

Ndipo pakati pa anthu pali ena amene amatsutsa za Mulungu pamene sazidziwa, ndipo amatsatira Satana aliyense ogalukira

22:4

كُتِبَ عَلَيۡهِ أَنَّهُۥ مَن تَوَلَّاهُ فَأَنَّهُۥ يُضِلُّهُۥ وَيَهۡدِيهِ إِلَىٰ عَذَابِ ٱلسَّعِيرِ

Kwa iye, zidalamulidwa kuti aliyense amene amutsatira iye, adzamusocheretsa ndipo adzamupititsa ku chilango cha ku ng’anjo ya moto

22:5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِن كُنتُمۡ فِي رَيۡبٍ مِّنَ ٱلۡبَعۡثِ فَإِنَّا خَلَقۡنَٰكُم مِّن تُرَابٍ ثُمَّ مِن نُّطۡفَةٍ ثُمَّ مِنۡ عَلَقَةٍ ثُمَّ مِن مُّضۡغَةٍ مُّخَلَّقَةٍ وَغَيۡرِ مُخَلَّقَةٍ لِّنُبَيِّنَ لَكُمۡۚ وَنُقِرُّ فِي ٱلۡأَرۡحَامِ مَا نَشَآءُ إِلَىٰٓ أَجَلٍ مُّسَمًّى ثُمَّ نُخۡرِجُكُمۡ طِفۡلًا ثُمَّ لِتَبۡلُغُوٓاْ أَشُدَّكُمۡۖ وَمِنكُم مَّن يُتَوَفَّىٰ وَمِنكُم مَّن يُرَدُّ إِلَىٰٓ أَرۡذَلِ ٱلۡعُمُرِ لِكَيۡلَا يَعۡلَمَ مِنۢ بَعۡدِ عِلۡمٍ شَيۡـًٔاۚ وَتَرَى ٱلۡأَرۡضَ هَامِدَةً فَإِذَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡهَا ٱلۡمَآءَ ٱهۡتَزَّتۡ وَرَبَتۡ وَأَنۢبَتَتۡ مِن كُلِّ زَوۡجِۭ بَهِيجٍ

Oh anthu inu! Ngati inu mukayika za kuukanso kwa akufa, ndithudi, Ife tidakulengani kuchokera ku dothi, ndi kudontho la umuna, losakanizana ndi ukazi ndiponso kuchokera ku mnofu oumbidwa bwino osonyeza ziwalo za munthu ndi wina mnopfu umene siunayambe kusonyeza ziwalo kuti tikusonyezeni mphamvu zathu. Ndipo Ife timakhazikitsa m’chiberekero cha mkazi chilichonse chimene tifuna panthawi yomwe yaikidwa ndipo timakutulutsani ngati makanda ndipo mumakula kufika pa msinkhu waumunthu. Ndipo ena a inu amafa ndipo ena amabwezeredwa moyo wapansi kuti asadziwe zonse zimene anali kudziwa kale. Ndipo inu mumaona nthaka ili youma yosamera chilichonse koma tikatsitsa madzi panthakapo, iyo imayamba kugwedezeka ndi kutupa ndi kumeretsa mbewu zokongola zamitundumitundu

22:6

ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ وَأَنَّهُۥ يُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَأَنَّهُۥ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ قَدِيرٌ

Zimenezo ndi chifukwa chakuti Mulungu ndiye choonadi ndipo Iye amapereka moyo ku zinthu zakufa ndipo ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

22:7

وَأَنَّ ٱلسَّاعَةَ ءَاتِيَةٌ لَّا رَيۡبَ فِيهَا وَأَنَّ ٱللَّهَ يَبۡعَثُ مَن فِي ٱلۡقُبُورِ

Ndithudi ola lili nkudza mosakayika pamene Mulungu adzawadzutsa onse amene ali m’manda

22:8

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يُجَٰدِلُ فِي ٱللَّهِ بِغَيۡرِ عِلۡمٍ وَلَا هُدًى وَلَا كِتَٰبٍ مُّنِيرٍ

Ndipo pakati pa anthu pali wina amene amatsutsa za Mulungu pamene sakudziwa chilichonse ndiponso chilangizo kapena Buku la chivumbulutso

22:9

ثَانِيَ عِطۡفِهِۦ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۖ لَهُۥ فِي ٱلدُّنۡيَا خِزۡيٌۖ وَنُذِيقُهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَذَابَ ٱلۡحَرِيقِ

Munthu wotere amathyola khosi monyadira ndi kusocheza ena ku njira ya Mulungu. Kwa otere kuli mnyozo m’moyo uno ndipo patsiku louka kwa akufa, tidzamulawitsa chilango cha moto woyaka

22:10

ذَٰلِكَ بِمَا قَدَّمَتۡ يَدَاكَ وَأَنَّ ٱللَّهَ لَيۡسَ بِظَلَّٰمٍ لِّلۡعَبِيدِ

“Izi ndi chifukwa cha zomwe manja anu adatsogoza ndipo, ndithudi, Mulungu sapondereza akapolo ake

22:11

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَعۡبُدُ ٱللَّهَ عَلَىٰ حَرۡفٍۖ فَإِنۡ أَصَابَهُۥ خَيۡرٌ ٱطۡمَأَنَّ بِهِۦۖ وَإِنۡ أَصَابَتۡهُ فِتۡنَةٌ ٱنقَلَبَ عَلَىٰ وَجۡهِهِۦ خَسِرَ ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةَۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡخُسۡرَانُ ٱلۡمُبِينُ

Ndipo pakati pa anthu pamakhala munthu amene amampembedza Mulungu mokayikira. Zikapezeka zabwino amakhala wokhutitsidwa ndi izo koma ngati mavuto amugwera amatembenuka motero; iye amataya zabwino za m’moyo uno ndi za m’moyo umene uli nkudza. Kumeneko ndiko kulephera koonekeratu

22:12

يَدۡعُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَضُرُّهُۥ وَمَا لَا يَنفَعُهُۥۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلضَّلَٰلُ ٱلۡبَعِيدُ

Iwo amapempha mowonjezera pa Mulungu, zimene sizingathe kumuononga kapena kumuthandiza. Kumeneko ndiko kusochera kwenikweni

22:13

يَدۡعُواْ لَمَن ضَرُّهُۥٓ أَقۡرَبُ مِن نَّفۡعِهِۦۚ لَبِئۡسَ ٱلۡمَوۡلَىٰ وَلَبِئۡسَ ٱلۡعَشِيرُ

Amapempha kwa iye amene mavuto ake ali pafupi kuposa chithandizo chake. Iye, ndithudi, ndi mtsogoleri woipa ndiponso bwenzi loipa

22:14

إِنَّ ٱللَّهَ يُدۡخِلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَفۡعَلُ مَا يُرِيدُ

Ndithudi Mulungu adzawalowetsa onse amene amakhulupilira ndipo amachita ntchito zabwino m’minda yothiriridwa ndi mitsinje ndi madzi oyenda. Ndithudi Mulungu amachita zimene afuna

22:15

مَن كَانَ يَظُنُّ أَن لَّن يَنصُرَهُ ٱللَّهُ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِ فَلۡيَمۡدُدۡ بِسَبَبٍ إِلَى ٱلسَّمَآءِ ثُمَّ لۡيَقۡطَعۡ فَلۡيَنظُرۡ هَلۡ يُذۡهِبَنَّ كَيۡدُهُۥ مَا يَغِيظُ

Ngati wina aganiza kuti Mulungu sadzathandiza Mtumwi wake m’dziko lino ndi m’dziko limene lili nkudza, mulekeni amange chingwe ku phaso la nyumba yake ndi kudzimangirira yekha. Ndipo mulekeni kuti awone yekha ngati cholinga chake chingachotse vuto lomwe limamukwiyitsa iye

22:16

وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَٰهُ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٍ وَأَنَّ ٱللَّهَ يَهۡدِي مَن يُرِيدُ

Kotero Ife talitumiza ilo ngati zizindikiro zooneka ndipo ndithudi Mulungu amatsogolera aliyense amene Iye wamufuna

22:17

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَٱلَّذِينَ هَادُواْ وَٱلصَّٰبِـِٔينَ وَٱلنَّصَٰرَىٰ وَٱلۡمَجُوسَ وَٱلَّذِينَ أَشۡرَكُوٓاْ إِنَّ ٱللَّهَ يَفۡصِلُ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ شَهِيدٌ

Ndithudi iwo amene amakhulupirira, ndi iwo amene ndi Ayuda, Masabina, Akhirisitu, a Magiyani ndi akunja, ndi iwo amene amapembedza zinthu zina mowonjezera pa Mulungu. Ndithudi, Mulungu adzawaweruza pa tsiku la kuuka kwa akufa ndipo Mulungu ndi mboni pa zinthu zonse

22:18

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يَسۡجُدُۤ لَهُۥۤ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ وَٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُ وَٱلنُّجُومُ وَٱلۡجِبَالُ وَٱلشَّجَرُ وَٱلدَّوَآبُّ وَكَثِيرٌ مِّنَ ٱلنَّاسِۖ وَكَثِيرٌ حَقَّ عَلَيۡهِ ٱلۡعَذَابُۗ وَمَن يُهِنِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن مُّكۡرِمٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَفۡعَلُ مَا يَشَآءُ

Kodi iwe siudaone kuti zinthu zonse zimalambira Mulungu mwachitsanzo zinthu zimene zimakhala kumwamba ndi padziko lapansi monga dzuwa, mwezi, nyenyezi, mapiri mitengo, nyama ndi anthu ambiri? Koma pali ambiri amene chilango ndi chowayenera. Aliyense amene achititsidwa manyazi ndi Mulungu, palibe wina amene angamulemekeze. Ndithudi! Mulungu amachita zimene afuna

22:19

هَٰذَانِ خَصۡمَانِ ٱخۡتَصَمُواْ فِي رَبِّهِمۡۖ فَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ قُطِّعَتۡ لَهُمۡ ثِيَابٌ مِّن نَّارٍ يُصَبُّ مِن فَوۡقِ رُءُوسِهِمُ ٱلۡحَمِيمُ

Awa awiri otsutsana, akutsutsana za Ambuye wawo ndipo akakhala sakhulupirira Mulungu, adzawasokera zovala za ku moto ndipo madzi ogaduka adzathiridwa paliombo pawo

22:20

يُصۡهَرُ بِهِۦ مَا فِي بُطُونِهِمۡ وَٱلۡجُلُودُ

Ndi iwo zidzasungunuka zonse zimene zili m’mimba mwawo ndi pa makungu pawo

22:21

وَلَهُم مَّقَٰمِعُ مِنۡ حَدِيدٍ

Iwo adzamangidwa ku unyolo wa zitsulo

22:22

كُلَّمَآ أَرَادُوٓاْ أَن يَخۡرُجُواْ مِنۡهَا مِنۡ غَمٍّ أُعِيدُواْ فِيهَا وَذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡحَرِيقِ

Nthawi iliyonse imene azidzafuna kuti athawe m’menemo, chifukwa chaululu, azidzabwezedwa momwemo ndipo adzauzidwa kuti, “Lawani chilango chamoto.”

22:23

إِنَّ ٱللَّهَ يُدۡخِلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ يُحَلَّوۡنَ فِيهَا مِنۡ أَسَاوِرَ مِن ذَهَبٍ وَلُؤۡلُؤًاۖ وَلِبَاسُهُمۡ فِيهَا حَرِيرٌ

Ndithudi Mulungu adzawalowetsa anthu okhulupirira ndi ochita ntchito zabwino, m’minda yothiriridwa ndi mitsinje yoyenda. Iwo adzavekedwa zibangiri za golide ndi mphete za nkhombe ndipo zovala zawo zidzakhala za silika

22:24

وَهُدُوٓاْ إِلَى ٱلطَّيِّبِ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ وَهُدُوٓاْ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡحَمِيدِ

Iwo ndi otsogozedwa ndi mawu abwino ndipo adatsogozedwa ku njira ya Iye amene ayenera kutamandika kwambiri

22:25

إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَيَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ ٱلَّذِي جَعَلۡنَٰهُ لِلنَّاسِ سَوَآءً ٱلۡعَٰكِفُ فِيهِ وَٱلۡبَادِۚ وَمَن يُرِدۡ فِيهِ بِإِلۡحَادِۭ بِظُلۡمٍ نُّذِقۡهُ مِنۡ عَذَابٍ أَلِيمٍ

Ndithudi! Iwo amene sakhulupirira ndipo amaletsa anzawo kutsatira njira ya Mulungu ndi kupita ku Mzikiti woyera umene tidaupereka kwa anthu a mitundu yonse, kaya ndi eni dziko kaya ndi alendo chimodzimodzi ngati amachita zoipa m’kati mwake, tidzamulawitsa chilango chowawa

22:26

وَإِذۡ بَوَّأۡنَا لِإِبۡرَٰهِيمَ مَكَانَ ٱلۡبَيۡتِ أَن لَّا تُشۡرِكۡ بِي شَيۡـًٔا وَطَهِّرۡ بَيۡتِيَ لِلطَّآئِفِينَ وَٱلۡقَآئِمِينَ وَٱلرُّكَّعِ ٱلسُّجُودِ

Ndi pamene tidamulangiza Abrahamu malo omangapo Mzikiti Woyera tidamuuza kuti, “Usapembedze wina aliyense koma Ine ndekha. Ndipo yeretsa nyumba yanga kuti izikhala yaukhondo chifukwa cha anthu amene amayenda kuizungulira iyo ndi iwo amene amaimirira kapena amagwada ndi kuwerama popembedza.”

22:27

وَأَذِّن فِي ٱلنَّاسِ بِٱلۡحَجِّ يَأۡتُوكَ رِجَالًا وَعَلَىٰ كُلِّ ضَامِرٍ يَأۡتِينَ مِن كُلِّ فَجٍّ عَمِيقٍ

Ndipo uza anthu onse kupita ku Hajji. Iwo adzadza kwa iwe poyenda ulendo wapansi kapena atakwera ngamira yowonda chifukwa chakutopa ndipo iwo adzadza kuchokera kumbali zonse za kutali ndi njira za m’mapiri

22:28

لِّيَشۡهَدُواْ مَنَٰفِعَ لَهُمۡ وَيَذۡكُرُواْ ٱسۡمَ ٱللَّهِ فِيٓ أَيَّامٍ مَّعۡلُومَٰتٍ عَلَىٰ مَا رَزَقَهُم مِّنۢ بَهِيمَةِ ٱلۡأَنۡعَٰمِۖ فَكُلُواْ مِنۡهَا وَأَطۡعِمُواْ ٱلۡبَآئِسَ ٱلۡفَقِيرَ

Kuti adzaona zinthu zimene zili zaphindu kwa iwo ndi kutchula dzina la Mulungu, pa masiku osankhidwa, pa nyama ya ng’ombe imene Iye wawapatsa iwo. Idyani gawo lina ndiponso dyetsani osauka amene ali pa mavuto

22:29

ثُمَّ لۡيَقۡضُواْ تَفَثَهُمۡ وَلۡيُوفُواْ نُذُورَهُمۡ وَلۡيَطَّوَّفُواْ بِٱلۡبَيۡتِ ٱلۡعَتِيقِ

Aloleni kuti amalize miyambo yofunika ndi kukwaniritsa malonjezo awo ndiponso kuzungulira Nyumba ya Makedzana

22:30

ذَٰلِكَۖ وَمَن يُعَظِّمۡ حُرُمَٰتِ ٱللَّهِ فَهُوَ خَيۡرٌ لَّهُۥ عِندَ رَبِّهِۦۗ وَأُحِلَّتۡ لَكُمُ ٱلۡأَنۡعَٰمُ إِلَّا مَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡۖ فَٱجۡتَنِبُواْ ٱلرِّجۡسَ مِنَ ٱلۡأَوۡثَٰنِ وَٱجۡتَنِبُواْ قَوۡلَ ٱلزُّورِ

Izi zikhale choncho. Ndipo aliyense amene alemekeza miyambo yolemekezeka ya Mulungu zidzakhala zabwino kwa iye pamaso pa Ambuye wake. Nyama ya ng’ombe, ndi yololedwa kwa inu kupatula nyama zokhazo zimene zikutchulidwa kwa inu kukhala zoletsedwa. Pewani zonyansa za mafano, ndipo pewani bodza

22:31

حُنَفَآءَ لِلَّهِ غَيۡرَ مُشۡرِكِينَ بِهِۦۚ وَمَن يُشۡرِكۡ بِٱللَّهِ فَكَأَنَّمَا خَرَّ مِنَ ٱلسَّمَآءِ فَتَخۡطَفُهُ ٱلطَّيۡرُ أَوۡ تَهۡوِي بِهِ ٱلرِّيحُ فِي مَكَانٍ سَحِيقٍ

Musapembedze wina aliyense koma Mulungu ndipo musatumikire milungu ina. Aliyense amene amatumikira milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, ali ngati iye amene agwa kuchokera kumwamba, ndipo asanagwe pansi, amalandiridwa ndi mbalame kapena kunyamulidwa ndi mphepo kukam’taya kumalo akutali

22:32

ذَٰلِكَۖ وَمَن يُعَظِّمۡ شَعَٰٓئِرَ ٱللَّهِ فَإِنَّهَا مِن تَقۡوَى ٱلۡقُلُوبِ

Zimenezi zili tero. Aliyense amene amalemekeza zizindikiro za Mulungu kumeneko ndiko kuyera mtima

22:33

لَكُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ إِلَىٰٓ أَجَلٍ مُّسَمًّى ثُمَّ مَحِلُّهَآ إِلَى ٱلۡبَيۡتِ ٱلۡعَتِيقِ

Mu izo muli zokoma zosiyanasiyana mpaka pa nthawi imene yaikidwa ndipo pomaliza zimaperekedwa ngati nsembe ku Nyumba ya Makedzana

22:34

وَلِكُلِّ أُمَّةٍ جَعَلۡنَا مَنسَكًا لِّيَذۡكُرُواْ ٱسۡمَ ٱللَّهِ عَلَىٰ مَا رَزَقَهُم مِّنۢ بَهِيمَةِ ٱلۡأَنۡعَٰمِۗ فَإِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٌ وَٰحِدٌ فَلَهُۥٓ أَسۡلِمُواْۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُخۡبِتِينَ

Ku mtundu uliwonse, Ife tidakhazikitsa miyambo yachipembedzo kuti azitchula dzina la Mulungu pa nyama zimene Iyeadawapatsaiwongatichakudya. Ndipo Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi yekha motero muzigonjera Iye yekha. Auzeni nkhani yabwino anthu onse odzichepetsa

22:35

ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِرَ ٱللَّهُ وَجِلَتۡ قُلُوبُهُمۡ وَٱلصَّٰبِرِينَ عَلَىٰ مَآ أَصَابَهُمۡ وَٱلۡمُقِيمِي ٱلصَّلَوٰةِ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ

Anthu amene mitima yawo imadzala ndi mantha pamene Mulungu atchulidwa ndiponso amene amapilira pamavuto amene awapeza ndipo amapitiriza mapemphero awo ndi kupereka zina za zimene tidawapatsa

22:36

وَٱلۡبُدۡنَ جَعَلۡنَٰهَا لَكُم مِّن شَعَٰٓئِرِ ٱللَّهِ لَكُمۡ فِيهَا خَيۡرٌۖ فَٱذۡكُرُواْ ٱسۡمَ ٱللَّهِ عَلَيۡهَا صَوَآفَّۖ فَإِذَا وَجَبَتۡ جُنُوبُهَا فَكُلُواْ مِنۡهَا وَأَطۡعِمُواْ ٱلۡقَانِعَ وَٱلۡمُعۡتَرَّۚ كَذَٰلِكَ سَخَّرۡنَٰهَا لَكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Ndi nyama zina tidazipanga kukhala ngati zina mwa zizindikiro za Mulungu ndipo mwa izo muli zofunika kwambiri kwa inu. Motero tchulani dzina la Mulungu pa izo pamene muziika kuti ziperekedwe nsembe. Ndipo zikaphedwa, idyani nyama yake ndiponso mumudyetse wopempha ndi amene apempha mwamanyazi. Kotero Ife nyamazi tazipereka kwa inu kuti mukhale othokoza

22:37

لَن يَنَالَ ٱللَّهَ لُحُومُهَا وَلَا دِمَآؤُهَا وَلَٰكِن يَنَالُهُ ٱلتَّقۡوَىٰ مِنكُمۡۚ كَذَٰلِكَ سَخَّرَهَا لَكُمۡ لِتُكَبِّرُواْ ٱللَّهَ عَلَىٰ مَا هَدَىٰكُمۡۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Si mnofu wawo kapena magazi awo amene amafika kwa Mulungu koma ndi kumvera Mulungu kumene kumafika kwa Iye. Kotero Ife tazilamula kuti zizikutumikirani kuti muzilemekeza Mulungu chifukwa chokulangizani inu njira yoyenera. Auze nkhani yabwino anthu angwiro

22:38

إِنَّ ٱللَّهَ يُدَٰفِعُ عَنِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ كُلَّ خَوَّانٍ كَفُورٍ

Ndithudi Mulungu amatchinjiriza anthu okhulupirira. Ndithudi Iye sakonda anthu a chinyengo ndiponso osathokoza

22:39

أُذِنَ لِلَّذِينَ يُقَٰتَلُونَ بِأَنَّهُمۡ ظُلِمُواْۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ نَصۡرِهِمۡ لَقَدِيرٌ

Chilolezo chomenya nkhondo chili kuperekedwa kwa iwo amene aputidwa, chifukwa chakuti awachimwira. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu yowapambanitsa

22:40

ٱلَّذِينَ أُخۡرِجُواْ مِن دِيَٰرِهِم بِغَيۡرِ حَقٍّ إِلَّآ أَن يَقُولُواْ رَبُّنَا ٱللَّهُۗ وَلَوۡلَا دَفۡعُ ٱللَّهِ ٱلنَّاسَ بَعۡضَهُم بِبَعۡضٍ لَّهُدِّمَتۡ صَوَٰمِعُ وَبِيَعٌ وَصَلَوَٰتٌ وَمَسَٰجِدُ يُذۡكَرُ فِيهَا ٱسۡمُ ٱللَّهِ كَثِيرًاۗ وَلَيَنصُرَنَّ ٱللَّهُ مَن يَنصُرُهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَقَوِيٌّ عَزِيزٌ

Anthuwo ndi amene apirikitsidwa kuchokerakunyumbazawomopandachilungamochifukwa chakuti iwo anati, “Ambuye wathu ndi Mulungu.” Ndipo Mulungu akadapanda kuyesa anthu ena ndi mphamvu za anthu anzawo makachisi, matchalitchi, masunagoge ndi mizikiti imene dzina la Mulungu limatchulidwa kwambiri ikadaonongekeratu. Ndithudi Mulungu adzathandiza amene amathandiza chipembedzo chake. Ndithudi Mulungu ndi mphamvu ndiponso Wopambana kwambiri

22:41

ٱلَّذِينَ إِن مَّكَّنَّٰهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَوُاْ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَمَرُواْ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَنَهَوۡاْ عَنِ ٱلۡمُنكَرِۗ وَلِلَّهِ عَٰقِبَةُ ٱلۡأُمُورِ

Iwo amene tawapatsa mphamvu padziko lapansi adzapitiriza mapemphero nthawi zonse ndi kupereka msonkho wothandiza osauka, ndipo adzakhazikitsa chilungamo ndi kuletsa zoipa. Kwa Mulungu ndiko kuli mapeto a zinthu zonse

22:42

وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدۡ كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٍ وَعَادٌ وَثَمُودُ

Ndipo ngati akukana iwe, ndithudi asanadze awa, nawonso anthu a Nowa, Aad ndi Thamud adakana Atumwi awo

22:43

وَقَوۡمُ إِبۡرَٰهِيمَ وَقَوۡمُ لُوطٍ

Ndiponso anthu a Abrahamu ndi anthu a Loti zidali choncho

22:44

وَأَصۡحَٰبُ مَدۡيَنَۖ وَكُذِّبَ مُوسَىٰۖ فَأَمۡلَيۡتُ لِلۡكَٰفِرِينَ ثُمَّ أَخَذۡتُهُمۡۖ فَكَيۡفَ كَانَ نَكِيرِ

Ndi anthu okhala ku Midiyani. Mose nayenso adakanidwa. Koma Ine ndidawapatsa nthawi anthu osakhulupirira ndipo pomaliza chilango changa chidawapeza onse. Kodi chilango changa chidali choopsa bwanji

22:45

فَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَا وَهِيَ ظَالِمَةٌ فَهِيَ خَاوِيَةٌ عَلَىٰ عُرُوشِهَا وَبِئۡرٍ مُّعَطَّلَةٍ وَقَصۡرٍ مَّشِيدٍ

Kodi ndi mizinda ingati ya anthu ochita zoipa imene taononga? Mizinda yawo idaonongeka, madenga ake kugwera pansi ndiponso ndi zitsime zingati zimene zidangokhala kusowa anthu otungapo madzi ndiponso ndi nyumba zingati zomangidwa bwino zimene zidasanduka mabwinja

22:46

أَفَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَتَكُونَ لَهُمۡ قُلُوبٌ يَعۡقِلُونَ بِهَآ أَوۡ ءَاذَانٌ يَسۡمَعُونَ بِهَاۖ فَإِنَّهَا لَا تَعۡمَى ٱلۡأَبۡصَٰرُ وَلَٰكِن تَعۡمَى ٱلۡقُلُوبُ ٱلَّتِي فِي ٱلصُّدُورِ

Kodi iwo sanayende pa dziko kuti mitima yawo ikhale yozindikira ndi makutu awo kuti amvere? Ndithudi si maso awo amene ali ndi khungu, koma ndi mitima imene ili mu zifuwa zawo imene ili ndi khungu

22:47

وَيَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَلَن يُخۡلِفَ ٱللَّهُ وَعۡدَهُۥۚ وَإِنَّ يَوۡمًا عِندَ رَبِّكَ كَأَلۡفِ سَنَةٍ مِّمَّا تَعُدُّونَ

Ndipo ali kuuza iwe kuti ufulumizitse chilango! Ndipo Mulungu salephera kukwaniritsa lonjezo lake. Ndithudi tsiku lililonse kwa Mulungu lili ngati zaka chikwi chimodzi mu kuwerenga kwanu

22:48

وَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ أَمۡلَيۡتُ لَهَا وَهِيَ ظَالِمَةٌ ثُمَّ أَخَذۡتُهَا وَإِلَيَّ ٱلۡمَصِيرُ

Ndi mizinda ingati imene ndidaipatsa mwayi wa nthawi pamene iyoyo inali kuchitabe zoipa? Ndipo pambuyo pake ndidaipatsa chilango Kwa Ine zinthu zonse zidzabwerera

22:49

قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّمَآ أَنَا۠ لَكُمۡ نَذِيرٌ مُّبِينٌ

Nena, “Oh anthu inu! Ndithudi ine ndatumizidwa ngati mchenjezi wanu!”

22:50

فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُم مَّغۡفِرَةٌ وَرِزۡقٌ كَرِيمٌ

Motero iwo amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhululukidwa machimo awo ndi kulipidwa mphotho yolemekezeka

22:51

وَٱلَّذِينَ سَعَوۡاْ فِيٓ ءَايَٰتِنَا مُعَٰجِزِينَ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَحِيمِ

Koma iwo amene amalimbikira kutsutsa zizindikiro zathu, adzakhala eni ake a ku Gahena

22:52

وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رَّسُولٍ وَلَا نَبِيٍّ إِلَّآ إِذَا تَمَنَّىٰٓ أَلۡقَى ٱلشَّيۡطَٰنُ فِيٓ أُمۡنِيَّتِهِۦ فَيَنسَخُ ٱللَّهُ مَا يُلۡقِي ٱلشَّيۡطَٰنُ ثُمَّ يُحۡكِمُ ٱللَّهُ ءَايَٰتِهِۦۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ

Ife sitidatumizepo Mtumwi kapena Mneneri, iwe usanadze, koma iye amati akamalakatula chivumbulutso kapena kulalikira, Satana anali kuonjezera bodza. Koma Mulungu amachotsa zonse zimene Satana waikamo. Motero Mulungu amakhazikitsa chivumbulutso chake ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha

22:53

لِّيَجۡعَلَ مَا يُلۡقِي ٱلشَّيۡطَٰنُ فِتۡنَةً لِّلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ وَٱلۡقَاسِيَةِ قُلُوبُهُمۡۗ وَإِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ لَفِي شِقَاقِۭ بَعِيدٍ

Kuti Iye apange zimene wanena Satana kukhala mayesero kwa iwo amene m’mitima mwawo muli matenda ndi amene mitima yawo ndi youma. Ndithudi anthu ochita zoipa amatsutsa kwambiri choonadi

22:54

وَلِيَعۡلَمَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَيُؤۡمِنُواْ بِهِۦ فَتُخۡبِتَ لَهُۥ قُلُوبُهُمۡۗ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهَادِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ

Ndipo kuti iwo amene adapatsidwa nzeru azindikire kuti ichi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wako ndipo ayenera kukhulupirira ndi kuti mitima yawo ikhale yodzichepetsa chifukwa cha iyo. Ndithudi Mulungu ndi Mtsogoleri wa iwo amene akhulupirira njira yoyenera

22:55

وَلَا يَزَالُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي مِرۡيَةٍ مِّنۡهُ حَتَّىٰ تَأۡتِيَهُمُ ٱلسَّاعَةُ بَغۡتَةً أَوۡ يَأۡتِيَهُمۡ عَذَابُ يَوۡمٍ عَقِيمٍ

Ndipo anthu osakhulupirira adzapitirira kukayikira chivumbulutso mpaka pamene ora lomaliza lidzawapeza mwadzidzidzi kapena mpaka pamene chilango cha tsiku louka kwa akufa chidzawadzera

22:56

ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَئِذٍ لِّلَّهِ يَحۡكُمُ بَيۡنَهُمۡۚ فَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ

Ufumu, patsiku limeneli, udzakhala wa Mulungu yekha. Iye adzaweruza pakati pawo. Motero onse amene adakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino adzakhala ku Paradiso

22:57

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَأُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٌ مُّهِينٌ

Ndipo iwo amene sanakhulupirire ndipo amakana zizindikiro zathu chawo chidzakhala chilango chochititsa manyazi

22:58

وَٱلَّذِينَ هَاجَرُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ ثُمَّ قُتِلُوٓاْ أَوۡ مَاتُواْ لَيَرۡزُقَنَّهُمُ ٱللَّهُ رِزۡقًا حَسَنًاۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهُوَ خَيۡرُ ٱلرَّٰزِقِينَ

Iwo amene adasamuka kwawo chifukwa chofuna kukweza chipembedzo cha Mulungu ndipo pambuyo pake adaphedwa kapena adafa, Mulungu, ndithudi, adzawapatsa mphatso zabwino. Ndithudi Mulungu ndi wopereka zabwino kuposa onse amene amapereka

22:59

لَيُدۡخِلَنَّهُم مُّدۡخَلًا يَرۡضَوۡنَهُۥۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَعَلِيمٌ حَلِيمٌ

Ndithudi Mulungu adzawalowetsa iwo ku malo amene adzasangalala nawo ndipo Mulungu, ndithudi, ndi wodziwa zonse ndiponso wopirira kwambiri

22:60

ذَٰلِكَۖ وَمَنۡ عَاقَبَ بِمِثۡلِ مَا عُوقِبَ بِهِۦ ثُمَّ بُغِيَ عَلَيۡهِ لَيَنصُرَنَّهُ ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَعَفُوٌّ غَفُورٌ

Izo zili tero. Ndipo aliyense amene abwezera mnzake chilango chofanana ndi chimene iye wapatsidwa ndipo pambuyo pake amulakwiranso, ndithudi, Mulungu adzamuthandiza iye. Ndithudi! Mulungu ndi wachisoni ndiponso wokhululukira

22:61

ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِ وَأَنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٌ

Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu amalowetsa usiku mu usana ndi kulowetsa usana mu usiku. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi woona

22:62

ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ هُوَ ٱلۡبَٰطِلُ وَأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡكَبِيرُ

Zonsezi ndi chifukwa chakuti Mulungu ndiye choonadi ndipo zonse zimene iwo amazipembedza kuonjezera pa Mulungu ndi zabodza. Ndithudi Mulungu ndi wapamwamba ndiponso wamkulu

22:63

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَتُصۡبِحُ ٱلۡأَرۡضُ مُخۡضَرَّةًۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَطِيفٌ خَبِيرٌ

Kodi iwe siukuona kuti Mulungu amagwetsa mvula kuchokera kumwamba ndipo kuti nthaka imakhala ndi zomera zobiriwira? Ndithudi Mulungu ndi Mwini chisoni chosatha, wodziwa zonse zobisika ndi zoonekera

22:64

لَّهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَهُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ

Mulungu ndiye mwini zonse za kumwamba ndi dziko lapansi. Ndithudi Mulungu ndi wolemera ndi wotamandidwa

22:65

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ سَخَّرَ لَكُم مَّا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَٱلۡفُلۡكَ تَجۡرِي فِي ٱلۡبَحۡرِ بِأَمۡرِهِۦ وَيُمۡسِكُ ٱلسَّمَآءَ أَن تَقَعَ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا بِإِذۡنِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِٱلنَّاسِ لَرَءُوفٌ رَّحِيمٌ

Kodi inu simuona kuti Mulungu wakupeputsirani zonse zimene zili pa dziko lapansi ndi zombo zimene mumayendera pa nyanja ndi chilolezo chake? Iye amagwira thambo kuti lisagwe pansi. Ndithudi Mulungu ndi wachisoni ndiponso wachifundo kwa anthu

22:66

وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَحۡيَاكُمۡ ثُمَّ يُمِيتُكُمۡ ثُمَّ يُحۡيِيكُمۡۗ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَكَفُورٌ

Iye ndiye amene adakupatsani moyo ndipo adzapangitsa kuti mufe ndi kukupatsaninso moyo kachiwiri. Ndithudi munthu ndi wosathokoza

22:67

لِّكُلِّ أُمَّةٍ جَعَلۡنَا مَنسَكًا هُمۡ نَاسِكُوهُۖ فَلَا يُنَٰزِعُنَّكَ فِي ٱلۡأَمۡرِۚ وَٱدۡعُ إِلَىٰ رَبِّكَۖ إِنَّكَ لَعَلَىٰ هُدًى مُّسۡتَقِيمٍ

Ku mtundu uliwonse Ife tidalamulira miyambo ya chipembedzo imene iwo ayenera kuitsatira ndipo iwo asakangane ndi iwe pa nkhani iyi. Koma aitanire kwa Ambuye wako. Ndithudi iwe uli pa njira yoyenera

22:68

وَإِن جَٰدَلُوكَ فَقُلِ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا تَعۡمَلُونَ

Ndipo ngati iwo atsutsana ndi iwe, nena “Mulungu amadziwa bwino zonse zimene inu mumachita.”

22:69

ٱللَّهُ يَحۡكُمُ بَيۡنَكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كُنتُمۡ فِيهِ تَخۡتَلِفُونَ

Mulungu adzaweruza, pakati panu, patsiku lachiweruzo, zimene inu munali kusiyana

22:70

أَلَمۡ تَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّ ذَٰلِكَ فِي كِتَٰبٍۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٌ

Kodi iwe siudziwa kuti Mulungu amadziwa zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi? Ndithudi zonse zidalembedwa m’Buku lake. Ndithudi zimenezo ndi zosavuta kwa Mulungu

22:71

وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَمۡ يُنَزِّلۡ بِهِۦ سُلۡطَٰنًا وَمَا لَيۡسَ لَهُم بِهِۦ عِلۡمٌۗ وَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِن نَّصِيرٍ

Ndipo iwo ali kupembedza zinthu zina mowonjezera pa Mulungu, zinthu zimene sanapatsidwe umboni kuti azizigwadira ndipo ndi zimene iwo salikuzindikira. Ndithudi, anthu ochimwa alibe wowathandiza

22:72

وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٍ تَعۡرِفُ فِي وُجُوهِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ ٱلۡمُنكَرَۖ يَكَادُونَ يَسۡطُونَ بِٱلَّذِينَ يَتۡلُونَ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِنَاۗ قُلۡ أَفَأُنَبِّئُكُم بِشَرٍّ مِّن ذَٰلِكُمُۚ ٱلنَّارُ وَعَدَهَا ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ

Ndipo pamene chivumbulutso chathu chomveka chilakatulidwa kwa iwo, iwe udzaona kukana pa maso pa anthu osakhulupirira! Iwo ali pafupifupi kumenyana ndi iwo amene amalakatula chivumbulutso chathu kwa iwo. Nena “Kodi mufuna ndikuuzeni zoipa kuposa chizindikiro choterechi? Chizindikirocho ndi moto wa ku Gahena umene Mulungu walonjeza anthu osakhulupirira ndipo amenewa ndi malo oipa kupitako.”

22:73

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ضُرِبَ مَثَلٌ فَٱسۡتَمِعُواْ لَهُۥٓۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ لَن يَخۡلُقُواْ ذُبَابًا وَلَوِ ٱجۡتَمَعُواْ لَهُۥۖ وَإِن يَسۡلُبۡهُمُ ٱلذُّبَابُ شَيۡـًٔا لَّا يَسۡتَنقِذُوهُ مِنۡهُۚ ضَعُفَ ٱلطَّالِبُ وَٱلۡمَطۡلُوبُ

Oh anthu inu! Fanizo laperekedwa ndipo limvetsetseni. Ndithudi! Iwo amene mumawapembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni sangathe kulenga ntchentche imodzi ngakhale onse atagwirizana kuti achite choncho. Ndipo ngati ntchentche italanda kalikonse kuchokera kwa iwo, iwo sangathe kuilanda ayi. Anthu opempha ndi wopemphedwa onse alibe mphamvu

22:74

مَا قَدَرُواْ ٱللَّهَ حَقَّ قَدۡرِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَقَوِيٌّ عَزِيزٌ

Iwo sapereka ulemu kwa Mulungu umene uyenera kuperekedwa kwa Iye. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu ndipo ndi Mwini mphamvu zonse

22:75

ٱللَّهُ يَصۡطَفِي مِنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ رُسُلًا وَمِنَ ٱلنَّاسِۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٌ

Mulungu amasankha Atumwi ake pakati pa Angelo ndi pakati pa anthu. Ndithudi Mulungu amamva zonse ndiponso amaona chilichonse

22:76

يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ

Iye amadziwa zonse zimene zili patsogolo pawo ndi zimene zili m’mbuyo mwawo. Kwa Mulungu zinthu zonse zimabwerera

22:77

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱرۡكَعُواْ وَٱسۡجُدُواْۤ وَٱعۡبُدُواْ رَبَّكُمۡ وَٱفۡعَلُواْ ٱلۡخَيۡرَ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ

oh inu anthu amene mwakhulupirira! weramani ndipo gunditsani mphumi zanu pansi ndi kupembedza Ambuye wanu ndipo chitani ntchito zabwino kuti mupambane

22:78

وَجَٰهِدُواْ فِي ٱللَّهِ حَقَّ جِهَادِهِۦۚ هُوَ ٱجۡتَبَىٰكُمۡ وَمَا جَعَلَ عَلَيۡكُمۡ فِي ٱلدِّينِ مِنۡ حَرَجٍۚ مِّلَّةَ أَبِيكُمۡ إِبۡرَٰهِيمَۚ هُوَ سَمَّىٰكُمُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ مِن قَبۡلُ وَفِي هَٰذَا لِيَكُونَ ٱلرَّسُولُ شَهِيدًا عَلَيۡكُمۡ وَتَكُونُواْ شُهَدَآءَ عَلَى ٱلنَّاسِۚ فَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱعۡتَصِمُواْ بِٱللَّهِ هُوَ مَوۡلَىٰكُمۡۖ فَنِعۡمَ ٱلۡمَوۡلَىٰ وَنِعۡمَ ٱلنَّصِيرُ

Ndipo limbikani kwambiri chifukwa cha chipembedzo chaMulungumongammenezikufunikira.Iyewakusankhani inu ndipo sadakukundikireni mavuto muchipembedzo chanu. Chipembedzo cha Abrahamu atate wanu. Iye ndiye amene akupatsani inu dzina lakuti Asilamu kuyambira kalekale ndiponso mu dzinali Mtumwi ndiye mboni yanu, ndipo nanunso mukhale mboni ya anthu anzanu. Pitirizani mapemphero, perekani msonkho wothandizira anthu osauka ndipo khulupirirani mwa Mulungu. Iye ndi Mtetezi wanu wabwino ndiponso Mthandizi wabwino kwambiri

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.