Surah 107 · 7 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Ma'un in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

107:1

أَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي يُكَذِّبُ بِٱلدِّينِ

Kodi wamuona munthu amene amakana kuti kuli tsiku la chiweruzo

107:2

فَذَٰلِكَ ٱلَّذِي يَدُعُّ ٱلۡيَتِيمَ

Iye ndiye amene amazunza mwana wamasiye

107:3

وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ

Ndipo sakakamiza anthu ena kuti azidyetsa anthu osauka

107:4

فَوَيۡلٌ لِّلۡمُصَلِّينَ

Motero tsoka kwa iwo amene amapemphera

107:5

ٱلَّذِينَ هُمۡ عَن صَلَاتِهِمۡ سَاهُونَ

Amene salabadira mapemphero awo

107:6

ٱلَّذِينَ هُمۡ يُرَآءُونَ

Amene amachita zabwino pofuna kuti ena awaone

107:7

وَيَمۡنَعُونَ ٱلۡمَاعُونَ

Ndipo amakana kupereka chaulere

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.