Surah 39 · 75 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Az-Zumar in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

39:1

تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ

Chivumbulutso cha Buku ili ndi chochokera kwa Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru

39:2

إِنَّآ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ بِٱلۡحَقِّ فَٱعۡبُدِ ٱللَّهَ مُخۡلِصًا لَّهُ ٱلدِّينَ

Ndithudi tavumbulutsa kwa iwe Buku mwachoonadi. Motero pembedza Mulungu yekha ndipo udzipereke kwa Iye kwathunthu

39:3

أَلَا لِلَّهِ ٱلدِّينُ ٱلۡخَالِصُۚ وَٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ مَا نَعۡبُدُهُمۡ إِلَّا لِيُقَرِّبُونَآ إِلَى ٱللَّهِ زُلۡفَىٰٓ إِنَّ ٱللَّهَ يَحۡكُمُ بَيۡنَهُمۡ فِي مَا هُمۡ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي مَنۡ هُوَ كَٰذِبٌ كَفَّارٌ

Ndithudi kumvera ndi kupembedza, ndi kwa Mulungu yekha ndipo iwo amene amasankha ena kuti akhale owasamala m’malo mwa Mulungu amati, “Ife sitiwapembedza iwo ayi koma timafuna kuti iwo atifikitse pafupi ndi Mulungu.” Ndithudi Mulungu adzaweruza pa zonse zimene iwo amatsutsana. Ndithudi Mulungu satsogolera wabodza ndi wosakhulupirira

39:4

لَّوۡ أَرَادَ ٱللَّهُ أَن يَتَّخِذَ وَلَدًا لَّٱصۡطَفَىٰ مِمَّا يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ سُبۡحَٰنَهُۥۖ هُوَ ٱللَّهُ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّارُ

Ngati Mulungu akadafuna kukhala ndi mwana, ndithudi, Iye akadasankha iwo amene wawafuna kuchokera ku gulu la zolengedwa zake. Koma ulemerero ukhale kwa Iye. Iye ndi Mulungu mmodzi ndi wogonjetsa onse

39:5

خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۖ يُكَوِّرُ ٱلَّيۡلَ عَلَى ٱلنَّهَارِ وَيُكَوِّرُ ٱلنَّهَارَ عَلَى ٱلَّيۡلِۖ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلٌّ يَجۡرِي لِأَجَلٍ مُّسَمًّىۗ أَلَا هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفَّٰرُ

Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi m’choonadi Iye amapanga usiku kuti uphimbe usana ndiponso amapanga usana kuti uphimbe usiku ndipo adalamula dzuwa ndi mwezi kukhala zopanda mphamvu. Chilichonse kumaenda mu msewu wakewake. Ndithudi Iye ndi wamphamvu, ndi wokhululukira nthawi zonse

39:6

خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسٍ وَٰحِدَةٍ ثُمَّ جَعَلَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ ثَمَٰنِيَةَ أَزۡوَٰجٍۚ يَخۡلُقُكُمۡ فِي بُطُونِ أُمَّهَٰتِكُمۡ خَلۡقًا مِّنۢ بَعۡدِ خَلۡقٍ فِي ظُلُمَٰتٍ ثَلَٰثٍۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ لَهُ ٱلۡمُلۡكُۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَأَنَّىٰ تُصۡرَفُونَ

Iye adakulengani inu nonse kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo adalenga mnzake wolingana naye. Ndipo Iye adakutumizirani inu ng’ombe zisanu ndi zitatu zazimuna ndi zazikazi. Iye adakulengani inu m’mimba mwa amayi anu, chilengedwe chotsagana ndi chilengedwe china, m’magulu atatu a mdima. Iye ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Kulibenso Mulungu wina koma Iye yekha. Nanga ndi chifukwa chiyani inu musocheretsedwa

39:7

إِن تَكۡفُرُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَنِيٌّ عَنكُمۡۖ وَلَا يَرۡضَىٰ لِعِبَادِهِ ٱلۡكُفۡرَۖ وَإِن تَشۡكُرُواْ يَرۡضَهُ لَكُمۡۗ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُم مَّرۡجِعُكُمۡ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ

Ngati inu simukhulupirira, ndithudi, muyenera kudziwa kuti Mulungu ndi woima payekha ndipo alibe nanu kanthu ayi. Iye sakonda kusakhulupirira kwa akapolo ake. Koma ngati inu muthokoza, Iye amasangalala nanu. Ndipo palibe munthu amene adzasenza katundu wa mnzake. Ndipo ndi kwa Ambuye wanu kumene nonse mudzabwerera. Ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene mudachita. Ndithudi Iye amadziwa chilichonse chimene chili m’mitima mwanu

39:8

وَإِذَا مَسَّ ٱلۡإِنسَٰنَ ضُرٌّ دَعَا رَبَّهُۥ مُنِيبًا إِلَيۡهِ ثُمَّ إِذَا خَوَّلَهُۥ نِعۡمَةً مِّنۡهُ نَسِيَ مَا كَانَ يَدۡعُوٓاْ إِلَيۡهِ مِن قَبۡلُ وَجَعَلَ لِلَّهِ أَندَادًا لِّيُضِلَّ عَن سَبِيلِهِۦۚ قُلۡ تَمَتَّعۡ بِكُفۡرِكَ قَلِيلًا إِنَّكَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلنَّارِ

Koma pamene mavuto akhazikika pa munthu, iye amapempha Ambuye wake pafupipafupi koma munthuyo akalandira chisomo chochokera kwa Ambuye wake iye amaiwala zimene amalilira poyamba ndipo amakhazikitsa opikisana ndi Mulungu ndi cholinga chosokoneza anthu ku njira yoyenera ya Mulungu. Nena “Basangalalani ndi kusakhulupirira kwanu kwa kanthawi kochepa. Ndithudi inu ndinu okakhala ku moto!”

39:9

أَمَّنۡ هُوَ قَٰنِتٌ ءَانَآءَ ٱلَّيۡلِ سَاجِدًا وَقَآئِمًا يَحۡذَرُ ٱلۡأٓخِرَةَ وَيَرۡجُواْ رَحۡمَةَ رَبِّهِۦۗ قُلۡ هَلۡ يَسۡتَوِي ٱلَّذِينَ يَعۡلَمُونَ وَٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَۗ إِنَّمَا يَتَذَكَّرُ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Kodi iye amene amamvera Mulungu ndipo amadzipereka m’mapemphero nthawi ya usiku ndi kugwada kapena kuimirira popembedza ndiponso amene amaopa za m’moyo umene uli nkudza ndipo amalakalaka chisomo cha Ambuye wake ndi wofanana ndi osakhulupirira? Nena, “Kodi iwo amene amadziwa ndi ofanana ndi iwo osadziwa?” Ndi okhawo amene ndi ozindikira amene adzakumbukira

39:10

قُلۡ يَٰعِبَادِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمۡۚ لِلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٌۗ وَأَرۡضُ ٱللَّهِ وَٰسِعَةٌۗ إِنَّمَا يُوَفَّى ٱلصَّٰبِرُونَ أَجۡرَهُم بِغَيۡرِ حِسَابٍ

Nena, “oh inu akapolo anga amene mwakhulupirira! opani Ambuye wanu. Mphotho yokoma ili kuwandikira iwo amene amachita zabwino m’dziko lino. Ndipo dziko la Mulungu lili ndi malo ambiri. Ndipo onse amene amapirira, ndithudi adzalandira mphotho yopanda malire.”

39:11

قُلۡ إِنِّيٓ أُمِرۡتُ أَنۡ أَعۡبُدَ ٱللَّهَ مُخۡلِصًا لَّهُ ٱلدِّينَ

Nena,“Inendalamulidwakutindizipembedza Mulungu ndi mtima wanga wonse.”

39:12

وَأُمِرۡتُ لِأَنۡ أَكُونَ أَوَّلَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ

“Ndiponso ine ndalamulidwa kukhala woyamba pakati pa iwo amene amadzipereka kwa Mulungu, m’Chisilamu.”

39:13

قُلۡ إِنِّيٓ أَخَافُ إِنۡ عَصَيۡتُ رَبِّي عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٍ

Nena, “Ndithudi ngati ine ndikapanda kumvera Ambuye wanga, ine ndimachita mantha ndi chilango cha tsiku loopsa.”

39:14

قُلِ ٱللَّهَ أَعۡبُدُ مُخۡلِصًا لَّهُۥ دِينِي

Nena, “Ndi Mulungu yekha amene ine ndimamupembedza ndi mtima wanga wonse.”

39:15

فَٱعۡبُدُواْ مَا شِئۡتُم مِّن دُونِهِۦۗ قُلۡ إِنَّ ٱلۡخَٰسِرِينَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَأَهۡلِيهِمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ أَلَا ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡخُسۡرَانُ ٱلۡمُبِينُ

Motero inu pembedzani aliyense amene mufuna kuonjezera pa Mulungu. “Ndithudi otayika ndi iwo amene adzataya miyoyo yawo ndi anthu awo pa tsiku lachiweruzo. Ndithudi kumeneku ndi kutayika kwenikweni.”

39:16

لَهُم مِّن فَوۡقِهِمۡ ظُلَلٌ مِّنَ ٱلنَّارِ وَمِن تَحۡتِهِمۡ ظُلَلٌۚ ذَٰلِكَ يُخَوِّفُ ٱللَّهُ بِهِۦ عِبَادَهُۥۚ يَٰعِبَادِ فَٱتَّقُونِ

Iwo adzakutidwa ndi moto pamwamba pawo ndi magawo a moto pansi pawo. Ndi chimenechi; Mulungu amaopseza akapolo ake. “Oh inu akapolo anga motero opani Ine.”

39:17

وَٱلَّذِينَ ٱجۡتَنَبُواْ ٱلطَّٰغُوتَ أَن يَعۡبُدُوهَا وَأَنَابُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ لَهُمُ ٱلۡبُشۡرَىٰۚ فَبَشِّرۡ عِبَادِ

Ndipo iwo amene sapembedza mafano ndipo amatembenukira kwa Mulungu molapa, iwo adzapeza nkhani zabwino. Kotero auze nkhani yabwino akapolo anga

39:18

ٱلَّذِينَ يَسۡتَمِعُونَ ٱلۡقَوۡلَ فَيَتَّبِعُونَ أَحۡسَنَهُۥٓۚ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ هَدَىٰهُمُ ٱللَّهُۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمۡ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Iwo amene amamva mawu anga ndipo adawatsatira, iwo ndiwo amene Mulungu wawatsogolera ndiponso iwo ndiwo anthu ozindikira

39:19

أَفَمَنۡ حَقَّ عَلَيۡهِ كَلِمَةُ ٱلۡعَذَابِ أَفَأَنتَ تُنقِذُ مَن فِي ٱلنَّارِ

Kodi iye amene chilango chake chagamulidwa mwachilungamo ndi wofanana ndi munthu wochimwa? Kodi iwe ungamupulumutse iye amene ali m’moto

39:20

لَٰكِنِ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ رَبَّهُمۡ لَهُمۡ غُرَفٌ مِّن فَوۡقِهَا غُرَفٌ مَّبۡنِيَّةٌ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ وَعۡدَ ٱللَّهِ لَا يُخۡلِفُ ٱللَّهُ ٱلۡمِيعَادَ

Koma iwo amene aopa Ambuye wawo ali ndi nyumba zokongola ndi zosanjikizana zimene zamangidwa ndipo pansi pake pamayenda mitsinje. Limeneli ndilo lonjezo la Mulungu ndipo Iye saphwanya lonjezo lake

39:21

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَسَلَكَهُۥ يَنَٰبِيعَ فِي ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ يُخۡرِجُ بِهِۦ زَرۡعًا مُّخۡتَلِفًا أَلۡوَٰنُهُۥ ثُمَّ يَهِيجُ فَتَرَىٰهُ مُصۡفَرًّا ثُمَّ يَجۡعَلُهُۥ حُطَٰمًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Kodi inu simuona mmene Mulungu amatumizira mvula kuchokera kumwamba ndipo amaisiya kuti ilowe pansi m’mitsinje? Mmene Iye amameretsera mbewu za maonekedwe osiyanasiyana zimene zimafota ndipo inu mumaziona zitasanduka zachikasu ndipo amazipanga izo kuti ziume ndi kuthetheka? Ndithudi mu zimenezi muli chikumbutso kwa anthu ozindikira

39:22

أَفَمَن شَرَحَ ٱللَّهُ صَدۡرَهُۥ لِلۡإِسۡلَٰمِ فَهُوَ عَلَىٰ نُورٍ مِّن رَّبِّهِۦۚ فَوَيۡلٌ لِّلۡقَٰسِيَةِ قُلُوبُهُم مِّن ذِكۡرِ ٱللَّهِۚ أُوْلَٰٓئِكَ فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ

Kodi iye amene Mulungu watsekula mtima wake kuti alowe Chisilamu ndi kuona kuwala kochokera kwa Ambuye wake ndi wofanana ndi munthu wouma mtima? Iyayi! Tsoka kwa iwo amene mitima yawo ndi yolimba pokumbukira Mulungu. Ndipo iwo ndi olakwa kwambiri

39:23

ٱللَّهُ نَزَّلَ أَحۡسَنَ ٱلۡحَدِيثِ كِتَٰبًا مُّتَشَٰبِهًا مَّثَانِيَ تَقۡشَعِرُّ مِنۡهُ جُلُودُ ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُمۡ ثُمَّ تَلِينُ جُلُودُهُمۡ وَقُلُوبُهُمۡ إِلَىٰ ذِكۡرِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ هُدَى ٱللَّهِ يَهۡدِي بِهِۦ مَن يَشَآءُۚ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٍ

Mulungu watumiza uthenga wabwino, Buku limene limabwerezabwereza chiphunzitso chake mosiyanasiyana. MatupiaiwoameneamaopaAmbuyewawo, amanjenjemera ndi Bukulo. Ndipo makungu ndi mitima yawo imafewa akamakumbukira Mulungu. Chimenechindichochilangizo cha Mulungu. Iye amatsogolera ndi icho aliyense amene Iye wamufuna. Koma iye amene Mulungu amamusiya kuti asochere, alibe wina woti angamutsogolere

39:24

أَفَمَن يَتَّقِي بِوَجۡهِهِۦ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ وَقِيلَ لِلظَّٰلِمِينَ ذُوقُواْ مَا كُنتُمۡ تَكۡسِبُونَ

Kodi iye amene adzapanga nkhope yake kukhala chishango cha chilango chowawa cha tsiku louka kwa akufa adzakhala wofanana ndi iye amene wapulumuka? Ndipo zidzanenedwa kwa anthu ochimwa kuti, “Lawani zipatso za ntchito zanu.”

39:25

كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَأَتَىٰهُمُ ٱلۡعَذَابُ مِنۡ حَيۡثُ لَا يَشۡعُرُونَ

Iwo amene adalipo kale nawonso adakana kotero chilango chidadza pa iwo kuchokera kumbali imene iwo sanali kuyembekezera

39:26

فَأَذَاقَهُمُ ٱللَّهُ ٱلۡخِزۡيَ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَكۡبَرُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ

Kotero Mulungu adawachititsa manyazi m’moyo uno koma chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chachikulu iwo akadadziwa

39:27

وَلَقَدۡ ضَرَبۡنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ مِن كُلِّ مَثَلٍ لَّعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ

Ndipo Ife tawaikira anthu, m’Buku la Korani, fanizo la mtundu uliwonse ndi cholinga chakuti azikumbukira

39:28

قُرۡءَانًا عَرَبِيًّا غَيۡرَ ذِي عِوَجٍ لَّعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ

Korani ya chiyankhulo cha Chiarabu, ndipo mulibe zinthu zolakwa, kuti iwo akhoza kulewa zoipa zimene Mulungu wawalamula

39:29

ضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلًا رَّجُلًا فِيهِ شُرَكَآءُ مُتَشَٰكِسُونَ وَرَجُلًا سَلَمًا لِّرَجُلٍ هَلۡ يَسۡتَوِيَانِ مَثَلًاۚ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Mulungu ali kupereka fanizo la kapolo amene ali ndi mabwana ambiri ndi kapolo amene ali ndi bwana mmodzi yekha. Kodi anthu awiriwa ndi ofanana m’machitidwe awo? Ulemerero ukhale kwa Mulungu! Koma anthu ambiri sadziwa

39:30

إِنَّكَ مَيِّتٌ وَإِنَّهُم مَّيِّتُونَ

Ndithudi iwe udzafa ndipo iwo adzafa

39:31

ثُمَّ إِنَّكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عِندَ رَبِّكُمۡ تَخۡتَصِمُونَ

Ndipo patsiku louka kwa akufa, nonse mudzatsutsana wina ndi mnzake pamaso pa Ambuye wanu

39:32

فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن كَذَبَ عَلَى ٱللَّهِ وَكَذَّبَ بِٱلصِّدۡقِ إِذۡ جَآءَهُۥٓۚ أَلَيۡسَ فِي جَهَنَّمَ مَثۡوًى لِّلۡكَٰفِرِينَ

Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa iye amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ndipo amakana choonadi pamene chidza kwa iye? Kodi ku Gahena kulibe malo okhalamo anthu osakhulupirira

39:33

وَٱلَّذِي جَآءَ بِٱلصِّدۡقِ وَصَدَّقَ بِهِۦٓ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُتَّقُونَ

Ndipo iye amene wabweretsa choonadi ndi amene adakhulupirira choonadi, ndithudi, amenewa ndiwo amene amachita bwino

39:34

لَهُم مَّا يَشَآءُونَ عِندَ رَبِّهِمۡۚ ذَٰلِكَ جَزَآءُ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Iwo adzapeza zonse zimene afuna kuchokera kwa Ambuye wawo. Imeneyi ndiyo mphotho ya anthu abwino

39:35

لِيُكَفِّرَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ أَسۡوَأَ ٱلَّذِي عَمِلُواْ وَيَجۡزِيَهُمۡ أَجۡرَهُم بِأَحۡسَنِ ٱلَّذِي كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Kuti Mulungu adzawakhululukira zoipitsitsa zimene amachita ndi kuwapatsa mphotho yawo molingana ndi ntchito zawo zabwino zimene adachita

39:36

أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِكَافٍ عَبۡدَهُۥۖ وَيُخَوِّفُونَكَ بِٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦۚ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٍ

Kodi Mulungu sakwana kuthandiza akapolo ake? Komabe iwo amayesetsa kukuopseza ndi milungu ina yoonjezera pa Iye. Ndipo aliyense amene Mulungu amusocheza alibe wina womutsogolera

39:37

وَمَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن مُّضِلٍّۗ أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِعَزِيزٍ ذِي ٱنتِقَامٍ

Ndipo iye amene Mulungu amamutsogolera palibe wina amene angamusocheze. Kodi Mulungu si wamphamvu zambiri ndiponso Ambuye wodziwa kubwezera

39:38

وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۚ قُلۡ أَفَرَءَيۡتُم مَّا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ إِنۡ أَرَادَنِيَ ٱللَّهُ بِضُرٍّ هَلۡ هُنَّ كَٰشِفَٰتُ ضُرِّهِۦٓ أَوۡ أَرَادَنِي بِرَحۡمَةٍ هَلۡ هُنَّ مُمۡسِكَٰتُ رَحۡمَتِهِۦۚ قُلۡ حَسۡبِيَ ٱللَّهُۖ عَلَيۡهِ يَتَوَكَّلُ ٱلۡمُتَوَكِّلُونَ

Ndipo, ndithudi, ngati ungawafunse kuti, “Kodi ndani adalenga kumwamba ndi dziko lapansi?” Ndithudi iwo adzayankha kuti, “Ndi Mulungu.” Nena, “Kodi zinthu zimene mumapembedza m’malo mwa Mulungu, ngati Mulungu afuna kugwetsa mavuto pa ine, kodi zinthuzo zingathe kuchotsa mavutowo? Kapena ngati Iye alangiza chisomo chake pa ine, kodi izo zingakanize chisomo chake?” Nena, “Mulungu ndi wokwana kwa ine. Mwa Iye onse okhulupirira ayenera kuika chikhulupiriro chawo.”

39:39

قُلۡ يَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَٰمِلٌۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Nena, “oh inu anthu anga! Gwirani ntchito yanu ndipo ine ndigwira yanga, ndipo inu mudzadziwa.”

39:40

مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٌ يُخۡزِيهِ وَيَحِلُّ عَلَيۡهِ عَذَابٌ مُّقِيمٌ

Iye amene alandira chilango chochititsa manyazi ndi iye amene alandira chilango chamuyaya

39:41

إِنَّآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ لِلنَّاسِ بِٱلۡحَقِّۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَلِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِوَكِيلٍ

Ndithudi tavumbulutsa kwa iwe Buku la ulangizi kwa anthu mwachoonadi. Kotero aliyense amene atsatira njira yoyenera amapulumutsa mzimu wake ndipo aliyense amene asochera alanga mzimu wake. Ndipo iwe sindiwe msungi wawo ayi

39:42

ٱللَّهُ يَتَوَفَّى ٱلۡأَنفُسَ حِينَ مَوۡتِهَا وَٱلَّتِي لَمۡ تَمُتۡ فِي مَنَامِهَاۖ فَيُمۡسِكُ ٱلَّتِي قَضَىٰ عَلَيۡهَا ٱلۡمَوۡتَ وَيُرۡسِلُ ٱلۡأُخۡرَىٰٓ إِلَىٰٓ أَجَلٍ مُّسَمًّىۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يَتَفَكَّرُونَ

Ndi Mulungu amene amachotsa mizimu ya anthu pa nthawi ya imfa ndi mizimu ya anthu a moyo akamagona. Iye amasunga mizimu ya amene adalamula kuti afe ndi kubweza mizimu ya ena mpaka nthawi yawo itakwana. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa iwo amene amaganiza kwambiri

39:43

أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ شُفَعَآءَۚ قُلۡ أَوَلَوۡ كَانُواْ لَا يَمۡلِكُونَ شَيۡـًٔا وَلَا يَعۡقِلُونَ

Kodi iwo asankha ena ngati a mkhalapakati poonjezera pa Mulungu? Nena, “Ngakhale kuti iwo alibe mphamvu iliyonse ndiponso alibe nzeru?”

39:44

قُل لِّلَّهِ ٱلشَّفَٰعَةُ جَمِيعًاۖ لَّهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ ثُمَّ إِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ

Nena “Mphamvu zonse za mkhalapakati zili m’manja mwa Mulungu. Iye ndiye Mwini wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo ndi kwa Iye kumene mudzabwerera.”

39:45

وَإِذَا ذُكِرَ ٱللَّهُ وَحۡدَهُ ٱشۡمَأَزَّتۡ قُلُوبُ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِۖ وَإِذَا ذُكِرَ ٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦٓ إِذَا هُمۡ يَسۡتَبۡشِرُونَ

Ndipo pamene dzina la Mulungu lokha litchulidwa, mitima ya iwo amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza imakhumudwa koma pamene milungu ina kupatula Mulungu weniweni itchulidwa, iwo amasangalala kwambiri

39:46

قُلِ ٱللَّهُمَّ فَاطِرَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ عَٰلِمَ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ أَنتَ تَحۡكُمُ بَيۡنَ عِبَادِكَ فِي مَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ

Nena, “oh Mulungu! Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi, Wodziwa zobisika ndi zooneka! Inu mudzaweruza pakati pa akapolo anu pa zimene amatsutsana.”

39:47

وَلَوۡ أَنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ مَا فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعًا وَمِثۡلَهُۥ مَعَهُۥ لَٱفۡتَدَوۡاْ بِهِۦ مِن سُوٓءِ ٱلۡعَذَابِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ وَبَدَا لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مَا لَمۡ يَكُونُواْ يَحۡتَسِبُونَ

Ngakhale anthu ochita zoipa akadakhala ndi zinthu zonse zimene zili pa dziko lapansi kapena zochuluka kuonjezera pa izi, ndithudi iwo akadazipereka izo ngati dipo kuti ziwapulumutse ku zowawa za chilango cha tsiku lachiweruzo. Ndipo chimene samachiganizira, chidzasonyezedwa kwa iwo ndi Mulungu

39:48

وَبَدَا لَهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا كَسَبُواْ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ

Mphotho za ntchito zawo zonse zoipa zidzaonekera poyera ndipo zonse zimene amazinyoza zidzawazungulira iwo

39:49

فَإِذَا مَسَّ ٱلۡإِنسَٰنَ ضُرٌّ دَعَانَا ثُمَّ إِذَا خَوَّلۡنَٰهُ نِعۡمَةً مِّنَّا قَالَ إِنَّمَآ أُوتِيتُهُۥ عَلَىٰ عِلۡمِۭۚ بَلۡ هِيَ فِتۡنَةٌ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ

Pamene vuto ligwa pa munthu, iye amatipempha Ife, koma pamene timuonetsa chifundo chathu, iye amati, “Izi zapatsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru zanga.” Iyayi! Awa ndi mayesero chabe koma ambiri a iwo sadziwa chilichonse

39:50

قَدۡ قَالَهَا ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ

Ndithudi iwo amene adalipo kale anali kunena chimodzimodzi koma chilichonse chimene anali kuchita chidali chopanda phindu kwa iwo

39:51

فَأَصَابَهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا كَسَبُواْۚ وَٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡ هَٰٓؤُلَآءِ سَيُصِيبُهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا كَسَبُواْ وَمَا هُم بِمُعۡجِزِينَ

Motero zoipa zimene adachita zidawatsata iwo. Ndipo iwo ochita zoipa a m’badwo uno zotsatira za ntchito zawo zidzawapeza ndipo iwo sadzatha kuthawa ayi

39:52

أَوَلَمۡ يَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يُؤۡمِنُونَ

Kodi iwo sadziwa kuti Mulungu amapereka moolowa manja kapena monyalapsa kwa aliyense amene Iye wamufuna? Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa iwo amene ama amakhulupirira

39:53

قُلۡ يَٰعِبَادِيَ ٱلَّذِينَ أَسۡرَفُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ لَا تَقۡنَطُواْ مِن رَّحۡمَةِ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَغۡفِرُ ٱلذُّنُوبَ جَمِيعًاۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ

Nena, “Oh akapolo anga amene mwalakwira mizimu yanu! Musakayike za chisomo cha Mulungu. Ndithudi Mulungu amakhululukira machimo onse. Ndithudi Iye amakhululukira nthawi zonse ndipo ndiye Mwini chisoni chosatha.”

39:54

وَأَنِيبُوٓاْ إِلَىٰ رَبِّكُمۡ وَأَسۡلِمُواْ لَهُۥ مِن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَكُمُ ٱلۡعَذَابُ ثُمَّ لَا تُنصَرُونَ

Lapani kwa Ambuye wanu nthawi ndi nthawi ndipo mudzipereke kwathunthu kwa Iye chilango chisanadze kwa inu chifukwa sipadzakhala wina wothandiza inu

39:55

وَٱتَّبِعُوٓاْ أَحۡسَنَ مَآ أُنزِلَ إِلَيۡكُم مِّن رَّبِّكُم مِّن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَكُمُ ٱلۡعَذَابُ بَغۡتَةً وَأَنتُمۡ لَا تَشۡعُرُونَ

Ndipotsatiranizabwinozonsezimenezavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu chilango chake chisanadze kwa inu mwadzidzidzi pamene inu simuli kuchiganizira

39:56

أَن تَقُولَ نَفۡسٌ يَٰحَسۡرَتَىٰ عَلَىٰ مَا فَرَّطتُ فِي جَنۢبِ ٱللَّهِ وَإِن كُنتُ لَمِنَ ٱلسَّٰخِرِينَ

Mwina mzimu ungadzanene kuti, “Oh tsoka kwa ine chifukwa chakulephera kwanga pokwaniritsa udindo wanga kwa Mulungu! Ndithudi ine ndidali mmodzi wa iwo amene anali kunyoza.”

39:57

أَوۡ تَقُولَ لَوۡ أَنَّ ٱللَّهَ هَدَىٰنِي لَكُنتُ مِنَ ٱلۡمُتَّقِينَ

Kapena akhoza kunena kuti, “Akadakhala kuti Mulungu adanditsogolera, ndithudi, ine ndikadakhala m’gulu la anthu angwiro.”

39:58

أَوۡ تَقُولَ حِينَ تَرَى ٱلۡعَذَابَ لَوۡ أَنَّ لِي كَرَّةً فَأَكُونَ مِنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Kapena pamene aona akhoza kunena chilango kuti, “N’kadakhala ndidali ndi mwayi wina, ndithudi, ndikadakhala m’gulu la iwo ochita zabwino.”

39:59

بَلَىٰ قَدۡ جَآءَتۡكَ ءَايَٰتِي فَكَذَّبۡتَ بِهَا وَٱسۡتَكۡبَرۡتَ وَكُنتَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Inde! Ndithudi ulangizi wanga unadza kwa inu koma inu munaukana. Inu munali kunyada ndipo munali m’gulu la anthu osakhulupirira

39:60

وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ تَرَى ٱلَّذِينَ كَذَبُواْ عَلَى ٱللَّهِ وُجُوهُهُم مُّسۡوَدَّةٌۚ أَلَيۡسَ فِي جَهَنَّمَ مَثۡوًى لِّلۡمُتَكَبِّرِينَ

Ndipo patsiku louka kwa akufa, iwe udzaona nkhope zonse za amene amanamizira Mulungu, zitadetsedwa. Kodi ku Gahena kulibe malo okhalako anthu a mwano

39:61

وَيُنَجِّي ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ بِمَفَازَتِهِمۡ لَا يَمَسُّهُمُ ٱلسُّوٓءُ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ

Ndipo Mulungu adzapereka onse amene amalewa zoipa ku malo awo opambana. Palibe choipa chimene chidzagwa pa iwo, ndipo iwo sadzamva chisoni ayi

39:62

ٱللَّهُ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٍۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ وَكِيلٌ

Mulungu ndiye Namalenga wa zinthu zonse, Wosamalira ndiponso Mgawi wa zinthu zonse

39:63

لَّهُۥ مَقَالِيدُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ

Chake ndi chuma chonse cha kumwamba ndi cha padziko lapansi. Ndipo iwo amene sakhulupirira muchivumbulutso cha Mulungu, amenewo ndiwo amene adzakhala olephera

39:64

قُلۡ أَفَغَيۡرَ ٱللَّهِ تَأۡمُرُوٓنِّيٓ أَعۡبُدُ أَيُّهَا ٱلۡجَٰهِلُونَ

Nena, “Kodi inu muli kundilamula kuti ndipembedze wina wake osati Mulungu? Oh inu anthu osadziwa!”

39:65

وَلَقَدۡ أُوحِيَ إِلَيۡكَ وَإِلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكَ لَئِنۡ أَشۡرَكۡتَ لَيَحۡبَطَنَّ عَمَلُكَ وَلَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ

Ndipo, ndithudi, zavumbulutsidwa kwa iwe ndi kwa iwo amene adalipo kale kuti, “Ndithudi ngati inu muphatikiza Mulungu ndi china chake, ndithudi, ntchito zanu zidzakhala zopanda phindu. Ndithudi inu mudzakhala m’gulu la anthu olephera.”

39:66

بَلِ ٱللَّهَ فَٱعۡبُدۡ وَكُن مِّنَ ٱلشَّٰكِرِينَ

Iyayi! Koma iwe upembedze Mulungu m’modzi yekha ndipo khala m’gulu la iwo amene amathokoza

39:67

وَمَا قَدَرُواْ ٱللَّهَ حَقَّ قَدۡرِهِۦ وَٱلۡأَرۡضُ جَمِيعًا قَبۡضَتُهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَٱلسَّمَٰوَٰتُ مَطۡوِيَّٰتُۢ بِيَمِينِهِۦۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ

Ndipo iwo sadamulemekeze Mulungu ndi ulemu umene uli woyenera kwa Iye ndipo dziko lapansi lidzakhala pa chikhato pake pa tsiku lachiweruzo. Kumwamba kudzakulungidwa m’dzanja lake lamanja. Ulemerero ukhale kwa Iye ndipo Iye ndi woposa mafano amene amamufanizira nawo

39:68

وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَصَعِقَ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا مَن شَآءَ ٱللَّهُۖ ثُمَّ نُفِخَ فِيهِ أُخۡرَىٰ فَإِذَا هُمۡ قِيَامٌ يَنظُرُونَ

Ndipo lipenga lidzalizidwa kotero onse amene ali kumwamba ndi onse amene ali padziko lapansi adzakomoka kupatula okhawo amene Mulungu wawafuna. Ndipo lidzalizidwanso kachiwiri ndipo onse adzakhala choimirira ndi kumangoyembekezera

39:69

وَأَشۡرَقَتِ ٱلۡأَرۡضُ بِنُورِ رَبِّهَا وَوُضِعَ ٱلۡكِتَٰبُ وَجِاْيٓءَ بِٱلنَّبِيِّـۧنَ وَٱلشُّهَدَآءِ وَقُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡحَقِّ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ

Ndipo dziko lapansi lidzawala ndi muuni wa Ambuye wako ndipo Buku lidzatsekulidwa. Atumwi ndi mboni zidzaitanidwa ndipo chiweruzo chidzaperekedwa mwachilungamo pakati pawo ndipo iwo sadzaponderezedwa konse

39:70

وَوُفِّيَتۡ كُلُّ نَفۡسٍ مَّا عَمِلَتۡ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِمَا يَفۡعَلُونَ

Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa mokwanira molingana ndi zimene udachita ndipo Iye amadziwa bwino zonse zimene mumachita

39:71

وَسِيقَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِلَىٰ جَهَنَّمَ زُمَرًاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُوهَا فُتِحَتۡ أَبۡوَٰبُهَا وَقَالَ لَهُمۡ خَزَنَتُهَآ أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ رُسُلٌ مِّنكُمۡ يَتۡلُونَ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِ رَبِّكُمۡ وَيُنذِرُونَكُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَاۚ قَالُواْ بَلَىٰ وَلَٰكِنۡ حَقَّتۡ كَلِمَةُ ٱلۡعَذَابِ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ

Ndipo onse osakhulupirira adzatengedwa paulendo wa ku Gahena m’magulumagulu ndipo pamene azidzafika pafupi, makomo ake adzatsekulidwa ndipo oyang’anira kumeneko adzati kwa iwo, “Kodi sikunadze kwa inu Atumwi a mtundu wanu kukulalikirani ulangizi wa Ambuye wanu ndi kukuchenjezani za kukumana kwanu ndi tsiku lino?” Iwo adzati, “Inde!” Koma chilango chakwaniritsidwa kwa anthu osakhulupirira

39:72

قِيلَ ٱدۡخُلُوٓاْ أَبۡوَٰبَ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَاۖ فَبِئۡسَ مَثۡوَى ٱلۡمُتَكَبِّرِينَ

Iwo adzauzidwa kuti, “Lowani nonse m’zipata za Gahena kuti muzikhala m’menemo.” Ndipo ndi oipa malowa womwe anthu onyada adzakhaleko

39:73

وَسِيقَ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ رَبَّهُمۡ إِلَى ٱلۡجَنَّةِ زُمَرًاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُوهَا وَفُتِحَتۡ أَبۡوَٰبُهَا وَقَالَ لَهُمۡ خَزَنَتُهَا سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡ طِبۡتُمۡ فَٱدۡخُلُوهَا خَٰلِدِينَ

Ndipo onse amene amaopa Ambuye wawo adzatsogozedwa ku Paradiso m’magulumagulu. Ndipo pamene iwo azidzafika pafupi, taonani makomo azipata adzatsekulidwa, ndipo oyang’anira kumeneko adzati, “Mtendere ukhale kwa inu!” Inu mudzakhala mosangalala kotero lowani kuti muzikhala momwemo.”

39:74

وَقَالُواْ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي صَدَقَنَا وَعۡدَهُۥ وَأَوۡرَثَنَا ٱلۡأَرۡضَ نَتَبَوَّأُ مِنَ ٱلۡجَنَّةِ حَيۡثُ نَشَآءُۖ فَنِعۡمَ أَجۡرُ ٱلۡعَٰمِلِينَ

Ndipo iwo adzati, “Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene wakwaniritsa kwa ife lonjezo lake ndipo watilola ife kuti tikhale m’dziko ili. Ife tidzakhala m’minda imene tifuna.” Kotero yabwino ndi mphotho ya anthu ogwira ntchito zabwino

39:75

وَتَرَى ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ حَآفِّينَ مِنۡ حَوۡلِ ٱلۡعَرۡشِ يُسَبِّحُونَ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡۚ وَقُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡحَقِّۚ وَقِيلَ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo iwe udzaona angelo atazungulira Mpando Wachifumu mbali zonse, ali kuimba mayamiko ndi kulemekeza Ambuye wawo. Ndipo chiweruzo chidzaperekedwa kwa zolengedwa zonse mwachilungamo ndipo kudzanenedwa kuti, “Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse.” Sura 40 • al-mu’min

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.