Surah 38 · 88 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Sad in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

38:1

صٓۚ وَٱلۡقُرۡءَانِ ذِي ٱلذِّكۡرِ

Suad. Pali Korani yodzadza ndi chikumbutso

38:2

بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي عِزَّةٍ وَشِقَاقٍ

Iyayi! anthu osakhulupirira ali kungodzikundikira ndi kumangotsutsa

38:3

كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّن قَرۡنٍ فَنَادَواْ وَّلَاتَ حِينَ مَنَاصٍ

Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga iwo asanadze ndipo iyo idalira poona kuti padalibe nthawi yothawa

38:4

وَعَجِبُوٓاْ أَن جَآءَهُم مُّنذِرٌ مِّنۡهُمۡۖ وَقَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا سَٰحِرٌ كَذَّابٌ

Ndipo iwo ali kudabwa kuti Mtumwi wadza kwa iwo kuchokera pakati pawo. Ndipo anthu osakhulupirira amati, “Uyu ndi munthu wamatsenga ndiponso wabodza!”

38:5

أَجَعَلَ ٱلۡأٓلِهَةَ إِلَٰهًا وَٰحِدًاۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ عُجَابٌ

“Kodi iye wapanga milungu yonse kukhala Mulungu mmodzi? Ndithudi ichi ndi chinthu chachilendo.”

38:6

وَٱنطَلَقَ ٱلۡمَلَأُ مِنۡهُمۡ أَنِ ٱمۡشُواْ وَٱصۡبِرُواْ عَلَىٰٓ ءَالِهَتِكُمۡۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ يُرَادُ

Ndipo atsogoleri awo amachoka monyinyirika nati, “Pitirizani inu ndipo mudzipereke kwathunthu kwa milungu yanu! Ndithudi ichi ndi chinthu choti chikusokonezani.”

38:7

مَا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِي ٱلۡمِلَّةِ ٱلۡأٓخِرَةِ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا ٱخۡتِلَٰقٌ

“Ife sitidamvepo zimenezi pakati pa anthu akale. Ichi si china koma nkhani zopeka chabe.”

38:8

أَءُنزِلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ مِنۢ بَيۡنِنَاۚ بَلۡ هُمۡ فِي شَكٍّ مِّن ذِكۡرِيۚ بَل لَّمَّا يَذُوقُواْ عَذَابِ

“Kodi uthenga wavumbulutsidwa kwa iye yekha pakati pathu?” Iyayi! Koma iwo ali kukayika za uthenga wanga. Iyayi! Iwo sadalawepo chilango changa

38:9

أَمۡ عِندَهُمۡ خَزَآئِنُ رَحۡمَةِ رَبِّكَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡوَهَّابِ

Kapena iwo ndi nkhokwe za chifundo cha Ambuye wako, Mwini Mphamvu zonse, Mwini kupereka zabwino zonse

38:10

أَمۡ لَهُم مُّلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَاۖ فَلۡيَرۡتَقُواْ فِي ٱلۡأَسۡبَٰبِ

Kapena iwo ali ndi ulamuliro kumwamba ndi padziko ndi kuti zonse zimene zili m’menemo ndi zawo? Ngati nditero, alekeni iwo kuti akwere mothandizidwa

38:11

جُندٌ مَّا هُنَالِكَ مَهۡزُومٌ مِّنَ ٱلۡأَحۡزَابِ

Iwo adzagonjetsedwa monga magulu akale

38:12

كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٍ وَعَادٌ وَفِرۡعَوۡنُ ذُو ٱلۡأَوۡتَادِ

Asanadze iwo, panali ena amene adakana Atumwi. Anthu a Nowa, a Aad, ndi a Farawo, mfumu ya zisonga

38:13

وَثَمُودُ وَقَوۡمُ لُوطٍ وَأَصۡحَٰبُ لۡـَٔيۡكَةِۚ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡأَحۡزَابُ

Thamoud ndi anthu a Loti ndi anthu okhala m’nkhalango, onsewa adali wothandizana

38:14

إِن كُلٌّ إِلَّا كَذَّبَ ٱلرُّسُلَ فَحَقَّ عِقَابِ

Panalibe mmodzi amene sadanene kuti Atumwi adali abodza, motero chilango changa chinali chowayenera

38:15

وَمَا يَنظُرُ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا صَيۡحَةً وَٰحِدَةً مَّا لَهَا مِن فَوَاقٍ

Ndipo awa ali kungodikira kulira kumodzi kokha kumene kuchitike mosachedwa

38:16

وَقَالُواْ رَبَّنَا عَجِّل لَّنَا قِطَّنَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ

Iwo amati, “Ambuye wathu, bweretsani msanga kwa ife Buku la ntchito zathu ngakhale nthawi yake siinakwane.”

38:17

ٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَٱذۡكُرۡ عَبۡدَنَا دَاوُۥدَ ذَا ٱلۡأَيۡدِۖ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ

Khala wopirira pa zimene ali kunena ndipo uzikumbukira kapolo wathu Davide, munthu wamphamvu. Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse

38:18

إِنَّا سَخَّرۡنَا ٱلۡجِبَالَ مَعَهُۥ يُسَبِّحۡنَ بِٱلۡعَشِيِّ وَٱلۡإِشۡرَاقِ

Ndithudi Ife tidauza mapiri kuti aziyimba pamodzi ndi iye mayamiko athu nthawi ya madzulo ndi m’mbandakucha

38:19

وَٱلطَّيۡرَ مَحۡشُورَةًۖ كُلٌّ لَّهُۥٓ أَوَّابٌ

Ndipo mbalame zidasonkhana, zonse pamodzi ndi iye zidalemekeza Mulungu

38:20

وَشَدَدۡنَا مُلۡكَهُۥ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحِكۡمَةَ وَفَصۡلَ ٱلۡخِطَابِ

Tidalimbikitsa Ufumu wake ndipo tidamupatsa nzeru ndi kuweruza kwabwino m’manenedwe ndi m’chiweruzo

38:21

وَهَلۡ أَتَىٰكَ نَبَؤُاْ ٱلۡخَصۡمِ إِذۡ تَسَوَّرُواْ ٱلۡمِحۡرَابَ

Kodi nkhani ya anthu okangana yakupeza iwe? Pamene, iwo adakwera chipupa cha nyumba ndi kulowa mnyumba ya padera

38:22

إِذۡ دَخَلُواْ عَلَىٰ دَاوُۥدَ فَفَزِعَ مِنۡهُمۡۖ قَالُواْ لَا تَخَفۡۖ خَصۡمَانِ بَغَىٰ بَعۡضُنَا عَلَىٰ بَعۡضٍ فَٱحۡكُم بَيۡنَنَا بِٱلۡحَقِّ وَلَا تُشۡطِطۡ وَٱهۡدِنَآ إِلَىٰ سَوَآءِ ٱلصِّرَٰطِ

Pamene adalowa kwa Davide, iye adachita mantha ndi iwo ndipo iwo adati, “Usaope. Ife ndife anthu okangana, ndipo wina wa ife wachimwira mnzake motero weruza mwachilungamo ndipo usatiweruze opanda chilungamo koma titsogolere ku njira yoyenera.”

38:23

إِنَّ هَٰذَآ أَخِي لَهُۥ تِسۡعٌ وَتِسۡعُونَ نَعۡجَةً وَلِيَ نَعۡجَةٌ وَٰحِدَةٌ فَقَالَ أَكۡفِلۡنِيهَا وَعَزَّنِي فِي ٱلۡخِطَابِ

“Ndithudi uyu ndi m’bale wanga ndipo ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zisanu ndi zinayi pamene ine ndili ndi nkhosa imodzi yokha basi. Komabe iye akuti, ‘Undipatse ine nkhosayo’ ndipo iye adandipambana mu zonena zake.”

38:24

قَالَ لَقَدۡ ظَلَمَكَ بِسُؤَالِ نَعۡجَتِكَ إِلَىٰ نِعَاجِهِۦۖ وَإِنَّ كَثِيرًا مِّنَ ٱلۡخُلَطَآءِ لَيَبۡغِي بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍ إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَقَلِيلٌ مَّا هُمۡۗ وَظَنَّ دَاوُۥدُ أَنَّمَا فَتَنَّٰهُ فَٱسۡتَغۡفَرَ رَبَّهُۥ وَخَرَّۤ رَاكِعًاۤ وَأَنَابَ

Iye adati, “Ndithudi iye wakulakwira kwambiri pokupempha kuti nkhosa yako imodzi yokha iperekedwe kwa iye kuonjezera pa zimene ali nazo.” Ndithudi anthu ambiri ochitira pamodzi malonda ndi amene akulakwirana wina ndi mnzake. Koma izi sizichitika ndi anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndipo anthu otere ndi ochepa. Ndipo Davide adazindikira kuti Ife tidamuyesa iye ndipo adapempha chikhululukiro kwa Ambuye wake ndipo iye adagwa nagunditsa mphumi yake pansi ndi kudza molapa

38:25

فَغَفَرۡنَا لَهُۥ ذَٰلِكَۖ وَإِنَّ لَهُۥ عِندَنَا لَزُلۡفَىٰ وَحُسۡنَ مَـَٔابٍ

Kotero Ife tidamukhululukira ndipo ndithudi adali kufupi ndi Ife ndipo ali ndi malo okongola pa nthawi yobwerera

38:26

يَٰدَاوُۥدُ إِنَّا جَعَلۡنَٰكَ خَلِيفَةً فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱحۡكُم بَيۡنَ ٱلنَّاسِ بِٱلۡحَقِّ وَلَا تَتَّبِعِ ٱلۡهَوَىٰ فَيُضِلَّكَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَضِلُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ لَهُمۡ عَذَابٌ شَدِيدُۢ بِمَا نَسُواْ يَوۡمَ ٱلۡحِسَابِ

Iwe Davide! Ndithudi Ife takukhazika iwe kukhala Kazembe padziko lapansi motero weruza pakati pa anthu mwachilungamo, ndipo usatsatire zilakolako za mtima wako chifukwa zidzakusocheretsa ku njira ya Mulungu. Ndithudi iwo amene asochera ku njira ya Mulungu adzalangidwa kwambiri chifukwa iwo amaiwala za tsiku lachiweruzo

38:27

وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَآءَ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا بَٰطِلًاۚ ذَٰلِكَ ظَنُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۚ فَوَيۡلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنَ ٱلنَّارِ

Si kuti tidasowa chochita polenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’kati mwake! Amenewo adali maganizo a anthu osakhulupirira! Ndipo tsoka kwa anthu osakhulupirira lochokera ku moto

38:28

أَمۡ نَجۡعَلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ كَٱلۡمُفۡسِدِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ نَجۡعَلُ ٱلۡمُتَّقِينَ كَٱلۡفُجَّارِ

Kodi Ife tingasamale mofanana anthu okhulupirira ndi ochita ntchito zabwino ndi iwo amene amadzetsa chisokonezo pa dziko? Kapena Ife tingasamalire anthu amene amalewa zoipa chimodzimodzi ndi iwo amene amachita zoipa

38:29

كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ إِلَيۡكَ مُبَٰرَكٌ لِّيَدَّبَّرُوٓاْ ءَايَٰتِهِۦ وَلِيَتَذَكَّرَ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Ili ndi Buku limene Ife tatumiza kwa iwe, lodzala ndi madalitso kuti akhoza kuganiza mofatsa pa mavesi ake ndi kuti anthu ozindikira akhoza kukumbukira

38:30

وَوَهَبۡنَا لِدَاوُۥدَ سُلَيۡمَٰنَۚ نِعۡمَ ٱلۡعَبۡدُ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ

Kwa Davide Ife tidamupatsa Solomoni. Kapolo wabwino zedi! Ndithudi iye anali kudzalapa kwa Ife

38:31

إِذۡ عُرِضَ عَلَيۡهِ بِٱلۡعَشِيِّ ٱلصَّٰفِنَٰتُ ٱلۡجِيَادُ

Ndipo pamene adadza nazo kwa iye, nthawi ya madzulo, Hatchi zophunzitsidwa bwino zamphamvu ndi zoberekedwa bwino

38:32

فَقَالَ إِنِّيٓ أَحۡبَبۡتُ حُبَّ ٱلۡخَيۡرِ عَن ذِكۡرِ رَبِّي حَتَّىٰ تَوَارَتۡ بِٱلۡحِجَابِ

Ndipo iye adati, “Ndithudi ine ndidakonda chuma kuposa kukumbukira Ambuye wanga. Mpaka pamene nthawi idatha ndipo dzuwa lidalowa mu mdima.”

38:33

رُدُّوهَا عَلَيَّۖ فَطَفِقَ مَسۡحَۢا بِٱلسُّوقِ وَٱلۡأَعۡنَاقِ

Ndipo iye adati “Bweretsani mahatchi kwa ine.” Ndipo iye adayamba kuzisisita miyendo ndi makosi awo

38:34

وَلَقَدۡ فَتَنَّا سُلَيۡمَٰنَ وَأَلۡقَيۡنَا عَلَىٰ كُرۡسِيِّهِۦ جَسَدًا ثُمَّ أَنَابَ

Ndipo, ndithudi, Ife tidamuyesa Solomoni ndipo Ife tidaika Satana pa mpando wake wachifumu koma iye adadza kwa Ife modzipereka ndi molapa

38:35

قَالَ رَبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَهَبۡ لِي مُلۡكًا لَّا يَنۢبَغِي لِأَحَدٍ مِّنۢ بَعۡدِيٓۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡوَهَّابُ

Iye adati, “Ambuye wanga! Khululukireni ndipo ndipatseni ufumu umene simudzapatsanso wina pambuyo panga chifukwa inu mumapereka zokoma zanu mopanda muyeso.”

38:36

فَسَخَّرۡنَا لَهُ ٱلرِّيحَ تَجۡرِي بِأَمۡرِهِۦ رُخَآءً حَيۡثُ أَصَابَ

Ndipo Ife tidamuchepetsera mphamvu yakuti mphepo imvere malamulo ake kuti iziyenda potsatira malamulo ake amene iye adalamula

38:37

وَٱلشَّيَٰطِينَ كُلَّ بَنَّآءٍ وَغَوَّاصٍ

Ndiponso a Satana ochokera kwa majini ndi m’misiri aliyense womanga nyumba ndi wodziwa kusambira pa madzi

38:38

وَءَاخَرِينَ مُقَرَّنِينَ فِي ٱلۡأَصۡفَادِ

Ndi ena omwe ndi omangidwa ku magoli

38:39

هَٰذَا عَطَآؤُنَا فَٱمۡنُنۡ أَوۡ أَمۡسِكۡ بِغَيۡرِ حِسَابٍ

Iyi ndi mphatso yathu yaulere, kotero pereka mowolowa manja kapena kuisunga. Iwe siudzaimbidwa mlandu

38:40

وَإِنَّ لَهُۥ عِندَنَا لَزُلۡفَىٰ وَحُسۡنَ مَـَٔابٍ

Ndipo ndithudi iye adali pafupi ndi Ife, ndi kubwera ku malo abwino

38:41

وَٱذۡكُرۡ عَبۡدَنَآ أَيُّوبَ إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَسَّنِيَ ٱلشَّيۡطَٰنُ بِنُصۡبٍ وَعَذَابٍ

Ndipo kumbukira kapolo wathu Yobu pamene adapempha kwa Ambuye wake kuti, “Satana wandikundikira mavuto ndi masautso.”

38:42

ٱرۡكُضۡ بِرِجۡلِكَۖ هَٰذَا مُغۡتَسَلُۢ بَارِدٌ وَشَرَابٌ

“Menya nthaka ndi phazi lako. Uyu ndi kasupe wa madzi oti usambe, ozizira ndi okoma pakumwa.”

38:43

وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ أَهۡلَهُۥ وَمِثۡلَهُم مَّعَهُمۡ رَحۡمَةً مِّنَّا وَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Ndipo Ife tidamubwezera banja lake ndi kuonjezera chiwerengero chawo ngati chisomo chochokera kwa Ife ndiponso chikumbutso kwa anthu ozindikira

38:44

وَخُذۡ بِيَدِكَ ضِغۡثًا فَٱضۡرِب بِّهِۦ وَلَا تَحۡنَثۡۗ إِنَّا وَجَدۡنَٰهُ صَابِرًاۚ نِّعۡمَ ٱلۡعَبۡدُ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ

Ndipo nyamula m’manja mwako mtolo wa udzu ochepa ndipo mumenye nawo koma usaphwanye lonjezo lako. Ndithudi! Ife tidamupeza ali wopirira kwambiri ndi okhazikika. Ndithudi iye adali Mtumwi wabwino! Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse

38:45

وَٱذۡكُرۡ عِبَٰدَنَآ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ أُوْلِي ٱلۡأَيۡدِي وَٱلۡأَبۡصَٰرِ

Ndipo kumbukira akapolo athu Abrahamu, Isake, Yakobo ameneadaliodzalandimphamvundiponsoomvetsa zinthu za chipembedzo

38:46

إِنَّآ أَخۡلَصۡنَٰهُم بِخَالِصَةٍ ذِكۡرَى ٱلدَّارِ

Ndithudi tidawasankha iwo ndi kuwapatsa chikumbumtima chamoyo umene uli nkudza

38:47

وَإِنَّهُمۡ عِندَنَا لَمِنَ ٱلۡمُصۡطَفَيۡنَ ٱلۡأَخۡيَارِ

Ndipo iwo timawaona. Ndithudi ali m’gulu la anthu odziwika ndi abwino

38:48

وَٱذۡكُرۡ إِسۡمَٰعِيلَ وَٱلۡيَسَعَ وَذَا ٱلۡكِفۡلِۖ وَكُلٌّ مِّنَ ٱلۡأَخۡيَارِ

Ndipo kumbukira Ishimayeli, Elisa, ndi Dhul-Kifl onse adali m’gulu la anthu ochita zabwino

38:49

هَٰذَا ذِكۡرٌۚ وَإِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ لَحُسۡنَ مَـَٔابٍ

Ichi ndi chikumbutso, ndithudi, kwa anthu olungama awo ndi malo abwino

38:50

جَنَّٰتِ عَدۡنٍ مُّفَتَّحَةً لَّهُمُ ٱلۡأَبۡوَٰبُ

Minda yosatha imene makomo ake adzakhalaotsekulidwakwaiwonthawizonse

38:51

مُتَّكِـِٔينَ فِيهَا يَدۡعُونَ فِيهَا بِفَٰكِهَةٍ كَثِيرَةٍ وَشَرَابٍ

M’menemo iwo adzakhala mwamtendere ndiponso m’menemo iwo adzaitanitsa zipatso zochuluka ndi zakumwa zokoma

38:52

وَعِندَهُمۡ قَٰصِرَٰتُ ٱلطَّرۡفِ أَتۡرَابٌ

Ndipo pambali pawo padzakhala a namwali angwiro ongoyang’ana maso awo pa amuna ofanana nawo zaka

38:53

هَٰذَا مَا تُوعَدُونَ لِيَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ

Limeneli ndi lonjezo limene lapatsidwa kwa inu lokhudza tsiku lachiweruzo

38:54

إِنَّ هَٰذَا لَرِزۡقُنَا مَا لَهُۥ مِن نَّفَادٍ

Ndithudi zimenezi ndi zokoma zathu kwa inu ndipo sizidzatha ayi

38:55

هَٰذَاۚ وَإِنَّ لِلطَّٰغِينَ لَشَرَّ مَـَٔابٍ

Izi zili choncho. Ndipo zoonadi anthu ochita zoipa adzakhala ku malo oipa kupitako

38:56

جَهَنَّمَ يَصۡلَوۡنَهَا فَبِئۡسَ ٱلۡمِهَادُ

Gahena! Ndi kumene iwo adzalowa ndipo ndi malo oipa kukhalamo

38:57

هَٰذَا فَلۡيَذُوقُوهُ حَمِيمٌ وَغَسَّاقٌ

Izi zili choncho! Kotero alekeni iwo alawe madzi owira ndi mafinya

38:58

وَءَاخَرُ مِن شَكۡلِهِۦٓ أَزۡوَٰجٌ

Ndi zilango zina zofanana zawo ndi zina zosiyanasiyana

38:59

هَٰذَا فَوۡجٌ مُّقۡتَحِمٌ مَّعَكُمۡ لَا مَرۡحَبَۢا بِهِمۡۚ إِنَّهُمۡ صَالُواْ ٱلنَّارِ

Ili ndi gulu la nkhondo limene lili kulowa ndi inu! Palibe kulandiridwa kwabwino kwa iwo! Ndithudi iwo adzalowa kumoto

38:60

قَالُواْ بَلۡ أَنتُمۡ لَا مَرۡحَبَۢا بِكُمۡۖ أَنتُمۡ قَدَّمۡتُمُوهُ لَنَاۖ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرَارُ

Iwo adzati, “Iyayi! Inunso. Simulandiridwa ayi. Ndinu amene mudatinyenga ife, kotero awa ndiwo malo oipa kwambiri kukhalako.”

38:61

قَالُواْ رَبَّنَا مَن قَدَّمَ لَنَا هَٰذَا فَزِدۡهُ عَذَابًا ضِعۡفًا فِي ٱلنَّارِ

Iwo adzati, “Ambuye wathu! Aliyense amene adachititsa kuti zimenezi zidze kwa ife muonjezereni kawiri chilango chake cha kumoto.”

38:62

وَقَالُواْ مَا لَنَا لَا نَرَىٰ رِجَالًا كُنَّا نَعُدُّهُم مِّنَ ٱلۡأَشۡرَارِ

Ndipo iwo adzati, “Kodi zachitika bwanji kuti ife sitili kuona anthu amene tinkawawerenga pakati pa anthu ochita choipa?”

38:63

أَتَّخَذۡنَٰهُمۡ سِخۡرِيًّا أَمۡ زَاغَتۡ عَنۡهُمُ ٱلۡأَبۡصَٰرُ

Kodi ife timangowanyoza kapena maso athu alephera kuwaona bwinobwino

38:64

إِنَّ ذَٰلِكَ لَحَقٌّ تَخَاصُمُ أَهۡلِ ٱلنَّارِ

Ndithudi zimenezi ndi zoona. Zokangana za anthu a ku moto

38:65

قُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ مُنذِرٌۖ وَمَا مِنۡ إِلَٰهٍ إِلَّا ٱللَّهُ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّارُ

Nena, “Ndithudi ine ndine mchenjezi basi ndipo kulibe mulungu wina koma Mulungu mmodzi yekha, wopambama ndi wofunika.”

38:66

رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفَّٰرُ

“Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo. Iye ndi wamphamvu zambiri ndi wokhululukira nthawi zonse.”

38:67

قُلۡ هُوَ نَبَؤٌاْ عَظِيمٌ

Nena, “Uwu ndi uthenga wofunika kwambiri.”

38:68

أَنتُمۡ عَنۡهُ مُعۡرِضُونَ

“Umeneinumulikuukana.”

38:69

مَا كَانَ لِيَ مِنۡ عِلۡمِۭ بِٱلۡمَلَإِ ٱلۡأَعۡلَىٰٓ إِذۡ يَخۡتَصِمُونَ

“Inesindidziwazamafumu olemekezeka pamene amatsutsana ndi kukambirana.”

38:70

إِن يُوحَىٰٓ إِلَيَّ إِلَّآ أَنَّمَآ أَنَا۠ نَذِيرٌ مُّبِينٌ

“Koma akuti ichi chavumbulutsidwa kwa ine kuti ndine opereka chenjezo lomveka ndiponso poyera.”

38:71

إِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنِّي خَٰلِقُۢ بَشَرًا مِّن طِينٍ

Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa Angelo, “Ndithudi Ine ndidzalenga munthu kuchokera ku dothi.”

38:72

فَإِذَا سَوَّيۡتُهُۥ وَنَفَخۡتُ فِيهِ مِن رُّوحِي فَقَعُواْ لَهُۥ سَٰجِدِينَ

Ndipo ndikatha kumulenga iye ndi kumupumira mzimu wanga kotero igwani nonse ndi kumulambira iye

38:73

فَسَجَدَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ كُلُّهُمۡ أَجۡمَعُونَ

Kotero Angelo onse pamodzi adamulambira

38:74

إِلَّآ إِبۡلِيسَ ٱسۡتَكۡبَرَ وَكَانَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Kupatula Satana, iye anali ndi mwano ndipo iye anali mmodzi wa osakhulupirira

38:75

قَالَ يَٰٓإِبۡلِيسُ مَا مَنَعَكَ أَن تَسۡجُدَ لِمَا خَلَقۡتُ بِيَدَيَّۖ أَسۡتَكۡبَرۡتَ أَمۡ كُنتَ مِنَ ٱلۡعَالِينَ

Mulungu adati, “Iwe Satana! Chakuletsa ndi chiyani kulambira munthu amene ndalenga ndi manja anga? Kodi ndiwe wamwano? Kodi kapena iwe ndiwe mmodzi wa apamwamba?”

38:76

قَالَ أَنَا۠ خَيۡرٌ مِّنۡهُ خَلَقۡتَنِي مِن نَّارٍ وَخَلَقۡتَهُۥ مِن طِينٍ

Iye adati, “Ine ndine wopambana kuposa iye. Inu mudandilenga ine kuchokera kumoto pamene iye mudamulenga kuchokera ku dothi.”

38:77

قَالَ فَٱخۡرُجۡ مِنۡهَا فَإِنَّكَ رَجِيمٌ

Mulungu adati, “Kotero choka pamaso panga chifukwa iwe ndiwe okanidwa ndi otembereredwa.”

38:78

وَإِنَّ عَلَيۡكَ لَعۡنَتِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلدِّينِ

“Ndipo ndithudi matemberero anga adzakhala pa iwe mpaka pa tsiku lachiweruzo.”

38:79

قَالَ رَبِّ فَأَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ

Satana adati, “Ambuye wanga! Ndipatseni mpata mpaka patsiku louka kwa akufa.”

38:80

قَالَ فَإِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ

Mulungu adati, “Mpata waperekedwa kwa iwe.”

38:81

إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡوَقۡتِ ٱلۡمَعۡلُومِ

“Mpaka pa nthawi yomwe idakhazikitsidwa.”

38:82

قَالَ فَبِعِزَّتِكَ لَأُغۡوِيَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ

Satana adati, “Kotero kudzera ku mphamvu zanu, ine ndidzawasocheretsa.”

38:83

إِلَّا عِبَادَكَ مِنۡهُمُ ٱلۡمُخۡلَصِينَ

“Kupatula akapolo anu osankhidwa amene ali pakati pawo.”

38:84

قَالَ فَٱلۡحَقُّ وَٱلۡحَقَّ أَقُولُ

Mulungu adati, “Ichi ndi choonadi ndipo choonadi ndicho chimene ndimanena.”

38:85

لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنكَ وَمِمَّن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ أَجۡمَعِينَ

“Kuti ndidzadzadza Gahena ndi iwe ndiponso onse amene amakutsatira iwe.”

38:86

قُلۡ مَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍ وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُتَكَلِّفِينَ

Nena “Ine sindili kukufunsani malipiro chifukwa cha ichi ndiponso ine sindine wodziyenereza.”

38:87

إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٌ لِّلۡعَٰلَمِينَ

“Ichi si china koma chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse.”

38:88

وَلَتَعۡلَمُنَّ نَبَأَهُۥ بَعۡدَ حِينِۭ

“Ndithudi nonse mudzadziwa choonadi chake nthawi ina.”

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.