Surah 82 · 19 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Infitar in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

82:1

إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنفَطَرَتۡ

Pamene thambo lidzang’ambika

82:2

وَإِذَا ٱلۡكَوَاكِبُ ٱنتَثَرَتۡ

Pamene nyenyezi zidzagwa ndi kubalalitsidwa

82:3

وَإِذَا ٱلۡبِحَارُ فُجِّرَتۡ

Ndi pamene nyanja zikuluzikulu zidzaphulika

82:4

وَإِذَا ٱلۡقُبُورُ بُعۡثِرَتۡ

Pamene manda adzatseguka

82:5

عَلِمَتۡ نَفۡسٌ مَّا قَدَّمَتۡ وَأَخَّرَتۡ

Pamenepo Mzimu uliwonse udzadziwa chimene udatumiza ndi chimene udasiya m’mbuyo

82:6

يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ مَا غَرَّكَ بِرَبِّكَ ٱلۡكَرِيمِ

oh Iwe munthu! Kodi ndi chiyani chikukunamiza kuti usiye kutsatira malamulo a Ambuye wako Wolemekezeka

82:7

ٱلَّذِي خَلَقَكَ فَسَوَّىٰكَ فَعَدَلَكَ

Amene adakulenga iwe ndi kukukonza kuti uzioneka bwino monga mmene uonekeramu

82:8

فِيٓ أَيِّ صُورَةٍ مَّا شَآءَ رَكَّبَكَ

Ndi nkhope ina iliyonse imene idamukondweretsa anakulenga iwe

82:9

كـَلَّا بَلۡ تُكَذِّبُونَ بِٱلدِّينِ

Iyayi! Koma inu mukukana kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo

82:10

وَإِنَّ عَلَيۡكُمۡ لَحَٰفِظِينَ

Koma pakati panu pali ena amene ali kukuyang’anirani

82:11

كِرَامًا كَٰتِبِينَ

Olemekezeka ndi odziwa kulemba

82:12

يَعۡلَمُونَ مَا تَفۡعَلُونَ

Iwo amadziwa chilichonse chimene mumachita

82:13

إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٍ

Ndithudi anthu onse angwiro adzakhala mu mtendere

82:14

وَإِنَّ ٱلۡفُجَّارَ لَفِي جَحِيمٍ

Ndipo, ndithudi, anthu onse oipa adzakhala ku Gahena

82:15

يَصۡلَوۡنَهَا يَوۡمَ ٱلدِّينِ

Imene iwo adzalowako ndi kulawa malawi ake patsiku lachiweruzo

82:16

وَمَا هُمۡ عَنۡهَا بِغَآئِبِينَ

Iwo sadzatha kuthawa ayi

82:17

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ

Kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo

82:18

ثُمَّ مَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ

Tinenanso kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo

82:19

يَوۡمَ لَا تَمۡلِكُ نَفۡسٌ لِّنَفۡسٍ شَيۡـًٔاۖ وَٱلۡأَمۡرُ يَوۡمَئِذٍ لِّلَّهِ

Ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzatha kuthandiza wina aliyense ndipo Mulungu yekha ndiye amene adzaweruza

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.