Surah 83 · 36 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Surah Al-Mutaffifin in Chichewa
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
ٱلَّذِينَ إِذَا ٱكۡتَالُواْ عَلَى ٱلنَّاسِ يَسۡتَوۡفُونَ
Iwo amene amati ena akamawayesera zinthu amafuna kuti zikwanire muyeso wake
وَإِذَا كَالُوهُمۡ أَو وَّزَنُوهُمۡ يُخۡسِرُونَ
Koma pamene iwo ayesa kapena awayesera anthu ena amawanyenga
يَوۡمَ يَقُومُ ٱلنَّاسُ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Tsiku limene anthu a mitundu yonse adzaima pamaso pa Ambuye wa zolengedwa zonse
كـَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡفُجَّارِ لَفِي سِجِّينٍ
Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu onse oipa chili mu Sijjin
وَمَا يُكَذِّبُ بِهِۦٓ إِلَّا كُلُّ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ
Palibe wina amene amalikana tsikuli kupatula munthu wogona m’machimo
إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Pamene chivumbulutso chathu chinenedwa kwa iye, iye amati: “Izi ndizo nthano za anthu akale.”
كـَلَّاۖ بَلۡۜ رَانَ عَلَىٰ قُلُوبِهِم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Iyayi! Koma m’mitima mwawo ndi mokutidwa ndi zintchito zimene amachita
كـَلَّآ إِنَّهُمۡ عَن رَّبِّهِمۡ يَوۡمَئِذٍ لَّمَحۡجُوبُونَ
Iyayi! Ndithudi iwo sadzaloledwa kuona Ambuye wawo pa tsikuli
ثُمَّ يُقَالُ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ
Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti: “Chimenechi ndicho chilango chija munkachinena kuti sichidzakhalako.”
كـَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡأَبۡرَارِ لَفِي عِلِّيِّينَ
Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu olungama chimasungidwa mu Illiyyun
يَشۡهَدُهُ ٱلۡمُقَرَّبُونَ
Limene limaonedwa ndi iwo okhawo amene ali kufupi ndi zofuna za Mulungu
يُسۡقَوۡنَ مِن رَّحِيقٍ مَّخۡتُومٍ
Iwo adzapatsidwa kuti amwe vinyo weniweni amene sanatsegulidwepo
خِتَٰمُهُۥ مِسۡكٌۚ وَفِي ذَٰلِكَ فَلۡيَتَنَافَسِ ٱلۡمُتَنَٰفِسُونَ
Womaliza wake adzakhala ndi fungo labwino ndipo pachifukwa cha ichi, aleke onse amene afuna kulimbikira kuti alimbike
إِنَّ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْ كَانُواْ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ يَضۡحَكُونَ
Ndithudi! Anthu amene amachita zoipa, anali kuwaseka anthu amene anakhulupirira
وَإِذَا ٱنقَلَبُوٓاْ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمُ ٱنقَلَبُواْ فَكِهِينَ
Ndipo iwo amati akabwerera kwa anthu awo amabwera ali kunyoza
وَإِذَا رَأَوۡهُمۡ قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَضَآلُّونَ
Ndipo amati akawaona iwo amati: “Ndithudi awa ndiwo anthu osochera.”
فَٱلۡيَوۡمَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنَ ٱلۡكُفَّارِ يَضۡحَكُونَ
Koma pa tsikuli anthu okhulupirira adzaseka anthu osakhulupirira
هَلۡ ثُوِّبَ ٱلۡكُفَّارُ مَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ
Kodi anthu osakhulupirira, sanalipidwe mphotho yawo molingana ndi ntchito zawo
Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.