بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
84:1إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنشَقَّتۡ
Pamene thambo lidzang’ambika
84:2وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ
Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi
84:3وَإِذَا ٱلۡأَرۡضُ مُدَّتۡ
Pamene nthaka idzatambasulidwa
84:4وَأَلۡقَتۡ مَا فِيهَا وَتَخَلَّتۡ
Ndi kutulutsa zonse zimene zinakwiriridwa m’kati mwake ndi kukhala yopanda kanthu
84:5وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ
Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi
84:6يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ إِنَّكَ كَادِحٌ إِلَىٰ رَبِّكَ كَدۡحًا فَمُلَٰقِيهِ
oh iwe munthu! Ndithudi iwe uli kubwerera kupita kwa Ambuye wako ndi ntchito zako. Kubwerera kotsimikizidwa. Motero udzakumana nazo
84:7فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ
Koma Iye amene adzapatsidwa Buku lake m’dzanja lamanja
84:8فَسَوۡفَ يُحَاسَبُ حِسَابًا يَسِيرًا
Adzawerengedwa mosavuta
84:9وَيَنقَلِبُ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورًا
Ndipo adzabwerera kwa anthu ake ndi chisangalalo
84:10وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ وَرَآءَ ظَهۡرِهِۦ
Koma iye amene adzapatsidwa buku lake kumbuyo kwake
84:11فَسَوۡفَ يَدۡعُواْ ثُبُورًا
Iye adzalira
84:12وَيَصۡلَىٰ سَعِيرًا
Ndipo akalowa ku moto walawi – lawi ku Gahena
84:13إِنَّهُۥ كَانَ فِيٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورًا
Ndithudi iye adali wansangala pakati pa anthu ake
84:14إِنَّهُۥ ظَنَّ أَن لَّن يَحُورَ
Ndithudi iye anali kuganiza kuti sadzabwerera kwa Mulungu
84:15بَلَىٰٓۚ إِنَّ رَبَّهُۥ كَانَ بِهِۦ بَصِيرًا
Inde! Ndithudi Ambuye wake anali kuona zonse zimene iye ankachita
84:16فَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلشَّفَقِ
Ine ndilumbira pali kufiira kwa kulowa kwa dzuwa
84:17وَٱلَّيۡلِ وَمَا وَسَقَ
Ndi pali usiku ndi zonse zimene umabweretsa mu mdima
84:18وَٱلۡقَمَرِ إِذَا ٱتَّسَقَ
Ndi pali mwezi pamene ufika pa chimake penipeni
84:19لَتَرۡكَبُنَّ طَبَقًا عَن طَبَقٍ
Ndipo inu, ndithudi, mudzayenda kupita kutsogolo, kuchoka apa ndi kufika apo
84:20فَمَا لَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Kodi ndi chifukwa chiyani choti iwo alibe chikhulupiriro
84:21وَإِذَا قُرِئَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقُرۡءَانُ لَا يَسۡجُدُونَۤ
Ndipo pamene Korani ili kuwerengedwa kwa iwo sagwa pansi. Al-Buruj
84:22بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُكَذِّبُونَ
Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amalikana
84:23وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يُوعُونَ
Ndipo Mulungu amadziwa zinthu zonse zimene amasonkhanitsa
84:24فَبَشِّرۡهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ
Choncho auze iwo za chilango chowawa
84:25إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونِۭ
Kupatula okhawo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, chifukwa iwo ali ndi malipiro opanda malire
Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.