Surah 75 · 40 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Surah Al-Qiyamah in Chichewa
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلنَّفۡسِ ٱللَّوَّامَةِ
Ndipo ndilumbira pali munthu amene amadzidzudzula yekha
أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَلَّن نَّجۡمَعَ عِظَامَهُۥ
Kodi munthu amaganiza kuti Ife sitidzalumikiza mafupa ake
بَلَىٰ قَٰدِرِينَ عَلَىٰٓ أَن نُّسَوِّيَ بَنَانَهُۥ
Inde Ife tikhoza kulumikiza mwaubwino nsonga za zala zake
بَلۡ يُرِيدُ ٱلۡإِنسَٰنُ لِيَفۡجُرَ أَمَامَهُۥ
Ngakhale tero, munthu amafuna kupitiliza kuchita zoipa
يَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذٍ أَيۡنَ ٱلۡمَفَرُّ
Patsikuli munthu adzafunsa kuti: “Kodi ndithawira kuti tsopano?”
يُنَبَّؤُاْ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذِۭ بِمَا قَدَّمَ وَأَخَّرَ
Patsiku limeneli, munthu adzauzidwa zonse zimene adachita kuyambira poyamba mpaka pomaliza
لَا تُحَرِّكۡ بِهِۦ لِسَانَكَ لِتَعۡجَلَ بِهِۦٓ
Usagwedeze lilime lako zokhudza Korani ponena mofulumira
إِنَّ عَلَيۡنَا جَمۡعَهُۥ وَقُرۡءَانَهُۥ
Ndi udindo wathu kuisonkhanitsa ndi kukupatsa nzeru kuilakatula iyo
فَإِذَا قَرَأۡنَٰهُ فَٱتَّبِعۡ قُرۡءَانَهُۥ
Ndipo pamene talakatula, tsatira mwandondomeko kalakatulidwe kake
وُجُوهٌ يَوۡمَئِذٍ نَّاضِرَةٌ
Nkhope zina, pa tsiku limeneli, zidzakhala zowala ndi chisangalalo
وَقِيلَ مَنۡۜ رَاقٍ
Ndipo kudzanenedwa kuti: “Kodi palibe woti angamuchize ndi kumupulumutsa ku imfa?”
ثُمَّ ذَهَبَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ يَتَمَطَّىٰٓ
Ndipo iye anapita kubanja lake monyada ali kudziyamikila yekha
أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَن يُتۡرَكَ سُدًى
Kodi munthu amaganiza kuti tidzangomulekerera kuti azichita chilichonse chimene afuna
ثُمَّ كَانَ عَلَقَةً فَخَلَقَ فَسَوَّىٰ
Ndipo iye adakhala kam’bulu ka magazi. Ndipo Mulungu adamuumba ndipo adamukonza m’maonekedwe okongola
فَجَعَلَ مِنۡهُ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰٓ
Ndipo adamulenga m’mitundu iwiri, mwamuna ndi mkazi
أَلَيۡسَ ذَٰلِكَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يُحۡـِۧيَ ٱلۡمَوۡتَىٰ
Kodi Iye alibe mphamvu yopereka moyo kwa anthu akufa
Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.