Surah 19 · 98 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Maryam in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

19:1

كٓهيعٓصٓ

Kaf ha ya ain suad

19:2

ذِكۡرُ رَحۡمَتِ رَبِّكَ عَبۡدَهُۥ زَكَرِيَّآ

Ichi ndi chikumbutso cha chifuniro cha Ambuye wako kwa kapolo wake Zakariya

19:3

إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥ نِدَآءً خَفِيًّا

Pamene Iye adamupempha Ambuye wake motsitsa mawu

19:4

قَالَ رَبِّ إِنِّي وَهَنَ ٱلۡعَظۡمُ مِنِّي وَٱشۡتَعَلَ ٱلرَّأۡسُ شَيۡبًا وَلَمۡ أَكُنۢ بِدُعَآئِكَ رَبِّ شَقِيًّا

Iye adati, “oh Ambuye wanga! Mafupa anga ndi ofoka ndipo mutu wanga uli ndi imvi chifukwa cha ukalamba. Komabe, Ambuye, ine sindidapemphe kwa Inu mopanda phindu.”

19:5

وَإِنِّي خِفۡتُ ٱلۡمَوَٰلِيَ مِن وَرَآءِي وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرًا فَهَبۡ لِي مِن لَّدُنكَ وَلِيًّا

“Ndithudi ine ndili ndi mantha ndi abale anga za amene adzalowe m’malo mwanga ndiponso mkazi wanga ndi chumba. Ndipatseni mwana wamwamuna.”

19:6

يَرِثُنِي وَيَرِثُ مِنۡ ءَالِ يَعۡقُوبَۖ وَٱجۡعَلۡهُ رَبِّ رَضِيًّا

“Amene adzalowe m’malo mwanga ndi m’malo mwa ana a Yakobo, ndipo mpangeni, Ambuye wanga, kukhala mmodzi wa wokondedwa wanu.”

19:7

يَٰزَكَرِيَّآ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ ٱسۡمُهُۥ يَحۡيَىٰ لَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ مِن قَبۡلُ سَمِيًّا

“Ee iwe Zakariya! Ife tili kukuuza nkhani yabwino yakuti iwe udzapatsidwa mwana wamwamuna ndipo adzatchedwa Yohane, dzina limene silidapatsidwe kwa aliyense kumbuyoku.”

19:8

قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٌ وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرًا وَقَدۡ بَلَغۡتُ مِنَ ٱلۡكِبَرِ عِتِيًّا

Zakariya adati, “Ambuye! Kodi ine ndingakhale ndi mwana wamwamuna bwanji, pamene mkazi wanga ndi chumba ndipo ine ndine wokalamba?”

19:9

قَالَ كَذَٰلِكَ قَالَ رَبُّكَ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٌ وَقَدۡ خَلَقۡتُكَ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ تَكُ شَيۡـًٔا

Iye adati, “Chimenechi, wanena Ambuye wako! Idzakhala ntchito yopepuka kwa Ine chifukwa Ine ndidakupanga kukhala munthu pamene iwe siunali chinthu china chilichonse chodziwika.”

19:10

قَالَ رَبِّ ٱجۡعَل لِّيٓ ءَايَةًۖ قَالَ ءَايَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ ٱلنَّاسَ ثَلَٰثَ لَيَالٍ سَوِيًّا

Zakariya adati, “Ambuye, ndipatseni chizindikiro chokhudza zimene zidzachitike.” Iye adati, “Chizindikiro chako ndi chakuti siudzalankhula ndi anthu usiku utatu ngakhale ulibe chilema.”

19:11

فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنَ ٱلۡمِحۡرَابِ فَأَوۡحَىٰٓ إِلَيۡهِمۡ أَن سَبِّحُواْ بُكۡرَةً وَعَشِيًّا

Pamene Zakariya adadza kwa anthu ake kuchokera m’kachisi, adawauza anthuwo kuti, “Lemekezani Ambuye wanu m’mawa ndi madzulo.”

19:12

يَٰيَحۡيَىٰ خُذِ ٱلۡكِتَٰبَ بِقُوَّةٍۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحُكۡمَ صَبِيًّا

“Oh Yohane! Samala mawu a Mulungu kwambiri.” Ife tidamupatsa luntha pamene adali mwana

19:13

وَحَنَانًا مِّن لَّدُنَّا وَزَكَوٰةًۖ وَكَانَ تَقِيًّا

Ndiponso tidamupatsa mtima wachifundo ndi woyeretsedwa ndipo adali munthu opewa zoipa

19:14

وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَيۡهِ وَلَمۡ يَكُن جَبَّارًا عَصِيًّا

Ndipo adali kulemekeza abambo ndi amayi ake. Iye sadali wodzikweza kapena wonyoza malamulo a Mulungu

19:15

وَسَلَٰمٌ عَلَيۡهِ يَوۡمَ وُلِدَ وَيَوۡمَ يَمُوتُ وَيَوۡمَ يُبۡعَثُ حَيًّا

Mtendere udali pa iye pa tsiku limene adabadwa ndi pa tsiku limene adafa ndipo mtendere ukhale pa iye pamene aukitsidwa kwa akufa

19:16

وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَرۡيَمَ إِذِ ٱنتَبَذَتۡ مِنۡ أَهۡلِهَا مَكَانًا شَرۡقِيًّا

Ndipo kukumbukira nkhani ya Maria m’Buku! Pamene iye adasiya anthu ake ndi kupita kumalo a payekha kumbali ya ku m’mawa

19:17

فَٱتَّخَذَتۡ مِن دُونِهِمۡ حِجَابًا فَأَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهَا رُوحَنَا فَتَمَثَّلَ لَهَا بَشَرًا سَوِيًّا

Ndipo iye adafunda nsalu kuti anthu asaone nkhope yake. Ife tidamutumizira iye Mzimu wathu umene udaoneka ngati munthu

19:18

قَالَتۡ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ مِنكَ إِن كُنتَ تَقِيًّا

Maria adati, “Mwini chisoni anditeteze ine kwa iwe! Ngati iwe umaopa Ambuye, ndisiye ndekha, usandiyandikire ayi.”

19:19

قَالَ إِنَّمَآ أَنَا۠ رَسُولُ رَبِّكِ لِأَهَبَ لَكِ غُلَٰمًا زَكِيًّا

Mngelo adati, “Ine ndine Mthenga wa Ambuye wako ndipo ndadza kudzakupatsa mwana wamwamuna woyera.”

19:20

قَالَتۡ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٌ وَلَمۡ يَمۡسَسۡنِي بَشَرٌ وَلَمۡ أَكُ بَغِيًّا

Maria adati, “Kodi ine ndidzabereka mwana bwanji pamene ine ndine wosakhudzidwa ndi mwamuna ndiponso si ndine wachiwerewere ayi?”

19:21

قَالَ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٌۖ وَلِنَجۡعَلَهُۥٓ ءَايَةً لِّلنَّاسِ وَرَحۡمَةً مِّنَّاۚ وَكَانَ أَمۡرًا مَّقۡضِيًّا

Mngelo adati, “Ndi momwemo” Ambuye wako wanena kuti, “Zimenezo, kwa Ine, ndi zopepuka. Tidzamupanga iye kukhala chizindikiro kwa anthu ndi madalitso ochoka kwa Ife. Limeneli ndilo lamulo limene lalamulidwa.”

19:22

فَحَمَلَتۡهُ فَٱنتَبَذَتۡ بِهِۦ مَكَانًا قَصِيًّا

Ndipo iye adakhala ndi pakati ndipo adapita kumalo akutali

19:23

فَأَجَآءَهَا ٱلۡمَخَاضُ إِلَىٰ جِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ قَالَتۡ يَٰلَيۡتَنِي مِتُّ قَبۡلَ هَٰذَا وَكُنتُ نَسۡيًا مَّنسِيًّا

Ndipo ululu wa kubereka udamubwerera pamene adali patsinde pa mtengo wa tende ndipo adalira nati, “Kalanga ine, bola ndikadangofa zisanachitike izi chifukwa ndikadakhala woiwalidwa.”

19:24

فَنَادَىٰهَا مِن تَحۡتِهَآ أَلَّا تَحۡزَنِي قَدۡ جَعَلَ رَبُّكِ تَحۡتَكِ سَرِيًّا

Kudabwera mawu kuchokera pansi oti: “Usadandaule ayi. Ambuye wako wakukonzera ka mtsinje kamene kalikuyenda ku mapazi ako.”

19:25

وَهُزِّيٓ إِلَيۡكِ بِجِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ تُسَٰقِطۡ عَلَيۡكِ رُطَبًا جَنِيًّا

“Ndipo gwedeza mtengo watendewu, iwo udzagwetsa zipatso za tende zaziwisi ndi zakupsa.”

19:26

فَكُلِي وَٱشۡرَبِي وَقَرِّي عَيۡنًاۖ فَإِمَّا تَرَيِنَّ مِنَ ٱلۡبَشَرِ أَحَدًا فَقُولِيٓ إِنِّي نَذَرۡتُ لِلرَّحۡمَٰنِ صَوۡمًا فَلَنۡ أُكَلِّمَ ٱلۡيَوۡمَ إِنسِيًّا

“Idya ndi umwe, kotero sangalala.” Ndipo ukakumana ndi munthu wina aliyense muuze kuti, “Ine ndalumbira kwa Mwini chisoni kusala chakudya ndipo sindidzayankhula ndi munthu wina aliyense lero.”

19:27

فَأَتَتۡ بِهِۦ قَوۡمَهَا تَحۡمِلُهُۥۖ قَالُواْ يَٰمَرۡيَمُ لَقَدۡ جِئۡتِ شَيۡـًٔا فَرِيًّا

Ndipo iye adatenga mwana wake nanka naye kwa anthu ake amene adati kwa iye’ “Iwe Maria! Ndithudi iwe wabweretsa chinthu cha chilendo.”

19:28

يَٰٓأُخۡتَ هَٰرُونَ مَا كَانَ أَبُوكِ ٱمۡرَأَ سَوۡءٍ وَمَا كَانَتۡ أُمُّكِ بَغِيًّا

“Iwe mlongo wake wa Aroni! Atate wako sanali munthu wochita zoipa ndiponso Amayi ako sadali a chiwerewere.”

19:29

فَأَشَارَتۡ إِلَيۡهِۖ قَالُواْ كَيۡفَ نُكَلِّمُ مَن كَانَ فِي ٱلۡمَهۡدِ صَبِيًّا

Maria adamuloza iye. Koma iwo adati, “Kodi ife tingayankhule ndi mwana wam’chikuta bwanji?”

19:30

قَالَ إِنِّي عَبۡدُ ٱللَّهِ ءَاتَىٰنِيَ ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلَنِي نَبِيًّا

Mwanayo adati, “Ine ndine kapolo wa Mulungu. Iye wandipatsa ine Buku labwino ndipo wandisankha kukhala Mtumwi.”

19:31

وَجَعَلَنِي مُبَارَكًا أَيۡنَ مَا كُنتُ وَأَوۡصَٰنِي بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ مَا دُمۡتُ حَيًّا

“Madalitso ake ali pa ine kulikonse kumene ndingapite ndipo wandilamulira kuti ndikhale wopemphera ndi kupereka chaulere kwa anthu osauka nthawi yonse ya moyo wanga.”

19:32

وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَتِي وَلَمۡ يَجۡعَلۡنِي جَبَّارًا شَقِيًّا

“Iye wandilamula kuti ndizilemekeza amayi anga ndipo sadandipange kukhala wamwano ndi woipa.”

19:33

وَٱلسَّلَٰمُ عَلَيَّ يَوۡمَ وُلِدتُّ وَيَوۡمَ أَمُوتُ وَيَوۡمَ أُبۡعَثُ حَيًّا

Ndipo mtendere ukhale kwa ine patsiku limene ndidabadwa, ndi patsiku limene ndidzafa ndiponso pa tsiku limene ndidzaukitsidwa kwa akufa

19:34

ذَٰلِكَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَۖ قَوۡلَ ٱلۡحَقِّ ٱلَّذِي فِيهِ يَمۡتَرُونَ

Ameneyo ndiye Yesu, mwana wa Maria. Liwu loonadi limene iwo ali kukayika

19:35

مَا كَانَ لِلَّهِ أَن يَتَّخِذَ مِن وَلَدٍۖ سُبۡحَٰنَهُۥٓۚ إِذَا قَضَىٰٓ أَمۡرًا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ

Sizili zoyenera kuti Mulungu akhale ndi mwana wamwamuna! Iye ayeretsedwe ku zimenezo. Ngati Iye afuna chinthu, Iye amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi

19:36

وَإِنَّ ٱللَّهَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٌ مُّسۡتَقِيمٌ

Ndithudi Mulungu ndi Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Kotero mpembedzeni Iye yekha. Imeneyo ndiyo njira

19:37

فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن مَّشۡهَدِ يَوۡمٍ عَظِيمٍ

Koma magulu a Akhirisitu adasemphana maganizo pakati pawo. Koma pamene tsiku loopsa lidza, tsoka kwa anthu osakhulupirira

19:38

أَسۡمِعۡ بِهِمۡ وَأَبۡصِرۡ يَوۡمَ يَأۡتُونَنَا لَٰكِنِ ٱلظَّٰلِمُونَ ٱلۡيَوۡمَ فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ

Kodi iwo adzaona ndi kumva momveka bwanji pa tsiku limene adzaonekera pa maso pathu! Koma anthu ochita zoipa lero ali mu chisokonezo choonekeratu

19:39

وَأَنذِرۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡحَسۡرَةِ إِذۡ قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٍ وَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Achenjeze za tsiku limene adzanong’oneza bombono, pamene malamulo athu adzakwaniritsidwa ndipo pamene iwo ali nkuiwala ndi kusakhulupirira

19:40

إِنَّا نَحۡنُ نَرِثُ ٱلۡأَرۡضَ وَمَنۡ عَلَيۡهَا وَإِلَيۡنَا يُرۡجَعُونَ

Ndithudi Ife tidzatenga dziko lapansi ndi onse amene amakhala m’menemo. Ndi kwa Ife kumene onse adzabwezedwa

19:41

وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِبۡرَٰهِيمَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقًا نَّبِيًّا

Ndipo kumbukira nkhani ya Abrahamu imene ili m’Buku. Iye adali Mtumwi ndi munthu wangwiro

19:42

إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ يَٰٓأَبَتِ لِمَ تَعۡبُدُ مَا لَا يَسۡمَعُ وَلَا يُبۡصِرُ وَلَا يُغۡنِي عَنكَ شَيۡـًٔا

Pamene iye adawauza bambo wake kuti, “Oh Abambo! Kodi inu mungalambire bwanji chinthu chimene sichingathe kumva, kuona kapena kukuthandizani pa chilichonse?”

19:43

يَٰٓأَبَتِ إِنِّي قَدۡ جَآءَنِي مِنَ ٱلۡعِلۡمِ مَا لَمۡ يَأۡتِكَ فَٱتَّبِعۡنِيٓ أَهۡدِكَ صِرَٰطًا سَوِيًّا

“Ohabambo! Choonadichavumbulutsidwa kwa ine chimene sichinakufikireni inu. Kotero nditsatireni ine kuti ndikutsogolereni ku njira yoyenera.”

19:44

يَٰٓأَبَتِ لَا تَعۡبُدِ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلرَّحۡمَٰنِ عَصِيًّا

“oh abambo! Musamapembedze Satana. Ndithudi Satana adanyoza Ambuye wachisoni chosatha.”

19:45

يَٰٓأَبَتِ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يَمَسَّكَ عَذَابٌ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ فَتَكُونَ لِلشَّيۡطَٰنِ وَلِيًّا

“oh abambo! Ine ndili kuopa kuti chilango cha Mulungu chidzadza pa inu ndipo mudzakhala bwenzi la Satana.”

19:46

قَالَ أَرَاغِبٌ أَنتَ عَنۡ ءَالِهَتِي يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ لَأَرۡجُمَنَّكَۖ وَٱهۡجُرۡنِي مَلِيًّا

Abambo ake adati, “Kodi ukudana ndi milungu yanga iwe Abrahamu? Ukapanda kusiya ndidzakuponya miyala ndipo unditalikire pa kanthawi kochepa.”

19:47

قَالَ سَلَٰمٌ عَلَيۡكَۖ سَأَسۡتَغۡفِرُ لَكَ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ بِي حَفِيًّا

Abrahamu adati, “Mtendere ukhale kwa inu. Ine ndidzapempha Ambuye wanga kuti akukhululukireni popeza, Mulungu, kwa ine, ndi wokoma mtima.”

19:48

وَأَعۡتَزِلُكُمۡ وَمَا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَأَدۡعُواْ رَبِّي عَسَىٰٓ أَلَّآ أَكُونَ بِدُعَآءِ رَبِّي شَقِيًّا

“Ine ndikuchokerani ndi zimene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu. Ine ndidzapempha kwa Ambuye wanga ndipo ndikhulupirira kuti popembedza Ambuye wanga ndisadzakhale watsoka

19:49

فَلَمَّا ٱعۡتَزَلَهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۖ وَكُلًّا جَعَلۡنَا نَبِيًّا

Ndipo pamene Abrahamu adasiya anthu ake ndi mafano amene iwo anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu, tidamupatsa Isake ndi Yakobo. Aliyense wa iwo tidamupanga kukhala Mtumwi

19:50

وَوَهَبۡنَا لَهُم مِّن رَّحۡمَتِنَا وَجَعَلۡنَا لَهُمۡ لِسَانَ صِدۡقٍ عَلِيًّا

Ndipo tidawapatsa onse mituka kuchokera m’chifundo chathu ndipo tidawapanga iwo kukhala otchulidwa mwaulemu

19:51

وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مُوسَىٰٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ مُخۡلَصًا وَكَانَ رَسُولًا نَّبِيًّا

Ndipo kumbukira nkhani ya Mose imene ili m’Buku, amene adali wosankhidwa ndiponso Mtumwi ndi Mneneri

19:52

وَنَٰدَيۡنَٰهُ مِن جَانِبِ ٱلطُّورِ ٱلۡأَيۡمَنِ وَقَرَّبۡنَٰهُ نَجِيًّا

Ife tidamuitana kuchokera kumbali ya dzanja la manja la phiri la Sinai ndipo tinamuyandikitsa kukhala pafupi ndi Ife kuti tiyankhule naye mwamseri

19:53

وَوَهَبۡنَا لَهُۥ مِن رَّحۡمَتِنَآ أَخَاهُ هَٰرُونَ نَبِيًّا

Tidamupatsa, mwachisoni chathu, m’bale wake Aroni kuti akhale Mtumwi

19:54

وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِسۡمَٰعِيلَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صَادِقَ ٱلۡوَعۡدِ وَكَانَ رَسُولًا نَّبِيًّا

Ndipo kumbukira nkhani ya Ishimayeli imene ili m’Buku. Iye adali wosunga pangano ndipo adali Mtumwi ndi Mneneri

19:55

وَكَانَ يَأۡمُرُ أَهۡلَهُۥ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ وَكَانَ عِندَ رَبِّهِۦ مَرۡضِيًّا

Iye anali kulamula anthu ake kuchita mapemphero ndi kupereka chothandiza nacho anthu osauka ndipo adali, kwa Ambuye wake, wokondedwa

19:56

وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِدۡرِيسَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقًا نَّبِيًّا

Ndipo kumbukira za Idrissa. Iye adali munthu wonena zoona ndi Mtumwi

19:57

وَرَفَعۡنَٰهُ مَكَانًا عَلِيًّا

Ife tidamukweza kukhala malo a pamwamba

19:58

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ مِن ذُرِّيَّةِ ءَادَمَ وَمِمَّنۡ حَمَلۡنَا مَعَ نُوحٍ وَمِن ذُرِّيَّةِ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡرَٰٓءِيلَ وَمِمَّنۡ هَدَيۡنَا وَٱجۡتَبَيۡنَآۚ إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُ ٱلرَّحۡمَٰنِ خَرُّواْۤ سُجَّدًاۤ وَبُكِيًّا

Awa ndi anthu amene Mulungu adawaonetsera chisomo chake. Atumwi ochokera ku m’badwo wa Adamu ndi iwo amene tidawatenga pamodzi m’chombo ndi Nowa. Ana a Abrahamu, a Israyeli ndi iwo amene Ife tawatsogolera ndi kuwasankha. Pamene zivumbulutso za Mwini chisoni chosatha zinali kulakatulidwa kwa iwo, iwo adali kugwa nkhope zawo pansi ndi kumalira

19:59

فَخَلَفَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ خَلۡفٌ أَضَاعُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَٱتَّبَعُواْ ٱلشَّهَوَٰتِۖ فَسَوۡفَ يَلۡقَوۡنَ غَيًّا

Koma mibadwo ya anthu imene inadza iwo atachoka idanyoza mapemphero ndi kutsatira zilakolako zawo. Ndithudi awa adzakumana ndi mavuto

19:60

إِلَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحًا فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ وَلَا يُظۡلَمُونَ شَيۡـًٔا

Kupatula amene alapa machimo ndi kukhulupirira choonadi ndi kumachita ntchito zabwino. Iwo adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa m’chilichonse

19:61

جَنَّٰتِ عَدۡنٍ ٱلَّتِي وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ عِبَادَهُۥ بِٱلۡغَيۡبِۚ إِنَّهُۥ كَانَ وَعۡدُهُۥ مَأۡتِيًّا

Iwo adzakhala m’minda ya Edeni mpaka muyaya, imene Mwini chisoni chosatha adalonjeza akapolo ake ngakhale kuti iwo sadaione. Ndithudi lonjezo lake lidzakwaniritsidwa

19:62

لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا إِلَّا سَلَٰمًاۖ وَلَهُمۡ رِزۡقُهُمۡ فِيهَا بُكۡرَةً وَعَشِيًّا

Kumeneko iwo sadzamva zinthu zopanda pake koma mawu a mtendere okha, ndipo chakudya chidzapatsidwa kwa iwo m’mawa ndi madzulo

19:63

تِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِي نُورِثُ مِنۡ عِبَادِنَا مَن كَانَ تَقِيًّا

Imeneyo ndiyo Paradiso imene tidzawapatsa akapolo athu omwe anali kuopa Mulungu

19:64

وَمَا نَتَنَزَّلُ إِلَّا بِأَمۡرِ رَبِّكَۖ لَهُۥ مَا بَيۡنَ أَيۡدِينَا وَمَا خَلۡفَنَا وَمَا بَيۡنَ ذَٰلِكَۚ وَمَا كَانَ رَبُّكَ نَسِيًّا

Ife sititsika kuchoka kumwamba pokhapokha ngati taloledwa ndi Ambuye wako. Iye ndiye mwini wa zinthu zonse zimene zili pamaso pathu, kumbuyo kwathu ndi zonse zimene zili pakati pa zimenezi. Ndipo Ambuye wako saiwala

19:65

رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا فَٱعۡبُدۡهُ وَٱصۡطَبِرۡ لِعِبَٰدَتِهِۦۚ هَلۡ تَعۡلَمُ لَهُۥ سَمِيًّا

Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo. Kotero m’pembedze Iye yekha ndipo khala wopirira pamapemphero ake. Kodi ukudziwa wina amene ali ndi dzina ngati la Iye

19:66

وَيَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَءِذَا مَا مِتُّ لَسَوۡفَ أُخۡرَجُ حَيًّا

Munthu amati, “Pamene ine nditafa kodi ndidzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo?”

19:67

أَوَلَا يَذۡكُرُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ يَكُ شَيۡـًٔا

Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga iye pamene poyamba sadali chinthu china chilichonse

19:68

فَوَرَبِّكَ لَنَحۡشُرَنَّهُمۡ وَٱلشَّيَٰطِينَ ثُمَّ لَنُحۡضِرَنَّهُمۡ حَوۡلَ جَهَنَّمَ جِثِيًّا

Motero pali Ambuye wako; ndithudi Tidzawasonkhanitsa pamodzi ndi a Satana ndipo onse tidzawabweretsa m’mphepete mwa Gahena atagwada

19:69

ثُمَّ لَنَنزِعَنَّ مِن كُلِّ شِيعَةٍ أَيُّهُمۡ أَشَدُّ عَلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ عِتِيًّا

Ndipo mwachoonadi tidzachotsa mugulu lililonse onse amene adanyoza Mulungu kwambiri

19:70

ثُمَّ لَنَحۡنُ أَعۡلَمُ بِٱلَّذِينَ هُمۡ أَوۡلَىٰ بِهَا صِلِيًّا

Ndithudi Ife tilikuwadziwa kwambiri amene ali oyenera kuotchedwa

19:71

وَإِن مِّنكُمۡ إِلَّا وَارِدُهَاۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ حَتۡمًا مَّقۡضِيًّا

Palibe wina wa inu amene sadzapita kumbali ya Moto. Limeneli ndilo lamulo la mphamvu la Ambuye wanu

19:72

ثُمَّ نُنَجِّي ٱلَّذِينَ ٱتَّقَواْ وَّنَذَرُ ٱلظَّٰلِمِينَ فِيهَا جِثِيًّا

Ndipo Ife tidzapulumutsa onse amene amaopa ndi kuwasiya ochita zoipa, atagwada, kuti amve ululu wake

19:73

وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٍ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَيُّ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ خَيۡرٌ مَّقَامًا وَأَحۡسَنُ نَدِيًّا

Pamene zivumbulutso zathu zilakatulidwa momveka kwa iwo, anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ndi gulu liti pa magulu awiriwa limene lili ndi malo abwino okhala ndi anthu apamwamba?”

19:74

وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هُمۡ أَحۡسَنُ أَثَٰثًا وَرِءۡيًا

Kodi ndi mibadwo ingati yakale imene tidaononga iwo asanadze, mibadwo imene idali ndi zinthu zabwino ndiponso zokongola

19:75

قُلۡ مَن كَانَ فِي ٱلضَّلَٰلَةِ فَلۡيَمۡدُدۡ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَدًّاۚ حَتَّىٰٓ إِذَا رَأَوۡاْ مَا يُوعَدُونَ إِمَّا ٱلۡعَذَابَ وَإِمَّا ٱلسَّاعَةَ فَسَيَعۡلَمُونَ مَنۡ هُوَ شَرٌّ مَّكَانًا وَأَضۡعَفُ جُندًا

Nena, “Aliyense amene alakwa, Mwini chisoni chosatha adzawaonjezera nthawi, mpaka pamene adzaone zomwe adalonjezedwa. Kaya ndi chilango kapena ola lomaliza, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndani amene ali mwini wa malo oipa ndi gulu lankhondo lofoka.”

19:76

وَيَزِيدُ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ٱهۡتَدَوۡاْ هُدًىۗ وَٱلۡبَٰقِيَٰتُ ٱلصَّٰلِحَٰتُ خَيۡرٌ عِندَ رَبِّكَ ثَوَابًا وَخَيۡرٌ مَّرَدًّا

Mulungu amapitiriza kutsogolera iwo amene atsatira njira yoyenera. Ntchito zabwino zimene zili ndi malipiro osatha zili ndi mphotho yabwino pamaso pa Ambuye wako ndiponso zotsatira zake ndi zabwino

19:77

أَفَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي كَفَرَ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالَ لَأُوتَيَنَّ مَالًا وَوَلَدًا

Kodi mwamuona munthu amene akana zivumbulutso zathu ndipo amanena kuti, “Ine, ndithudi, ndidzapatsidwa chuma ndi ana?”

19:78

أَطَّلَعَ ٱلۡغَيۡبَ أَمِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدًا

Kodi iye waziona zinthu zosaoneka kapena Mwini chisoni chosatha wamupatsa lonjezo lotere

19:79

كـَلَّاۚ سَنَكۡتُبُ مَا يَقُولُ وَنَمُدُّ لَهُۥ مِنَ ٱلۡعَذَابِ مَدًّا

Osatheka! Ife tidzalemba zimene akunena ndi kuchipanga chilango chake kukhala chachitali

19:80

وَنَرِثُهُۥ مَا يَقُولُ وَيَأۡتِينَا فَرۡدًا

Zonse zimene azilankhula iye zidzabwerera kwa Ife ndipo adzadza pamaso pathu yekha

19:81

وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةً لِّيَكُونُواْ لَهُمۡ عِزًّا

Anthu osakhulupirira adadzisankhira milungu ina kuti iwapatse mphamvu ndi ulemerero

19:82

كـَلَّاۚ سَيَكۡفُرُونَ بِعِبَادَتِهِمۡ وَيَكُونُونَ عَلَيۡهِمۡ ضِدًّا

Ayi. Koma milunguyo idzakana kupembedza kwawo ndipo idzakhala adani awo

19:83

أَلَمۡ تَرَ أَنَّآ أَرۡسَلۡنَا ٱلشَّيَٰطِينَ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ تَؤُزُّهُمۡ أَزًّا

Kodi siudaone kuti timatumiza kwa anthu osakhulupirira a Satana amene amawaonetsa zinthu zoti achimwe nazo

19:84

فَلَا تَعۡجَلۡ عَلَيۡهِمۡۖ إِنَّمَا نَعُدُّ لَهُمۡ عَدًّا

Kotero musafulumize kuwapemphera chionongeko, ndithudi, tikuwawerengera masiku awo

19:85

يَوۡمَ نَحۡشُرُ ٱلۡمُتَّقِينَ إِلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ وَفۡدًا

Tsiku limenetidzasonkhanitsaanthuolungamam’magulu kufika pamaso pa Ambuye wachisoni kudzalandira ulemu

19:86

وَنَسُوقُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ إِلَىٰ جَهَنَّمَ وِرۡدًا

Ndipo tidzawakusa anthu oipa kupita ku moto wa ku Gahena ali ndi ludzu lodetsa nkhawa

19:87

لَّا يَمۡلِكُونَ ٱلشَّفَٰعَةَ إِلَّا مَنِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدًا

Palibe amene adzakhala ndi mphamvu zodandaula kupatula yekhayo amene walandira chilolezo cha Mwini chisoni chosatha

19:88

وَقَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَلَدًا

Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabala mwana wamwamuna.”

19:89

لَّقَدۡ جِئۡتُمۡ شَيۡـًٔا إِدًّا

Ndithudi mwanena chinthu choipitsitsa

19:90

تَكَادُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ يَتَفَطَّرۡنَ مِنۡهُ وَتَنشَقُّ ٱلۡأَرۡضُ وَتَخِرُّ ٱلۡجِبَالُ هَدًّا

Pafupifupi kumwamba kumafuna kung’ambika chifukwa cha mawu amenewa ndipo nthaka imafuna kugawikana ndi mapiri kugudubuzika ndi kuonongeka

19:91

أَن دَعَوۡاْ لِلرَّحۡمَٰنِ وَلَدًا

Chifukwa chonena Mwini Chisoni Chosatha ali ndi mwana wamwamuna

19:92

وَمَا يَنۢبَغِي لِلرَّحۡمَٰنِ أَن يَتَّخِذَ وَلَدًا

Si zoyenera kwa Mwini chisoni chosatha kuti akhale ndi mwana

19:93

إِن كُلُّ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ إِلَّآ ءَاتِي ٱلرَّحۡمَٰنِ عَبۡدًا

Palibe china chilichonse chimene chili kumwamba kapena pa dziko lapansi chimene chimabwera kwa Mwini chisoni chosatha kupatula ngati kapolo

19:94

لَّقَدۡ أَحۡصَىٰهُمۡ وَعَدَّهُمۡ عَدًّا

Iye wasunga chiwerengero cha zolengedwa zake zonse

19:95

وَكُلُّهُمۡ ءَاتِيهِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَرۡدًا

Ndipo onse, mmodzimmodzi, adzabwerera kwa Iye pa tsiku la kuuka kwa akufa

19:96

إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَيَجۡعَلُ لَهُمُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وُدًّا

Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, Mwini chisoni chosatha adzawakonda

19:97

فَإِنَّمَا يَسَّرۡنَٰهُ بِلِسَانِكَ لِتُبَشِّرَ بِهِ ٱلۡمُتَّقِينَ وَتُنذِرَ بِهِۦ قَوۡمًا لُّدًّا

Motero Ife tapanga iyo kukhala yosavuta ya m’chiyankhulo chako kuti upeleke nkhani yabwino kwa anthu oopa ndi kuchenjeza ndi ilo anthu otsutsa

19:98

وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هَلۡ تُحِسُّ مِنۡهُم مِّنۡ أَحَدٍ أَوۡ تَسۡمَعُ لَهُمۡ رِكۡزَۢا

Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga kale iwo asanadze? Kodi uli kumuona mmodzi aliyense wa iwo kapena kumva manong’onong’o ochokera kwa iwo

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.