Surah 68 · 52 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Qalam in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

68:1

نٓۚ وَٱلۡقَلَمِ وَمَا يَسۡطُرُونَ

Nun. Pali cholembera ndi zimene amalemba

68:2

مَآ أَنتَ بِنِعۡمَةِ رَبِّكَ بِمَجۡنُونٍ

Mwachisomo cha Ambuye wako, sindiwe wamisala ayi

68:3

وَإِنَّ لَكَ لَأَجۡرًا غَيۡرَ مَمۡنُونٍ

Ndithudi iwe udzalandira mphotho yosatha

68:4

وَإِنَّكَ لَعَلَىٰ خُلُقٍ عَظِيمٍ

Ndithudi iwe uli ndi makhalidwe abwino

68:5

فَسَتُبۡصِرُ وَيُبۡصِرُونَ

Iwe udzaona ndipo nawo adzaona

68:6

بِأَييِّكُمُ ٱلۡمَفۡتُونُ

Kuti ndani wa inu amene ndi wamisala

68:7

إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِۦ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ

Ndithudi Ambuye wako amadziwa bwino amene wasochera ku njira yake ndipo amadziwa bwino amene amayenda m’njira yoyenera

68:8

فَلَا تُطِعِ ٱلۡمُكَذِّبِينَ

Motero usatsatire zochita za anthu osakhulupirira

68:9

وَدُّواْ لَوۡ تُدۡهِنُ فَيُدۡهِنُونَ

Iwo afuna utagwirizana nawo kuti nawonso agwirizane nawe

68:10

وَلَا تُطِعۡ كُلَّ حَلَّافٍ مَّهِينٍ

Ndipo usamvere zonena za munthu wotukwana amene alibe phindu

68:11

هَمَّازٍ مَّشَّآءِۭ بِنَمِيمٍ

Woononga mbiri ya anzake ponena Al Qalam 613 za bodza

68:12

مَّنَّاعٍ لِّلۡخَيۡرِ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ

Woletsa ntchito zachilungamo, wophwanya malamulo ndi wochita zoipa

68:13

عُتُلِّۭ بَعۡدَ ذَٰلِكَ زَنِيمٍ

woipa mtima ndipo wobadwa mosalongosoka

68:14

أَن كَانَ ذَا مَالٍ وَبَنِينَ

Chifukwa iye ali ndi chuma ndi ana

68:15

إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Pamene chivumbulutso chathu chilakatulidwa kwa iye, amati: “Ndi nkhani za anthu a makedzana.”

68:16

سَنَسِمُهُۥ عَلَى ٱلۡخُرۡطُومِ

Ife tidzaika chizindikiro pa mphuno pake

68:17

إِنَّا بَلَوۡنَٰهُمۡ كَمَا بَلَوۡنَآ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ إِذۡ أَقۡسَمُواْ لَيَصۡرِمُنَّهَا مُصۡبِحِينَ

Ndithudi Ife tidawayesa iwo monga momwe tidawayesera eni ake a munda, amene adalumbira kuti adzakolola mbewu zawo m’mawa mwake

68:18

وَلَا يَسۡتَثۡنُونَ

Osaonjezera mawu oti: “Ngati Mulungu alola.”

68:19

فَطَافَ عَلَيۡهَا طَآئِفٌ مِّن رَّبِّكَ وَهُمۡ نَآئِمُونَ

Kotero kudadutsa china chake chochokera kwa Ambuye wako nthawi ya usiku ndi kuwotcha pamene iwo anali kugona

68:20

فَأَصۡبَحَتۡ كَٱلصَّرِيمِ

Ndipo m’mawa, munda udasanduka wakuda monga mdima wa usiku

68:21

فَتَنَادَوۡاْ مُصۡبِحِينَ

Ndipo mmawa iwo adaitanizana wina ndi mnzake

68:22

أَنِ ٱغۡدُواْ عَلَىٰ حَرۡثِكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰرِمِينَ

Nati: “Mulawirire ku munda ngati mufuna kukakolola.”

68:23

فَٱنطَلَقُواْ وَهُمۡ يَتَخَٰفَتُونَ

Ndipo iwo adapita, namanong’onezana wina ndi mnzake

68:24

أَن لَّا يَدۡخُلَنَّهَا ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكُم مِّسۡكِينٌ

“Palibe munthu wosauka amene adzaloledwa kulowa m’mundamo kudzapempha”

68:25

وَغَدَوۡاْ عَلَىٰ حَرۡدٍ قَٰدِرِينَ

Ndipo m’mawa, onse adapita ndi mphamvu zotchinjirizira anthu osauka

68:26

فَلَمَّا رَأَوۡهَا قَالُوٓاْ إِنَّا لَضَآلُّونَ

Koma pamene iwo adaona zimene zidachitika, onse adati: “Ndithudi ife talakwa.”

68:27

بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ

“Iai! Ndithudi ife tapwetekeka.”

68:28

قَالَ أَوۡسَطُهُمۡ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ لَوۡلَا تُسَبِّحُونَ

wangwiro amene anali pakati pawo adati: “Kodi ine sindidakuuzeni kuti bwanji inu simunena kuti: Ngati Mulungu alola?”

68:29

قَالُواْ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ

“Iwo adati ulemerero ukhale kwa Ambuye wathu! Ndithudi ife ndife olakwa.”

68:30

فَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍ يَتَلَٰوَمُونَ

Ndipo iwo adayamba kudzudzulana kuti wina adali wolakwa

68:31

قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا طَٰغِينَ

Iwo adati: “Tsoka kwa ife! Ndithudi Ife tidali ophwanya malamulo.”

68:32

عَسَىٰ رَبُّنَآ أَن يُبۡدِلَنَا خَيۡرًا مِّنۡهَآ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا رَٰغِبُونَ

“Mwina kuti Ambuye wathu adzatipatsa munda wina wabwino m’malo mwa uwu. Ndithudi ndi kwa Iye kumene timapempha modzichepetsa.”

68:33

كَذَٰلِكَ ٱلۡعَذَابُۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَكۡبَرُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ

Chimenechi ndicho chilango koma ndithudi chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chowawa kwambiri, iwo akadadziwa

68:34

إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ عِندَ رَبِّهِمۡ جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ

Ndithudi anthu onse angwiro adzalandira minda ya madalitso imene ili ndi Ambuye wawo

68:35

أَفَنَجۡعَلُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ كَٱلۡمُجۡرِمِينَ

Kodi Ife tidzasamala anthu angwiro chimodzimodzi ndi anthu ochimwa

68:36

مَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ

Kodi mwatani? Kodi inu mumaweruza bwanji

68:37

أَمۡ لَكُمۡ كِتَٰبٌ فِيهِ تَدۡرُسُونَ

Kapena kodi muli ndi Buku limene mumawerengamo

68:38

إِنَّ لَكُمۡ فِيهِ لَمَا تَخَيَّرُونَ

Kuti inu mudzapeza m’menemo chilichonse chimene mukufuna

68:39

أَمۡ لَكُمۡ أَيۡمَٰنٌ عَلَيۡنَا بَٰلِغَةٌ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ إِنَّ لَكُمۡ لَمَا تَحۡكُمُونَ

Kapena inu mwalandira kuchokera kwa Ife, lonjezo lotsimikizika mpaka pa tsiku louka kwa akufa kuti, ndithudi, inu mudzapeza zimene mukufuna

68:40

سَلۡهُمۡ أَيُّهُم بِذَٰلِكَ زَعِيمٌ

Tawafunsa ngati wina wa iwo angachitire umboni za lonjezolo

68:41

أَمۡ لَهُمۡ شُرَكَآءُ فَلۡيَأۡتُواْ بِشُرَكَآئِهِمۡ إِن كَانُواْ صَٰدِقِينَ

Kapena, kodi iwo ali ndi milungu ina? Aleke abweretse milungu yawo ngati iwo anena zoona

68:42

يَوۡمَ يُكۡشَفُ عَن سَاقٍ وَيُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ

Ndipatsikulimenechinthuchoopsachidzachitika, iwo adzaitanidwa kuti apembedze, koma adzalephera kutero

68:43

خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٌۖ وَقَدۡ كَانُواْ يُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ وَهُمۡ سَٰلِمُونَ

Maso awo adzayang’ana pansi ndipo adzanyozedwa kwambiri chifukwa iwo adauzidwa kupembedza pamene adali pa mtendere

68:44

فَذَرۡنِي وَمَن يُكَذِّبُ بِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِۖ سَنَسۡتَدۡرِجُهُم مِّنۡ حَيۡثُ لَا يَعۡلَمُونَ

Kotero ndisiyire aliyense amene akutsutsana ndi chenjezo ili. Ife tidzawalanga pang’onopang’ono m’njira imene iwo saizindikira

68:45

وَأُمۡلِي لَهُمۡۚ إِنَّ كَيۡدِي مَتِينٌ

Ndipo Ine ndidzalekerera pa kanthawi! Ndithudi chikonzero changa ndi champhamvu

68:46

أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ أَجۡرًا فَهُم مِّن مَّغۡرَمٍ مُّثۡقَلُونَ

Kapena kodi iwe uli kuwafunsa malipiro moti iwo ali ndi ngongole yambiri

68:47

أَمۡ عِندَهُمُ ٱلۡغَيۡبُ فَهُمۡ يَكۡتُبُونَ

Kapena kodi iwo amadziwa za Buku lobisika kuti iwo akhoza kulemba

68:48

فَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ وَلَا تَكُن كَصَاحِبِ ٱلۡحُوتِ إِذۡ نَادَىٰ وَهُوَ مَكۡظُومٌ

Motero pirira podikilira chiweruzo cha Ambuye wako ndipo usakhale ngati amene adamezedwa ndi nsomba pamene adalira kupempha chithandizo iye ali m’mavuto

68:49

لَّوۡلَآ أَن تَدَٰرَكَهُۥ نِعۡمَةٌ مِّن رَّبِّهِۦ لَنُبِذَ بِٱلۡعَرَآءِ وَهُوَ مَذۡمُومٌ

Ngati Ambuye wake akadapanda kumuonetsa chisomo chake, ndithudi iye akadakhalabe koma iye adaponyedwa pa mtunda pamene anali wolakwa

68:50

فَٱجۡتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَجَعَلَهُۥ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Koma Ambuye wake adamusankha ndipo adamuchititsa kukhala wabwino

68:51

وَإِن يَكَادُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَيُزۡلِقُونَكَ بِأَبۡصَٰرِهِمۡ لَمَّا سَمِعُواْ ٱلذِّكۡرَ وَيَقُولُونَ إِنَّهُۥ لَمَجۡنُونٌ

Ndipo, ndithudi, iwo onse osakhulupirira akadakusokeretsa ndi maso awo pamene amakumbutsidwa ndipo amati: “Ndithudi uyu ndi Wamisala.”

68:52

وَمَا هُوَ إِلَّا ذِكۡرٌ لِّلۡعَٰلَمِينَ

Koma ichi si china koma chikumbutso kwa zolengedwa zonse

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.