Surah 43 · 89 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Az-Zukhruf in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

43:1

حمٓ

Ha mim

43:2

وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ

Ndilumbira pali Buku limene limafotokoza zinthu mosabisa

43:3

إِنَّا جَعَلۡنَٰهُ قُرۡءَٰنًا عَرَبِيًّا لَّعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ

Ndithudi talipanga ilo kukhala Korani yam’chinenero cha Chiarabu kuti iwe ukhoza kulizindikira

43:4

وَإِنَّهُۥ فِيٓ أُمِّ ٱلۡكِتَٰبِ لَدَيۡنَا لَعَلِيٌّ حَكِيمٌ

Ndithudi ilo lili mu Make Buku limene lili pamaso pathu, lolemekezeka ndi lodzala ndi nzeru

43:5

أَفَنَضۡرِبُ عَنكُمُ ٱلذِّكۡرَ صَفۡحًا أَن كُنتُمۡ قَوۡمًا مُّسۡرِفِينَ

Kodi Ife tisiye kukukumbutsani inu nonse chifukwa chakuti ndinu anthu osasamala ndi oswa malamulo

43:6

وَكَمۡ أَرۡسَلۡنَا مِن نَّبِيٍّ فِي ٱلۡأَوَّلِينَ

Kodi ndi Atumwi angati amene Ife tidatumiza ku mitundu ya anthu akale

43:7

وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن نَّبِيٍّ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ

Ndipo kwa iwo sikunadze Mtumwi amene iwo sadamunyoze

43:8

فَأَهۡلَكۡنَآ أَشَدَّ مِنۡهُم بَطۡشًا وَمَضَىٰ مَثَلُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Kotero Ife tidawaononga, anthu amphamvu kuposa awa, ndipo chitsanzo cha anthu onse akale chadutsa

43:9

وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ خَلَقَهُنَّ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡعَلِيمُ

Ndithudi ngati iwe ukawafunsa kuti, “Kodi ndani adalenga kumwamba ndi dziko lapansi?” Iwo, ndithudi, adzakuyankha kuti, “Mwini mphamvu ndi Mwini wodziwa ndiye amene adazilenga.”

43:10

ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مَهۡدًا وَجَعَلَ لَكُمۡ فِيهَا سُبُلًا لَّعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ

Iye ndi amene adalenga dziko kukhala malo anu a mpumulo ndipo adaika mu ilo njira kuti inu mukhoza kutsogozedwa bwino

43:11

وَٱلَّذِي نَزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٍ فَأَنشَرۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةً مَّيۡتًاۚ كَذَٰلِكَ تُخۡرَجُونَ

Ndipo ndiye amene amatumiza mvula kuchokera kumitambo molingana ndi muyeso. Ndipo Ife timadzutsa nthaka imene idali yakufa ndi iyo, kotero nanunso mudzadzutsidwa chimodzimodzi

43:12

وَٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا وَجَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡفُلۡكِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ مَا تَرۡكَبُونَ

Ndipo ndiye amene adalenga zinthu ziwiriziwiri ndipo adapanga zombo ndi nyama kuti muzikwera

43:13

لِتَسۡتَوُۥاْ عَلَىٰ ظُهُورِهِۦ ثُمَّ تَذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ رَبِّكُمۡ إِذَا ٱسۡتَوَيۡتُمۡ عَلَيۡهِ وَتَقُولُواْ سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَنَا هَٰذَا وَمَا كُنَّا لَهُۥ مُقۡرِنِينَ

Kuti inu mukhoza kukhala okhazikika pa misana pawo ndi kukumbukira ubwino wa Ambuye wanu pamene mumakhazikikapo ndi kunena kuti, “Ulemerero ukhale kwa Iye amene adazipanga izo kukhala zopanda mphamvu kwa ife ndipo ife sitikadatha kutero.”

43:14

وَإِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا لَمُنقَلِبُونَ

“Ndithudi kwa Ambuye wathu ife tidzabwerera.”

43:15

وَجَعَلُواْ لَهُۥ مِنۡ عِبَادِهِۦ جُزۡءًاۚ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَكَفُورٌ مُّبِينٌ

Komabe iwo amawapatsa ena mwa akapolo ake gawo lake. Ndithudi munthu ndi wosayamika

43:16

أَمِ ٱتَّخَذَ مِمَّا يَخۡلُقُ بَنَاتٍ وَأَصۡفَىٰكُم بِٱلۡبَنِينَ

Kodi Iye wadzisankhira ana aakazi kuchokera ku zimene walenga ndipo adakusankhani inu kukhala ndi ana aamuna

43:17

وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِمَا ضَرَبَ لِلرَّحۡمَٰنِ مَثَلًا ظَلَّ وَجۡهُهُۥ مُسۡوَدًّا وَهُوَ كَظِيمٌ

Ndipo ngati wina wa iwo auzidwa nkhani za chimene Iye amati ndi chofanana ndi Mulungu, nkhope yake imada ndipo amakhala wokwiya

43:18

أَوَمَن يُنَشَّؤُاْ فِي ٱلۡحِلۡيَةِ وَهُوَ فِي ٱلۡخِصَامِ غَيۡرُ مُبِينٍ

Icho ndi chimene chidapangidwa ngati chosangalatsa ndipo pa mtsutso, icho sichingathe kuyankhula bwinobwino

43:19

وَجَعَلُواْ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ ٱلَّذِينَ هُمۡ عِبَٰدُ ٱلرَّحۡمَٰنِ إِنَٰثًاۚ أَشَهِدُواْ خَلۡقَهُمۡۚ سَتُكۡتَبُ شَهَٰدَتُهُمۡ وَيُسۡـَٔلُونَ

Ndipo iwo amasandutsa angelo amene ali akapolo a Mulungu, kukhala akazi. Kodi iwo adaonerera chilengedwe chawo? Umboni wawo udzalembedwa ndipo iwo adzafunsidwa

43:20

وَقَالُواْ لَوۡ شَآءَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَا عَبَدۡنَٰهُمۗ مَّا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ

Ndipo iwo adati, “Chikadakhala chifuniro cha Mwini Chisoni Chosatha, ife sitikadapembedza milungu ina.” Iwo sadziwa china chilichonse chokhudza chimenechi. Ndipo iwo amangonama chabe

43:21

أَمۡ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ كِتَٰبًا مِّن قَبۡلِهِۦ فَهُم بِهِۦ مُسۡتَمۡسِكُونَ

Kodi kapena Ife tidawapatsa Buku lina ili lisanadze limene iwo ali kukhulupilira

43:22

بَلۡ قَالُوٓاْ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٍ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّهۡتَدُونَ

Iyayi! Iwo amati, “Ife tidapeza makolo athu ali kutsatira njira ina ndi chipembedzo china chake ndipo ife timatsogozedwa potsatira zimene iwo amachita.”

43:23

وَكَذَٰلِكَ مَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي قَرۡيَةٍ مِّن نَّذِيرٍ إِلَّا قَالَ مُتۡرَفُوهَآ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٍ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّقۡتَدُونَ

Ndipo Ife sitidatumize Mchenjezi iwe usanadze kwa anthu ena, koma achuma amene anali kukhala pakati pawo ankati; “Ife tidapeza makolo athu ali kutsatira njira yina ndi chipembedzo china chake ndipo ndithudi ife tidzatsatira zimene iwo anali kuchita.”

43:24

قَٰلَ أَوَلَوۡ جِئۡتُكُم بِأَهۡدَىٰ مِمَّا وَجَدتُّمۡ عَلَيۡهِ ءَابَآءَكُمۡۖ قَالُوٓاْ إِنَّا بِمَآ أُرۡسِلۡتُم بِهِۦ كَٰفِرُونَ

Iye adati; “Ngakhale kuti ine nditakubweretserani langizo labwino loposa limene mukuti mudapeza makolo anu ali kutsatira?” Iwo adati, “Ndithudi ife sitikhulupirira zimene iwe ukuti watumizidwa.”

43:25

فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُكَذِّبِينَ

Kotero Ife tidagwetsa chilango pa iwo ndipo taona mmene chinalili chimaliziro cha iwo amene adakana choonadi

43:26

وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِيمُ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦٓ إِنَّنِي بَرَآءٌ مِّمَّا تَعۡبُدُونَ

Ndipo Abrahamu adawauza abambo ake pamodzi ndi anthu ake kuti, “Ndithudi ine ndili kudzipatula ku zimene inu mupembedza.”

43:27

إِلَّا ٱلَّذِي فَطَرَنِي فَإِنَّهُۥ سَيَهۡدِينِ

“Kupatula yekhayo amene adandilenga ine ndipo, ndithudi, Iye adzanditsogolera.”

43:28

وَجَعَلَهَا كَلِمَةَۢ بَاقِيَةً فِي عَقِبِهِۦ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Ndipo adawapanga mawu kuti akhazikike mwa iwo amene adadza iye atachoka kuti akhoza kubwerera

43:29

بَلۡ مَتَّعۡتُ هَٰٓؤُلَآءِ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ وَرَسُولٌ مُّبِينٌ

Iyayi! Koma Ine ndidawapatsa ,iwo ndiponso makolo awo, chisangalalo mpaka pamene choonadi chidadza kwa iwo ndi Mtumwi amene anali kuwafotokozera zonse momveka

43:30

وَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٌ وَإِنَّا بِهِۦ كَٰفِرُونَ

Koma pamene choonadi chidadza pa iwo, iwo adati, “Awa ndi matsenga ndipo ife sitikhulupirira mwa iwo.”

43:31

وَقَالُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانُ عَلَىٰ رَجُلٍ مِّنَ ٱلۡقَرۡيَتَيۡنِ عَظِيمٍ

Ndipo iwo amati: “Bwanji Korani iyi siidatumizidwe kwa munthu wina wotchuka wochokera ku Mzinda wina pakati pa Mizinda iwiri?”

43:32

أَهُمۡ يَقۡسِمُونَ رَحۡمَتَ رَبِّكَۚ نَحۡنُ قَسَمۡنَا بَيۡنَهُم مَّعِيشَتَهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَرَفَعۡنَا بَعۡضَهُمۡ فَوۡقَ بَعۡضٍ دَرَجَٰتٍ لِّيَتَّخِذَ بَعۡضُهُم بَعۡضًا سُخۡرِيًّاۗ وَرَحۡمَتُ رَبِّكَ خَيۡرٌ مِّمَّا يَجۡمَعُونَ

Kodi ndiwo amene akhoza kugawa gawo lina la chisomo cha Ambuye wako? Ndife amene timagawa pakati pawo chakudya chawo cha moyo uno ndipo tawakweza ena kukhala apamwamba kuposa anzawo kotero kuti akhoza kulemba ntchito anzawo. Koma chisoni cha Ambuye wako ndi chabwino kwambiri kuposa chuma chimene amasonkhanitsa

43:33

وَلَوۡلَآ أَن يَكُونَ ٱلنَّاسُ أُمَّةً وَٰحِدَةً لَّجَعَلۡنَا لِمَن يَكۡفُرُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ لِبُيُوتِهِمۡ سُقُفًا مِّن فِضَّةٍ وَمَعَارِجَ عَلَيۡهَا يَظۡهَرُونَ

Ndipo zikadakhala kuti anthu onse anali a chipembedzo chimodzi, ndithudi, Ife tikadawapatsa onse amene sakhulupirira mwa Mulungu madenga a siliva kuti aike pa nyumba zawo ndi pa makwerero oti azikwererapo

43:34

وَلِبُيُوتِهِمۡ أَبۡوَٰبًا وَسُرُرًا عَلَيۡهَا يَتَّكِـُٔونَ

Ndipo nyumba, zitseko ndi mipando, zonse zikadakhala za siliva kuti azikhalapo

43:35

وَزُخۡرُفًاۚ وَإِن كُلُّ ذَٰلِكَ لَمَّا مَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَٱلۡأٓخِرَةُ عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُتَّقِينَ

Ndipo zipangizo zina zikadakhala za golide. Komabe zonsezi sizikadakhala chinthu china koma chisangalalo cha m’moyo uno. Ndipo moyo umene uli nkudza, umene uli ndi Ambuye wako, ndi wa anthu ochita ntchito zabwino

43:36

وَمَن يَعۡشُ عَن ذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ نُقَيِّضۡ لَهُۥ شَيۡطَٰنًا فَهُوَ لَهُۥ قَرِينٌ

Aliyense amene asiya kukumbukira Mwini chisoni chosatha, Ife timamusankhira iye Satana kuti akhale bwenzi lake la pamtima

43:37

وَإِنَّهُمۡ لَيَصُدُّونَهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُم مُّهۡتَدُونَ

Ndipo, ndithudi, iwo amangowasokoneza ku njira yoyenera koma iwo amaganiza kuti ali kutsogozedwa bwino

43:38

حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَنَا قَالَ يَٰلَيۡتَ بَيۡنِي وَبَيۡنَكَ بُعۡدَ ٱلۡمَشۡرِقَيۡنِ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرِينُ

Mpaka pamene wotereyu abwerera kwa Ife, iye amati, pomuuza bwenzi lake la pamtima, “Kukadakhala kuti pakati pa ine ndi iwe panali mtunda wotalika monga kutalikirana kwa kum’mawa kuwiri!” Bwenzi loipa lenileni

43:39

وَلَن يَنفَعَكُمُ ٱلۡيَوۡمَ إِذ ظَّلَمۡتُمۡ أَنَّكُمۡ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ

Ndipo popeza inu munali kuchita zoipa, lero sizidzakuthandizani popeza nonse ndinu olandira chilango

43:40

أَفَأَنتَ تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ أَوۡ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَمَن كَانَ فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ

Kodi iwe ungawapange agonthi kumva kapena kutsogolera anthu akhungu kapena kutsogolera iye amene ndi ochimwa

43:41

فَإِمَّا نَذۡهَبَنَّ بِكَ فَإِنَّا مِنۡهُم مُّنتَقِمُونَ

Ndipo Ife tikakutenga, Ife, ndithudi, tidzagwetsa chilango chathu pa iwo

43:42

أَوۡ نُرِيَنَّكَ ٱلَّذِي وَعَدۡنَٰهُمۡ فَإِنَّا عَلَيۡهِم مُّقۡتَدِرُونَ

Kapena ngati Ife titakuonetsa zina zimene tawalonjeza iwo, ndipo ndithudi, Ife tili ndi mphamvu pa zinthu zonse

43:43

فَٱسۡتَمۡسِكۡ بِٱلَّذِيٓ أُوحِيَ إِلَيۡكَۖ إِنَّكَ عَلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ

Kotero gwiritsa chimene chavumbulutsidwa kwa iwe. Ndithudi iwe uli pa njira yoyenera

43:44

وَإِنَّهُۥ لَذِكۡرٌ لَّكَ وَلِقَوۡمِكَۖ وَسَوۡفَ تُسۡـَٔلُونَ

Ndipo ndithudi Ichi ndi chikumbutso kwa iwe ndi kwa anthu ako ndipo posachedwapa mudzafunsidwa

43:45

وَسۡـَٔلۡ مَنۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رُّسُلِنَآ أَجَعَلۡنَا مِن دُونِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ءَالِهَةً يُعۡبَدُونَ

Ndipo afunse iwo za Atumwi athu amene Ife tidawatuma iwe usanabadwe. Kodi Ife tidasankha milungu ina yoti izipembedzedwa yoonjezera pa Mwini Chisoni Chosatha

43:46

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَقَالَ إِنِّي رَسُولُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo, ndithudi, Ife tidamutumiza Mose ndi uthenga wathu kwa Farawo ndi mafumu ake ndipo iye adati, “Ndithudi ine ndine Mtumwi wa Ambuye wa zolengedwa zonse.”

43:47

فَلَمَّا جَآءَهُم بِـَٔايَٰتِنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَضۡحَكُونَ

Koma pamene iye adadza kwa iwo ndi zizindikiro zathu zooneka, iwo adaziseka zizindikirozo

43:48

وَمَا نُرِيهِم مِّنۡ ءَايَةٍ إِلَّا هِيَ أَكۡبَرُ مِنۡ أُخۡتِهَاۖ وَأَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡعَذَابِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Tidawaonetsa zizindikiro zosiyanasiyana, chilichonse chopambana chinzake, ndipo Ife tidawapatsa chilango kuti akhoza kutembenuka

43:49

وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَ ٱلسَّاحِرُ ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ بِمَا عَهِدَ عِندَكَ إِنَّنَا لَمُهۡتَدُونَ

Ndipo iwo adati, “oh iwe munthu wamatsenga! Mupemphe Ambuye wako m’malo mwathu, molingana ndi lonjezo limene Iye adapanga ndi iwe. Ndithudi ife tidzatsatira njira yoyenera.”

43:50

فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابَ إِذَا هُمۡ يَنكُثُونَ

Koma pamene tidawachotsera chilango, iwo adaphwanya lonjezo lawo

43:51

وَنَادَىٰ فِرۡعَوۡنُ فِي قَوۡمِهِۦ قَالَ يَٰقَوۡمِ أَلَيۡسَ لِي مُلۡكُ مِصۡرَ وَهَٰذِهِ ٱلۡأَنۡهَٰرُ تَجۡرِي مِن تَحۡتِيٓۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ

Ndipo Farawo adalengeza pamaso pa anthu ake kuti, “Oh inu anthu anga! Kodi Ufumu wa dziko la Aiguputo si wanga? Nanga mitsinje imene ilikuyenda pansi pa mapazi anga, kodi simuli kuiona?”

43:52

أَمۡ أَنَا۠ خَيۡرٌ مِّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي هُوَ مَهِينٌ وَلَا يَكَادُ يُبِينُ

“Kodi ine sindine wopambana kwambiri kuposa munthu wonyozeka amene ali kukanika kuyankhula momveka?”

43:53

فَلَوۡلَآ أُلۡقِيَ عَلَيۡهِ أَسۡوِرَةٌ مِّن ذَهَبٍ أَوۡ جَآءَ مَعَهُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ مُقۡتَرِنِينَ

“Nanga ndi chifukwa chiyani iye sadavekedwe zigwinjiri za golide kapena bwanji silinadze ndi iye gulu la angelo lomuperekeza?”

43:54

فَٱسۡتَخَفَّ قَوۡمَهُۥ فَأَطَاعُوهُۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمًا فَٰسِقِينَ

Motero iye adawapusitsa anthu ake ndipo iwo amamumvera iye. Ndithudi iwo adali anthu onyoza

43:55

فَلَمَّآ ءَاسَفُونَا ٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ أَجۡمَعِينَ

Ndipo pamene iwo adatikwiyitsa, Ife tidawagwetsera chilango ndipo onse tidawamiza m’madzi

43:56

فَجَعَلۡنَٰهُمۡ سَلَفًا وَمَثَلًا لِّلۡأٓخِرِينَ

Ndipo tidawapanga iwo kukhala phunziro kwa mibadwo yam’tsogolo

43:57

وَلَمَّا ضُرِبَ ٱبۡنُ مَرۡيَمَ مَثَلًا إِذَا قَوۡمُكَ مِنۡهُ يَصِدُّونَ

Ndipo pamene mwana wamwamuna wa Maria atchulidwa ngati chitsanzo, taona! Anthu ako amaseka

43:58

وَقَالُوٓاْ ءَأَٰلِهَتُنَا خَيۡرٌ أَمۡ هُوَۚ مَا ضَرَبُوهُ لَكَ إِلَّا جَدَلَۢاۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٌ خَصِمُونَ

Ndipo iwo amati, “Kodi milungu yathu ndiyo yopambana kapena iyeyo ndiye wopambana?” Izi amangozinena kwa iwe ndi cholinga chofuna mikangano ndipo iwo ndi anthu amwano

43:59

إِنۡ هُوَ إِلَّا عَبۡدٌ أَنۡعَمۡنَا عَلَيۡهِ وَجَعَلۡنَٰهُ مَثَلًا لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ

Iye sadali wina koma kapolo wathu amene tidamulangiza chisomo chathu, ndipo tidamupanga Iye kukhala chitsanzo kwa ana a Israyeli

43:60

وَلَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَا مِنكُم مَّلَٰٓئِكَةً فِي ٱلۡأَرۡضِ يَخۡلُفُونَ

Ndipo tikadafuna tikadapanga ena a inu kukhala angelo kuti akhale padziko m’malo mwanu

43:61

وَإِنَّهُۥ لَعِلۡمٌ لِّلسَّاعَةِ فَلَا تَمۡتَرُنَّ بِهَا وَٱتَّبِعُونِۚ هَٰذَا صِرَٰطٌ مُّسۡتَقِيمٌ

Ndithudi ichi ndi chizindikiro cha ola, kotero musakayike za ilo ndipo nditsateni ine. Iyo ndiyo njira yoyenera

43:62

وَلَا يَصُدَّنَّكُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوٌّ مُّبِينٌ

Ndipo musalole kuti Satana akutchinjirizeni chifukwa, ndithudi, iye ndi mdani wanu weniweni

43:63

وَلَمَّا جَآءَ عِيسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالَ قَدۡ جِئۡتُكُم بِٱلۡحِكۡمَةِ وَلِأُبَيِّنَ لَكُم بَعۡضَ ٱلَّذِي تَخۡتَلِفُونَ فِيهِۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ

Pamene Yesu adadza ndi zizindikiro zooneka adati, “Tsopano ndadza kwa inu ndi luntha ndi cholinga chokuuzani tsatanetsatane za fundo zina zimene mumatsutsana. Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”

43:64

إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٌ مُّسۡتَقِيمٌ

“Ndithudi Mulungu! Ndiye Ambuye wanga ndi Ambuye wanu. Motero mutumikireni Iye. Imeneyi ndiyo njira yoyenera.”

43:65

فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٌ لِّلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡ عَذَابِ يَوۡمٍ أَلِيمٍ

Koma magulu ena a pakati pawo adapatukana, kotero tsoka kwa iwo amene adali oipa chifukwa cha chilango chowawa chimene chidzadza pa iwo patsiku la masautso

43:66

هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا ٱلسَّاعَةَ أَن تَأۡتِيَهُم بَغۡتَةً وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Kodi iwo ali kungodikira kuti ola lidzadza pa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sali kudziwa

43:67

ٱلۡأَخِلَّآءُ يَوۡمَئِذِۭ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوٌّ إِلَّا ٱلۡمُتَّقِينَ

Abwenzi patsiku limeneli adzasanduka adani kupatula okhawo amene amalewa zoipa

43:68

يَٰعِبَادِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡكُمُ ٱلۡيَوۡمَ وَلَآ أَنتُمۡ تَحۡزَنُونَ

oh inu akapolo anga! Palibe chochititsa mantha kwa inu lero lino ndipo simudzamva chisoni

43:69

ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ مُسۡلِمِينَ

Inu amene mwakhulupirira chivumbulutso chathu ndipo munali Asilamu

43:70

ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ أَنتُمۡ وَأَزۡوَٰجُكُمۡ تُحۡبَرُونَ

Lowani m’Paradiso, inu pamodzi ndi akazi anu ndipo mudzasangalatsidwa

43:71

يُطَافُ عَلَيۡهِم بِصِحَافٍ مِّن ذَهَبٍ وَأَكۡوَابٍۖ وَفِيهَا مَا تَشۡتَهِيهِ ٱلۡأَنفُسُ وَتَلَذُّ ٱلۡأَعۡيُنُۖ وَأَنتُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Mbale za golide ndi zikho zomwera zidzaperekedwa kwa iwo ndipo mu izo mudzakhala zimene mitima yawo inali kulakalaka ndi ponso zosangalala kuziona. Ndipo inu mudzakhala momwemo mpaka kalekale

43:72

وَتِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِيٓ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Ndipo uwu ndi munda umene mwapatsidwa kuti mukhalemo chifukwa cha zimene mudachita

43:73

لَكُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٌ كَثِيرَةٌ مِّنۡهَا تَأۡكُلُونَ

M’menemo mudzapeza zipatso zochuluka zimene muzidzadya

43:74

إِنَّ ٱلۡمُجۡرِمِينَ فِي عَذَابِ جَهَنَّمَ خَٰلِدُونَ

Ndithudi onse osakhulupirira adzakhala ku moto wa ku Gahena mpaka kalekale

43:75

لَا يُفَتَّرُ عَنۡهُمۡ وَهُمۡ فِيهِ مُبۡلِسُونَ

Chilango chawo sichidzachepetsedwa ndipo adzasowa chonena chifukwa adzakhala ndi mantha

43:76

وَمَا ظَلَمۡنَٰهُمۡ وَلَٰكِن كَانُواْ هُمُ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ife sitidawalakwire koma iwo adadzilakwitsa okha

43:77

وَنَادَوۡاْ يَٰمَٰلِكُ لِيَقۡضِ عَلَيۡنَا رَبُّكَۖ قَالَ إِنَّكُم مَّٰكِثُونَ

Ndipo iwo adzalira kuti, “Oh Maliki! Muuze Ambuye wako kuti atimalize ife! Ndipo iye adzati, “Ndithudi inu mudzakhalabe ndi moyo.”

43:78

لَقَدۡ جِئۡنَٰكُم بِٱلۡحَقِّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَكُمۡ لِلۡحَقِّ كَٰرِهُونَ

Ndithudi Ife tabweretsa choonadi kwa iwe koma ambiri a inu mumadana ndi choonadi

43:79

أَمۡ أَبۡرَمُوٓاْ أَمۡرًا فَإِنَّا مُبۡرِمُونَ

Kapene iwo ali ndi chikonzekero china? Motero nafenso tili kukonzeka

43:80

أَمۡ يَحۡسَبُونَ أَنَّا لَا نَسۡمَعُ سِرَّهُمۡ وَنَجۡوَىٰهُمۚ بَلَىٰ وَرُسُلُنَا لَدَيۡهِمۡ يَكۡتُبُونَ

Kapena iwo amaganiza kuti Ife sitikumva zimene amabisa ndi nkhani zawo za chinsinsi? Ndithudi Ife timamva ndipo Atumwi athu amene ali pakati pawo amalemba chilichonse

43:81

قُلۡ إِن كَانَ لِلرَّحۡمَٰنِ وَلَدٌ فَأَنَا۠ أَوَّلُ ٱلۡعَٰبِدِينَ

Nena, “Ngati Mwini Chisoni Chosatha akadakhala ndi Mwana, ine ndikadakhala woyamba kumupembedza.”

43:82

سُبۡحَٰنَ رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ رَبِّ ٱلۡعَرۡشِ عَمَّا يَصِفُونَ

“Ulemerero ukhale kwa Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, Ambuye Mwini mpando wachifumu! Iye akhale pamwamba pa zimene amukundukira Iye.”

43:83

فَذَرۡهُمۡ يَخُوضُواْ وَيَلۡعَبُواْ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ

Kotero aleke kuti ayambe kuyankhula zinthu zopanda pake ndi kusewera mpaka pamene akumana ndi tsiku limene amaopsedwa nalo

43:84

وَهُوَ ٱلَّذِي فِي ٱلسَّمَآءِ إِلَٰهٌ وَفِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَٰهٌۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡعَلِيمُ

Iye ndiye Mulungu wakumwamba ndi Mulungu wa padziko lapansi ndipo Iye ndi waluntha ndi wodziwa chinthu china chilichonse

43:85

وَتَبَارَكَ ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَعِندَهُۥ عِلۡمُ ٱلسَّاعَةِ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ

Ndipo wodala ndi Mwini Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo. Iye ndiye amene amadziwa ola lachiweruzo ndipo kwa Iye ndi kumene nonse mudzabwerera

43:86

وَلَا يَمۡلِكُ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِهِ ٱلشَّفَٰعَةَ إِلَّا مَن شَهِدَ بِٱلۡحَقِّ وَهُمۡ يَعۡلَمُونَ

Ndipo onse amene amawapembedza oonjezera pa Mulungu alibe mphamvu yowaimirira kupatula yekhayo amene amachitira umboni woona ndiye amene iwo amamudziwa

43:87

وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَهُمۡ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ

Ndipo ngati iwe utawafunsa kuti kodi adawalenga ndani? Ndithudi iwo adzayankha kuti, “Mulungu.” Nanga ndi chifukwa chiyani amasiya choonadi

43:88

وَقِيلِهِۦ يَٰرَبِّ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ قَوۡمٌ لَّا يُؤۡمِنُونَ

Ndi zonena zake kuti, “Ambuye wanga! Ndithudi awa ndi anthu amene safuna kukhulupirira.”

43:89

فَٱصۡفَحۡ عَنۡهُمۡ وَقُلۡ سَلَٰمٌۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ

Kotero asiye okha ndipo nena, “Mtendere!” Koma iwo adzadziwa posachedwapa

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.