Surah 78 · 40 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Surah An-Naba in Chichewa
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡمُعۡصِرَٰتِ مَآءً ثَجَّاجًا
Ndipo tidatumiza mvula yambiri kuchokera ku mitambo ya mvula
يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَتَأۡتُونَ أَفۡوَاجًا
Tsiku limene lipenga lidzalira ndipo inu mudzadza mu magulumagulu
وَفُتِحَتِ ٱلسَّمَآءُ فَكَانَتۡ أَبۡوَٰبًا
Ndipomumlengalengamudzatsegulidwa ndipo mudzakhala ngati makomo
وَسُيِّرَتِ ٱلۡجِبَالُ فَكَانَتۡ سَرَابًا
Ndipo mapiri onse adzayendetsedwa ndi kukhala ngati nthunzi yamadzi
لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرۡدًا وَلَا شَرَابًا
Kumeneko sadzalawa chozizira kapena kumwa china chilichonse
إِنَّهُمۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ حِسَابًا
Chifukwa, ndithudi, iwo sanali kuopa chidzudzulo chathu
فَذُوقُواْ فَلَن نَّزِيدَكُمۡ إِلَّا عَذَابًا
Motero inu lawani! Inu simudzalandira china chilichonse koma manzunzo ochuluka
لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا وَلَا كِذَّٰبًا
Kumeneko iwo sadzamva mawu opanda pake kapena nkhani zabodza
جَزَآءً مِّن رَّبِّكَ عَطَآءً حِسَابًا
Imeneyi ndiyo mphotho yochokera kwa Ambuye wako ndipo ndi mphotho yokwanira
رَّبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلرَّحۡمَٰنِۖ لَا يَمۡلِكُونَ مِنۡهُ خِطَابًا
Ambuye wa Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, Mwini chisoni chosatha ndipo iwo sadzatha kulankhula naye
يَوۡمَ يَقُومُ ٱلرُّوحُ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ صَفًّاۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَقَالَ صَوَابًا
Patsiku limene Mzimu ndi angelo adzaima pa mizere ndipo palibe amene adzalankhula kupatula yekhayo amene adzalandira chilolezo cha Mwini chifundo chosatha ndipo adzanena chinthu chimene chili choona
ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ مَـَٔابًا
Ndithudi tsiku limeneli ndi loona, motero iye amene afuna, mulekeni atsatire njira yobwerera kwa Ambuye wake
إِنَّآ أَنذَرۡنَٰكُمۡ عَذَابًا قَرِيبًا يَوۡمَ يَنظُرُ ٱلۡمَرۡءُ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُ وَيَقُولُ ٱلۡكَافِرُ يَٰلَيۡتَنِي كُنتُ تُرَٰبَۢا
Ndithudi takuchenjezani za chilango chowawa chimene chili nkudza posachedwa. Tsiku limene munthu adzayang’ana ntchito zimene manja ake adatsogoza, ndipo osakhulupirira adzati: “Kalanga ine, ndikanakhala dothi.”
Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.