Surah 56 · 96 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Waqi'ah in Chichewa

In English with tafsir

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

56:1

إِذَا وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ

Pamene ola la chiweruzo lidza

56:2

لَيۡسَ لِوَقۡعَتِهَا كَاذِبَةٌ

Ndipo palibe mzimu umene udzakana kudza kwake

56:3

خَافِضَةٌ رَّافِعَةٌ

Kutsitsa gulu lina ndikukweza gulu linzake

56:4

إِذَا رُجَّتِ ٱلۡأَرۡضُ رَجًّا

Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chigwedezo choopsya

56:5

وَبُسَّتِ ٱلۡجِبَالُ بَسًّا

Ndi pamene mapiri adzafumbutuka kukhala fumbi lokhalokha

56:6

فَكَانَتۡ هَبَآءً مُّنۢبَثًّا

Motero iwo adzakhala fumbi louluzika paliponse

56:7

وَكُنتُمۡ أَزۡوَٰجًا ثَلَٰثَةً

Ndipo inu mudzagawidwa m’magulu atatu

56:8

فَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ

Iwo a ku dzanja la manja. Kodi a ku dzanja la manja adzakhala ndani

56:9

وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ

Iwo akudzanja la mazere. Kodi akudzanja la mazere adzakhala ndani

56:10

وَٱلسَّٰبِقُونَ ٱلسَّٰبِقُونَ

Ndipo gulu la iwo amene adzakhala kutsogolo m’chikhulupiriro adzakhala kutsogolo m’moyo umene uli nkudza

56:11

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡمُقَرَّبُونَ

Awa ndiwo amene adzakhala kufupi ndi Mulungu

56:12

فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ

M’minda ya Paradiso

56:13

ثُلَّةٌ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ

Gulu lalikulu lidzachokera ku mibadwo ya kale

56:14

وَقَلِيلٌ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ

Ndi gulu lochepa lidzachokera ku mibadwo ya m’mbuyo mwake

56:15

عَلَىٰ سُرُرٍ مَّوۡضُونَةٍ

Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo yomatidwa golide ndi miyala ya mtengo wapatali

56:16

مُّتَّكِـِٔينَ عَلَيۡهَا مُتَقَٰبِلِينَ

Atakhala pa iyo ndi kumayang’anizana

56:17

يَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ وِلۡدَٰنٌ مُّخَلَّدُونَ

Iwo adzatumikiridwa ndi anyamata a muyaya

56:18

بِأَكۡوَابٍ وَأَبَارِيقَ وَكَأۡسٍ مِّن مَّعِينٍ

Ndi mabakuli, miphika ndi zikho za vinyo wabwino

56:19

لَّا يُصَدَّعُونَ عَنۡهَا وَلَا يُنزِفُونَ

Amene sadzawawitsa mitu yawo kapena kuwatopetsa

56:20

وَفَٰكِهَةٍ مِّمَّا يَتَخَيَّرُونَ

Ndi zipatso zimene adzasankhepo

56:21

وَلَحۡمِ طَيۡرٍ مِّمَّا يَشۡتَهُونَ

Ndi nyama ya nkhuku imene angafune

56:22

وَحُورٌ عِينٌ

Ndipo padzakhala anzawo okongola, a maso akulu ndi ochititsa kaso

56:23

كَأَمۡثَٰلِ ٱللُّؤۡلُوِٕ ٱلۡمَكۡنُونِ

Monga ndolo zosamalidwa bwino

56:24

جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Malipiro a ntchito zimene adachita kale

56:25

لَا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا وَلَا تَأۡثِيمًا

Palibe nkhani zopanda pake kapena zolaula zimene adzamva

56:26

إِلَّا قِيلًا سَلَٰمًا سَلَٰمًا

Kupatula mawu akuti Mtendere, Mtendere

56:27

وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ

Iwo a kudzanja lamanja, kodi akudzanja lamanja adzakhala ndani

56:28

فِي سِدۡرٍ مَّخۡضُودٍ

Iwo adzakhala pakati pa m’mithunzi ya mitengo ya Sidrah

56:29

وَطَلۡحٍ مَّنضُودٍ

Ndi m’mapata a nthochi zokhala ndi mikoko wina pamwamba pa unzake

56:30

وَظِلٍّ مَّمۡدُودٍ

M’mithunzi yotambasuka

56:31

وَمَآءٍ مَّسۡكُوبٍ

Pambali pa madzi osefukira

56:32

وَفَٰكِهَةٍ كَثِيرَةٍ

Ndi zipatso zochuluka

56:33

لَّا مَقۡطُوعَةٍ وَلَا مَمۡنُوعَةٍ

Zimene nyengo yake sikutha ndipo kuchuluka kwake kudzakhalabe

56:34

وَفُرُشٍ مَّرۡفُوعَةٍ

Ndi pa mipando yawofowofo yokwezedwa

56:35

إِنَّآ أَنشَأۡنَٰهُنَّ إِنشَآءً

Ndithudi Ife tawalenga iwo mu chilengedwe cha padera

56:36

فَجَعَلۡنَٰهُنَّ أَبۡكَارًا

Ndi kuwapanga kukhala a Namwali abwino

56:37

عُرُبًا أَتۡرَابًا

A chikondi pa anzawo olingana nawo zaka

56:38

لِّأَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ

A iwo amene adzakhala kudzanja lamanja

56:39

ثُلَّةٌ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ

Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo yoyamba, yakale

56:40

وَثُلَّةٌ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ

Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo ya pambuyo pake

56:41

وَأَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ

Gulu la anthu a kudzanja lamanzere. Kodi anthu a kudzanja la manzere adzakhala otani

56:42

فِي سَمُومٍ وَحَمِيمٍ

M’katikati mwa malawi a moto ndi m’madzi ogaduka

56:43

وَظِلٍّ مِّن يَحۡمُومٍ

Ndi m’mithunzi ya utsi wakuda

56:44

لَّا بَارِدٍ وَلَا كَرِيمٍ

Yosazizira kapena yabwino

56:45

إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَبۡلَ ذَٰلِكَ مُتۡرَفِينَ

Ndithudi iwo kale adali kukhala m’moyo wosavutika ndi opeza zinthu zambiri

56:46

وَكَانُواْ يُصِرُّونَ عَلَى ٱلۡحِنثِ ٱلۡعَظِيمِ

Ndipo adapitirira kuchita zoipa zikulu zikulu

56:47

وَكَانُواْ يَقُولُونَ أَئِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ

Ndipo iwo anali kukonda kunena kuti: “Pamene ife tafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, kodi tingadzaukitsidwenso?”

56:48

أَوَءَابَآؤُنَا ٱلۡأَوَّلُونَ

“Ndi makolo athu a nthawi ya makedzana?”

56:49

قُلۡ إِنَّ ٱلۡأَوَّلِينَ وَٱلۡأٓخِرِينَ

Nena: “Ndithudi onse oyambirira ndi otsiriza.”

56:50

لَمَجۡمُوعُونَ إِلَىٰ مِيقَٰتِ يَوۡمٍ مَّعۡلُومٍ

“Ndithudi onse adzasonkhanitsidwa pamodzi pa tsiku lokhazikitsidwa.”

56:51

ثُمَّ إِنَّكُمۡ أَيُّهَا ٱلضَّآلُّونَ ٱلۡمُكَذِّبُونَ

“Kuphatikiza inu nonse amene muchimwa ndi kukana choonadi.”

56:52

لَأٓكِلُونَ مِن شَجَرٍ مِّن زَقُّومٍ

“Ndithudi inu mudzadya zipatso za mtengo wa Zaqqoom.”

56:53

فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ

“Ndipo mudzakhutitsa mimba zanu ndi izo.”

56:54

فَشَٰرِبُونَ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡحَمِيمِ

“Ndi kumwa madzi ogaduka.”

56:55

فَشَٰرِبُونَ شُرۡبَ ٱلۡهِيمِ

“Ndi kumwa monga momwe ngamira yodwala ndi yaludzu imamwera.”

56:56

هَٰذَا نُزُلُهُمۡ يَوۡمَ ٱلدِّينِ

Kumeneko ndiko kudzakhala kusangalala kwawo patsiku lachiweruzo

56:57

نَحۡنُ خَلَقۡنَٰكُمۡ فَلَوۡلَا تُصَدِّقُونَ

Ndife amene tidakulengani inu nanga ndi chifukwa chiyani simukhulupilira

56:58

أَفَرَءَيۡتُم مَّا تُمۡنُونَ

Ndiuzeni za umuna umene mumatulutsa

56:59

ءَأَنتُمۡ تَخۡلُقُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡخَٰلِقُونَ

Kodi ndinu amene mumaulenga kapena Ife ndife timaulenga

56:60

نَحۡنُ قَدَّرۡنَا بَيۡنَكُمُ ٱلۡمَوۡتَ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ

Ife tidalamulira imfa kukhala pakati panu ndipo Ife sitingagonjetsedwe ayi

56:61

عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ أَمۡثَٰلَكُمۡ وَنُنشِئَكُمۡ فِي مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Kukusinthani inu ndi kukulengani kukhala china chake chimene inu simuchidziwa

56:62

وَلَقَدۡ عَلِمۡتُمُ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأُولَىٰ فَلَوۡلَا تَذَكَّرُونَ

Ndithudi inu mumadziwa za chilengedwe choyamba. Nanga ndi chifukwa chiyani simulabadira

56:63

أَفَرَءَيۡتُم مَّا تَحۡرُثُونَ

Kodi mudayamba mwaganiza za mbewu imene mumabzala

56:64

ءَأَنتُمۡ تَزۡرَعُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلزَّٰرِعُونَ

Kodi ndinu amene mumaimeretsa kapena ndife amene timameretsa

56:65

لَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَٰهُ حُطَٰمًا فَظَلۡتُمۡ تَفَكَّهُونَ

Ngati titafuna, Ife tikadaiphwanya m’timagawomagawo touma ndipo inu mukadayamba kudandaula

56:66

إِنَّا لَمُغۡرَمُونَ

Ndithudi ife tapatsidwa chingongole cholemera

56:67

بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ

Iyayi. Koma tamanidwa

56:68

أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلۡمَآءَ ٱلَّذِي تَشۡرَبُونَ

Kodi inu mumawaona madzi amene mumamwa

56:69

ءَأَنتُمۡ أَنزَلۡتُمُوهُ مِنَ ٱلۡمُزۡنِ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنزِلُونَ

Kodi ndinu amene mumawagwetsa kuchokera ku mitambo kapena ndife

56:70

لَوۡ نَشَآءُ جَعَلۡنَٰهُ أُجَاجًا فَلَوۡلَا تَشۡكُرُونَ

Chikadakhala chifuniro chathu tikadawapanga iwo kukhala a mchere. Nanga ndi chifukwa chiyani simuthokoza

56:71

أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلنَّارَ ٱلَّتِي تُورُونَ

Kodi inu mumaganizira za moto umene mumasonkha

56:72

ءَأَنتُمۡ أَنشَأۡتُمۡ شَجَرَتَهَآ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنشِـُٔونَ

Kodi ndinu amene mumameretsa mtengo umene umayaka moto kapena ndife amene timaumeretsa

56:73

نَحۡنُ جَعَلۡنَٰهَا تَذۡكِرَةً وَمَتَٰعًا لِّلۡمُقۡوِينَ

Ife taupanga iwo kukhala chikumbutso ndi chinthu chothandiza anthu amene ali paulendo

56:74

فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ

Kotero lemekezani dzina la Ambuye wanu Wamkulu

56:75

فَلَآ أُقۡسِمُ بِمَوَٰقِعِ ٱلنُّجُومِ

Ndipo ndilumbira pali nyenyezi zimene zili kugwa

56:76

وَإِنَّهُۥ لَقَسَمٌ لَّوۡ تَعۡلَمُونَ عَظِيمٌ

Ndithudi ili ndi lonjezo lalikulu inu mukadadziwa

56:77

إِنَّهُۥ لَقُرۡءَانٌ كَرِيمٌ

Ndithudi ndi Buku lolemekezeka la Korani

56:78

فِي كِتَٰبٍ مَّكۡنُونٍ

Limene lili m’Buku lotetezedwa

56:79

لَّا يَمَسُّهُۥٓ إِلَّا ٱلۡمُطَهَّرُونَ

Palibe amene adzalikhudza kupatula oyeretsedwa okha

56:80

تَنزِيلٌ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Chivumbulutso chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse

56:81

أَفَبِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ أَنتُم مُّدۡهِنُونَ

Kodi muli kunyozabe uthenga uwu

56:82

وَتَجۡعَلُونَ رِزۡقَكُمۡ أَنَّكُمۡ تُكَذِّبُونَ

Mmalo mothokoza chifukwa cha zinthu zimene amakupatsani inu mumamukana Iye

56:83

فَلَوۡلَآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلۡحُلۡقُومَ

Nanga ndi chifukwa chiyani inu simuthandiza pamene mzimu wa munthu amene ali kufa ufika pa khosi pake

56:84

وَأَنتُمۡ حِينَئِذٍ تَنظُرُونَ

Pamene panthawiyo, inu mumangoyang’ana

56:85

وَنَحۡنُ أَقۡرَبُ إِلَيۡهِ مِنكُمۡ وَلَٰكِن لَّا تُبۡصِرُونَ

Koma Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu koma inu simutiona

56:86

فَلَوۡلَآ إِن كُنتُمۡ غَيۡرَ مَدِينِينَ

Nanga ndi chifukwa chiyani simutero ngati inu simudzaweruzidwa patsogolo pake

56:87

تَرۡجِعُونَهَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Bwezerani mzimuwo ngati ndinu anthu a choonadi

56:88

فَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ

Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa anthu amene ali kufupi ndi Mulungu

56:89

فَرَوۡحٌ وَرَيۡحَانٌ وَجَنَّتُ نَعِيمٍ

Iye adzapeza mpumulo ndi chakudya ndi munda wa chisangalalo

56:90

وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ

Ndipo ngati iye ndi wam’gulu la anthu akudzanja la manja

56:91

فَسَلَٰمٌ لَّكَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ

Kotero kuli mtendere kwa iwo a kudzanja lamanja

56:92

وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُكَذِّبِينَ ٱلضَّآلِّينَ

Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa iwo okana choonadi ndi amene amalakwa

56:93

فَنُزُلٌ مِّنۡ حَمِيمٍ

Motero kulandiridwa kwake kudzakhala kwa madzi otentha kwambiri

56:94

وَتَصۡلِيَةُ جَحِيمٍ

Ndi kulowetsedwa ku Gahena

56:95

إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ حَقُّ ٱلۡيَقِينِ

Ndithudi ichi ndi choonadi chosakayikitsa

56:96

فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ

Motero lemekezani dzina la Ambuye wanu, Wamkulu

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.